Surah Al-Ankaboot — The Spider
Surah Al-Ankaboot (The Spider) is chapter 29 of the Quran, with 69 verses. This page presents the Arabic text with a Chichewa translation, verse by verse.
الٓمٓ
Alif. Lam Mim
Ayah 1أَحَسِبَ ٱلنَّاسُ أَن يُتۡرَكُوٓاْ أَن يَقُولُوٓاْ ءَامَنَّا وَهُمۡ لَا يُفۡتَنُونَ
Kodi anthu amaganiza kuti adzasiyidwa okha osayesedwa chifukwa anena kuti, “Ife ndife okhulupirira?”
Ayah 2وَلَقَدۡ فَتَنَّا ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡۖ فَلَيَعۡلَمَنَّ ٱللَّهُ ٱلَّذِينَ صَدَقُواْ وَلَيَعۡلَمَنَّ ٱلۡكَٰذِبِينَ
Ndipo ndithudi Ife tidawayesa anthu amene adalipo iwo asanadze. Ndithudi Mulungu adzawazindikira iwo amene ndi olungama, ndipo ndithudi, adzawazindikira iwo amene ndi abodza
Ayah 3أَمۡ حَسِبَ ٱلَّذِينَ يَعۡمَلُونَ ٱلسَّيِّـَٔاتِ أَن يَسۡبِقُونَاۚ سَآءَ مَا يَحۡكُمُونَ
Kodi kapena iwo amene amachita zoipa amaganiza kuti adzatithawa ife? Iwo amaweruza molakwa
Ayah 4مَن كَانَ يَرۡجُواْ لِقَآءَ ٱللَّهِ فَإِنَّ أَجَلَ ٱللَّهِ لَأٓتࣲۚ وَهُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡعَلِيمُ
Aliyense amene amakhulupirira kuti adzakumana ndi Mulungu nthawi imene Mulungu adakhazikitsa, ndithudi, idzabwera ndipo Iye ndi wakumva ndi wodziwa
Ayah 5وَمَن جَٰهَدَ فَإِنَّمَا يُجَٰهِدُ لِنَفۡسِهِۦٓۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَغَنِيٌّ عَنِ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Ndipo aliyense amene adzipereka kwathunthu, akudzipereka podzithandiza iye mwini. Ndithudi Mulungu ndi woima payekha ndipo Iye safuna thandizo lochokera kwa zolengedwa zake
Ayah 6وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ لَنُكَفِّرَنَّ عَنۡهُمۡ سَيِّـَٔاتِهِمۡ وَلَنَجۡزِيَنَّهُمۡ أَحۡسَنَ ٱلَّذِي كَانُواْ يَعۡمَلُونَ
Ndipo iwo amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, Ife tidzawakhululukira machimo awo ndikuwapatsa malipiro ofanana ndi ntchito zawo zabwino
Ayah 7وَوَصَّيۡنَا ٱلۡإِنسَٰنَ بِوَٰلِدَيۡهِ حُسۡنࣰ اۖ وَإِن جَٰهَدَاكَ لِتُشۡرِكَ بِي مَا لَيۡسَ لَكَ بِهِۦ عِلۡمࣱ فَلَا تُطِعۡهُمَآۚ إِلَيَّ مَرۡجِعُكُمۡ فَأُنَبِّئُكُم بِمَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ
Ndipo Ife tidamulamula munthu kuonetsa ubwino kwa makolo ake koma ngati iwo akuuza kuti uzindiphatikiza Ine ndi ena ake amene iwe siuwazindikira, usawamvere ayi. Kwa Ine ndiko mudzabwerera ndipo ndidzakuuzani zimene munali kuchita
Ayah 8وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ لَنُدۡخِلَنَّهُمۡ فِي ٱلصَّٰلِحِينَ
Ndipo iwo amene akhulupirira ndi kumachita ntchito zabwino, ndithudi, Ife tidzawaika m’gulu la anthu angwiro
Ayah 9وَمِنَ ٱلنَّاسِ مَن يَقُولُ ءَامَنَّا بِٱللَّهِ فَإِذَآ أُوذِيَ فِي ٱللَّهِ جَعَلَ فِتۡنَةَ ٱلنَّاسِ كَعَذَابِ ٱللَّهِۖ وَلَئِن جَآءَ نَصۡرࣱ مِّن رَّبِّكَ لَيَقُولُنَّ إِنَّا كُنَّا مَعَكُمۡۚ أَوَلَيۡسَ ٱللَّهُ بِأَعۡلَمَ بِمَا فِي صُدُورِ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Ndipo pakati pa anthu pali iye amene amati, “Ife timakhulupirira mwa Mulungu.” Koma akangoona mavuto chifukwa chodzipereka kwa Mulungu, amaganiza kuti kuponderezedwa kwawo ndi anthu ndi mkwiyo wochokera kwa Mulungu! Ndipo ngati thandizo lidza kwa iwe kuchokera kwa Ambuye wako, ndithudi, iwo adzati, “Ife tidali kumbali yako.” Kodi mukuganiza kuti Mulungu sadziwa zonse zimene zili m’mitima mwawo pakati pa zolengedwa zake zonse
Ayah 10وَلَيَعۡلَمَنَّ ٱللَّهُ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَلَيَعۡلَمَنَّ ٱلۡمُنَٰفِقِينَ
Ndithudi Mulungu amawadziwa anthu onse okhulupirira ndi anthu onse a chinyengo
Ayah 11وَقَالَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لِلَّذِينَ ءَامَنُواْ ٱتَّبِعُواْ سَبِيلَنَا وَلۡنَحۡمِلۡ خَطَٰيَٰكُمۡ وَمَا هُم بِحَٰمِلِينَ مِنۡ خَطَٰيَٰهُم مِّن شَيۡءٍۖ إِنَّهُمۡ لَكَٰذِبُونَ
Ndipo anthu osakhulupirira amanena kwa anthu okhulupirira kuti, “Tsatirani njira yathu ndipo ife tidzavomera chilango chifukwa cha kuchimwa kwanu. Iwo sadzavomera chilango china chilichonse m’malo mwawo. Ndithudi iwo ndi abodza
Ayah 12وَلَيَحۡمِلُنَّ أَثۡقَالَهُمۡ وَأَثۡقَالࣰ ا مَّعَ أَثۡقَالِهِمۡۖ وَلَيُسۡـَٔلُنَّ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ عَمَّا كَانُواْ يَفۡتَرُونَ
Iwo adzanyamula mtolo wawo pamodzi ndi mitolo ina ndi yawo. Ndipo patsiku lachiweruzo iwo adzafunsidwa kufotokoza mabodza awo
Ayah 13وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا نُوحًا إِلَىٰ قَوۡمِهِۦ فَلَبِثَ فِيهِمۡ أَلۡفَ سَنَةٍ إِلَّا خَمۡسِينَ عَامࣰ ا فَأَخَذَهُمُ ٱلطُّوفَانُ وَهُمۡ ظَٰلِمُونَ
Ndipo ndithudi tidamutumiza Nowa kwa anthu ake ndipo adakhala pakati pawo zaka chikwi chimodzi kuchotsapo zaka makumi asanu. Ndipo chigumula chidawapeza ali pa uchimo
Ayah 14فَأَنجَيۡنَٰهُ وَأَصۡحَٰبَ ٱلسَّفِينَةِ وَجَعَلۡنَٰهَآ ءَايَةࣰ لِّلۡعَٰلَمِينَ
Kotero tidamupulumutsa iye pamodzi ndi iwo amene adali naye m’chombo ndipo tidachipanga icho kukhala phunziro kwa anthu a mitundu yonse
Ayah 15وَإِبۡرَٰهِيمَ إِذۡ قَالَ لِقَوۡمِهِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ وَٱتَّقُوهُۖ ذَٰلِكُمۡ خَيۡرࣱ لَّكُمۡ إِن كُنتُمۡ تَعۡلَمُونَ
Ndipo Ife tidamupulumutsa Abrahamu pamene adati kwa anthu ake, “Pembedzani Mulungu ndipo muzimuopa Iye. Chimenecho chidzakhala chinthu chabwino kwa inu ngati mukadazindikira.”
Ayah 16إِنَّمَا تَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ أَوۡثَٰنࣰ ا وَتَخۡلُقُونَ إِفۡكًاۚ إِنَّ ٱلَّذِينَ تَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ لَا يَمۡلِكُونَ لَكُمۡ رِزۡقࣰ ا فَٱبۡتَغُواْ عِندَ ٱللَّهِ ٱلرِّزۡقَ وَٱعۡبُدُوهُ وَٱشۡكُرُواْ لَهُۥٓۖ إِلَيۡهِ تُرۡجَعُونَ
Chifukwa inu mumapembedza mafano oonjezera pa Mulungu ndipo inu mumapeka bodza. Zinthu zimene mumapembedza zoonjezera pa Mulungu zilibemphamvuzokupatsanizofunazanu.Koteropemphani zofuna zanu kwa Mulungu ndipo muzimuthokoza Iye. Kwa Iye ndiko kumene mudzabwerera
Ayah 17وَإِن تُكَذِّبُواْ فَقَدۡ كَذَّبَ أُمَمࣱ مِّن قَبۡلِكُمۡۖ وَمَا عَلَى ٱلرَّسُولِ إِلَّا ٱلۡبَلَٰغُ ٱلۡمُبِينُ
Ndipo ngati inu mukana uthenga dziwani kuti nawonso amene adalipo inu musanadze adachita chimodzimodzi. Ndipo udindo wa Mtumwi ndi kulalikira pagulu momveka
Ayah 18أَوَلَمۡ يَرَوۡاْ كَيۡفَ يُبۡدِئُ ٱللَّهُ ٱلۡخَلۡقَ ثُمَّ يُعِيدُهُۥٓۚ إِنَّ ذَٰلِكَ عَلَى ٱللَّهِ يَسِيرࣱ
Iwo sakuona mmene Mulungu amayambitsira chilengedwe ndiponso mmene amachibwerezanso. Ndithudi zimenezo ndi za pafupi kwa Mulungu
Ayah 19قُلۡ سِيرُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ فَٱنظُرُواْ كَيۡفَ بَدَأَ ٱلۡخَلۡقَۚ ثُمَّ ٱللَّهُ يُنشِئُ ٱلنَّشۡأَةَ ٱلۡأٓخِرَةَۚ إِنَّ ٱللَّهَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءࣲ قَدِيرࣱ
Nena, “Yendani paliponse pa dziko lapansi ndipo muone mmene Mulungu adayambitsira chilengedwe. Kotero Mulungu adzalenga chilengedwe chinanso. Mulungu ali ndi mphamvu pa chinthu china chilichonse.”
Ayah 20يُعَذِّبُ مَن يَشَآءُ وَيَرۡحَمُ مَن يَشَآءُۖ وَإِلَيۡهِ تُقۡلَبُونَ
Iye amalanga aliyense amene wamufuna ndiponso amaonetsa chifundo chake kwa aliyense amene wamufuna. Ndipo ndi kwa Iye kumene nonse mudzabwerera
Ayah 21وَمَآ أَنتُم بِمُعۡجِزِينَ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَلَا فِي ٱلسَّمَآءِۖ وَمَا لَكُم مِّن دُونِ ٱللَّهِ مِن وَلِيࣲّ وَلَا نَصِيرࣲ
Kaya ndi pa dziko lapansi kapena kumwamba, kulibe kumene inu mungathawire. Ndipo inu mulibe wina kupatula Mulungu amene angakutetezeni kapena kukuthandizani
Ayah 22وَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ وَلِقَآئِهِۦٓ أُوْلَٰٓئِكَ يَئِسُواْ مِن رَّحۡمَتِي وَأُوْلَٰٓئِكَ لَهُمۡ عَذَابٌ أَلِيمࣱ
onse amene amakana zizindikiro za Mulungu ndiponso zokumana naye m’moyo umene uli nkudza ndiwo amene amakayika za chifundo changa. Ndipo iwo adzalandira chilango chowawa kwambiri
Ayah 23فَمَا كَانَ جَوَابَ قَوۡمِهِۦٓ إِلَّآ أَن قَالُواْ ٱقۡتُلُوهُ أَوۡ حَرِّقُوهُ فَأَنجَىٰهُ ٱللَّهُ مِنَ ٱلنَّارِۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتࣲ لِّقَوۡمࣲ يُؤۡمِنُونَ
Yankho la anthu a Abrahamu lidali lamwano ndipo adati, “Mumuphe kapena mumutenthe.” Koma Mulungu adamupulumutsa iye ku moto. Ndithudi mu zimenezi muli phunziro kwa anthu okhulupirira
Ayah 24وَقَالَ إِنَّمَا ٱتَّخَذۡتُم مِّن دُونِ ٱللَّهِ أَوۡثَٰنࣰ ا مَّوَدَّةَ بَيۡنِكُمۡ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَاۖ ثُمَّ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ يَكۡفُرُ بَعۡضُكُم بِبَعۡضࣲ وَيَلۡعَنُ بَعۡضُكُم بَعۡضࣰ ا وَمَأۡوَىٰكُمُ ٱلنَّارُ وَمَا لَكُم مِّن نَّٰصِرِينَ
Ndipo iye adati, “Inu mwasankha kupembedza mafano kuonjezera pa Mulungu weniweni chifukwa chokweza mgwirizano wa pakati panu m’moyo uno. Koma pa tsiku lachiweruzo inu mudzakanana wina ndi mnzake. Ndipo malo anu akakhala ku moto ndipo inu simudzakhala ndi wina wokuthandizani.”
Ayah 25۞فَـَٔامَنَ لَهُۥ لُوطࣱۘ وَقَالَ إِنِّي مُهَاجِرٌ إِلَىٰ رَبِّيٓۖ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ
Koma Loti adamukhulupirira iye. Iye adati, “Ndidzachoka pa nyumba yanga chifukwa cha Ambuye wanga chifukwa Iye ndi wamphamvu zambiri ndi wanzeru.”
Ayah 26وَوَهَبۡنَا لَهُۥٓ إِسۡحَٰقَ وَيَعۡقُوبَ وَجَعَلۡنَا فِي ذُرِّيَّتِهِ ٱلنُّبُوَّةَ وَٱلۡكِتَٰبَ وَءَاتَيۡنَٰهُ أَجۡرَهُۥ فِي ٱلدُّنۡيَاۖ وَإِنَّهُۥ فِي ٱلۡأٓخِرَةِ لَمِنَ ٱلصَّٰلِحِينَ
Ndipo tidamupatsa Abrahamu, Isake ndiYakobo ndipo tidakhazikitsa pakati pa ana ake utumiki ndi chivumbulutso. Ndipo Ife tidamupatsa mphotho yake m’moyo uno ndipo iye adzakhala m’moyo umene uli nkudza, pagulu la anthu olungama
Ayah 27وَلُوطًا إِذۡ قَالَ لِقَوۡمِهِۦٓ إِنَّكُمۡ لَتَأۡتُونَ ٱلۡفَٰحِشَةَ مَا سَبَقَكُم بِهَا مِنۡ أَحَدࣲ مِّنَ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Ndipo tidatumiza Loti, kotero iye adati kwa anthu ake, “Inu muli kuchita zinthu zonyansa zimene sizidachitikeponso ndi mtundu wa anthu kuyambira kalekale.”
Ayah 28أَئِنَّكُمۡ لَتَأۡتُونَ ٱلرِّجَالَ وَتَقۡطَعُونَ ٱلسَّبِيلَ وَتَأۡتُونَ فِي نَادِيكُمُ ٱلۡمُنكَرَۖ فَمَا كَانَ جَوَابَ قَوۡمِهِۦٓ إِلَّآ أَن قَالُواْ ٱئۡتِنَا بِعَذَابِ ٱللَّهِ إِن كُنتَ مِنَ ٱلصَّٰدِقِينَ
“Kodi inu mumakaputa anthu a aamuna ndi kuchita chifwamba m’misewu ndiponso mumaphunzitsa zoipa ngakhale m’magulu anu?” Iwo sadayankhe china chilichonse kupatula kuti iwo adati, “Bweretsa pa ife chilango cha Mulungu ngati iwe ukunena zoona.”
Ayah 29قَالَ رَبِّ ٱنصُرۡنِي عَلَى ٱلۡقَوۡمِ ٱلۡمُفۡسِدِينَ
Iye adati, “Ambuye wanga! Thandizeni polimbana ndi anthu oipawa.”
Ayah 30وَلَمَّا جَآءَتۡ رُسُلُنَآ إِبۡرَٰهِيمَ بِٱلۡبُشۡرَىٰ قَالُوٓاْ إِنَّا مُهۡلِكُوٓاْ أَهۡلِ هَٰذِهِ ٱلۡقَرۡيَةِۖ إِنَّ أَهۡلَهَا كَانُواْ ظَٰلِمِينَ
Ndipo pamene Atumwi athu adadza kwa Abrahamu, ndi nkhani ya bwino, iwo adati, “Ndithudi ife tidzaononga anthu a mu mzinda uno chifukwa anthu ake ndi osalungama.”
Ayah 31قَالَ إِنَّ فِيهَا لُوطࣰ اۚ قَالُواْ نَحۡنُ أَعۡلَمُ بِمَن فِيهَاۖ لَنُنَجِّيَنَّهُۥ وَأَهۡلَهُۥٓ إِلَّا ٱمۡرَأَتَهُۥ كَانَتۡ مِنَ ٱلۡغَٰبِرِينَ
Iye adati, “Ndithudi mu mzindamo muli Loti.” Iwo adati, “Ife tikudziwa amene ali m’menemo. Ndithudi ife tidzamupulumutsa iye ndi omutsatira ake onse kupatula mkazi wake. Iye adzakhala m’gulu la anthu otsalira.”
Ayah 32وَلَمَّآ أَن جَآءَتۡ رُسُلُنَا لُوطࣰ ا سِيٓءَ بِهِمۡ وَضَاقَ بِهِمۡ ذَرۡعࣰ اۖ وَقَالُواْ لَا تَخَفۡ وَلَا تَحۡزَنۡ إِنَّا مُنَجُّوكَ وَأَهۡلَكَ إِلَّا ٱمۡرَأَتَكَ كَانَتۡ مِنَ ٱلۡغَٰبِرِينَ
Ndipo pamene Atumwi athu adadza kwa Loti, iye anada nkhawa pa zimene zingawachitikire iwo ndipo iye adaoneka wopanda mphamvu yowateteza iwo. Ndipo iwo adati, “Usaope kapena kuda nkhawa. Ndithudi ife tidzakupulumutsa iwe pamodzi ndi okutsatira ako kupatula mkazi wako. Iye adzakhala m’gulu la anthu otsalira.”
Ayah 33إِنَّا مُنزِلُونَ عَلَىٰٓ أَهۡلِ هَٰذِهِ ٱلۡقَرۡيَةِ رِجۡزࣰ ا مِّنَ ٱلسَّمَآءِ بِمَا كَانُواْ يَفۡسُقُونَ
Ndithudi Ife tidzatsitsa chilango kuchokera kumwamba, kuti chilange anthu a mzinda uno chifukwa cha machimo awo
Ayah 34وَلَقَد تَّرَكۡنَا مِنۡهَآ ءَايَةَۢ بَيِّنَةࣰ لِّقَوۡمࣲ يَعۡقِلُونَ
Ndithudi Ife tasiya chiphunzitso chokwanira kwa anthu ozindikira
Ayah 35وَإِلَىٰ مَدۡيَنَ أَخَاهُمۡ شُعَيۡبࣰ ا فَقَالَ يَٰقَوۡمِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ وَٱرۡجُواْ ٱلۡيَوۡمَ ٱلۡأٓخِرَ وَلَا تَعۡثَوۡاْ فِي ٱلۡأَرۡضِ مُفۡسِدِينَ
Ndipo kwa anthu a ku Midiyani tidatumiza m’bale wawo Shaibu ndipo iye adati, “oh anthu anga! Tumikirani Mulungu ndipo opani tsiku limene lili nkudza ndipo musayambitse chisokonezo m’dziko pochita zinthu zoipa.”
Ayah 36فَكَذَّبُوهُ فَأَخَذَتۡهُمُ ٱلرَّجۡفَةُ فَأَصۡبَحُواْ فِي دَارِهِمۡ جَٰثِمِينَ
Koma iwo adamukana iye, kotero chivomezi chachikulu chidadza pa iwo ndipo mitembo yawo idali lambilambi m’nyumba zawo
Ayah 37وَعَادࣰ ا وَثَمُودَاْ وَقَد تَّبَيَّنَ لَكُم مِّن مَّسَٰكِنِهِمۡۖ وَزَيَّنَ لَهُمُ ٱلشَّيۡطَٰنُ أَعۡمَٰلَهُمۡ فَصَدَّهُمۡ عَنِ ٱلسَّبِيلِ وَكَانُواْ مُسۡتَبۡصِرِينَ
Ndi Aad ndi Thamoud. Chitsimikizo chake chili m’mabanja a m’mizindayi. Satana adawapangitsa kuganiza kuti ntchito zawo zoipa zidali zabwino ndipo iye adawabweza ku njira yoyenera ngakhale kuti iwo adali anthu anzeru ndi aluntha
Ayah 38وَقَٰرُونَ وَفِرۡعَوۡنَ وَهَٰمَٰنَۖ وَلَقَدۡ جَآءَهُم مُّوسَىٰ بِٱلۡبَيِّنَٰتِ فَٱسۡتَكۡبَرُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَمَا كَانُواْ سَٰبِقِينَ
Ndipo Ife tidaononga Karuni, Farawo ndi Hamani. Ndithudi Mose adadza kwa iwo ndi chiphunzitso chabwino koma iwo anali kukhala mwamwano m’dziko ngakhale kuti iwo sakadatha kutigonjetsa Ife
Ayah 39فَكُلًّا أَخَذۡنَا بِذَنۢبِهِۦۖ فَمِنۡهُم مَّنۡ أَرۡسَلۡنَا عَلَيۡهِ حَاصِبࣰ ا وَمِنۡهُم مَّنۡ أَخَذَتۡهُ ٱلصَّيۡحَةُ وَمِنۡهُم مَّنۡ خَسَفۡنَا بِهِ ٱلۡأَرۡضَ وَمِنۡهُم مَّنۡ أَغۡرَقۡنَاۚ وَمَا كَانَ ٱللَّهُ لِيَظۡلِمَهُمۡ وَلَٰكِن كَانُوٓاْ أَنفُسَهُمۡ يَظۡلِمُونَ
Kotero tidalanga aliyense chifukwa cha machimo ake. Pakati pa iwo padali iwo amene tidawatumizira mvula yamkuntho, ndipo pakati pawo padali iwo amene adavutika ndi mphenzi, ndipo pakati pawo padalinso iwo amene adamezedwa ndi nthaka ndipo padalinso iwo amene tidawamiza ndipo Mulungu sadalakwe ayi koma iwo ndiwo amene adalakwira mizimu yawo
Ayah 40مَثَلُ ٱلَّذِينَ ٱتَّخَذُواْ مِن دُونِ ٱللَّهِ أَوۡلِيَآءَ كَمَثَلِ ٱلۡعَنكَبُوتِ ٱتَّخَذَتۡ بَيۡتࣰ اۖ وَإِنَّ أَوۡهَنَ ٱلۡبُيُوتِ لَبَيۡتُ ٱلۡعَنكَبُوتِۚ لَوۡ كَانُواْ يَعۡلَمُونَ
Fanizo la iwo amene amasankha owateteza kuonjezera pa Mulungu ndi Kangaude amene amamanga nyumba yake yaulusi. Ndipo ndithudi iwo akadayenera kudziwa kuti nyumba ya Kangaude ndi imodzi mwa nyumba zosalimba
Ayah 41إِنَّ ٱللَّهَ يَعۡلَمُ مَا يَدۡعُونَ مِن دُونِهِۦ مِن شَيۡءࣲۚ وَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ
Ndithudi Mulungu amadziwa chilichonse chimene iwo amapembedza kuonjezera pa Iye ndipo Iye ndi wamphamvu ndi wanzeru
Ayah 42وَتِلۡكَ ٱلۡأَمۡثَٰلُ نَضۡرِبُهَا لِلنَّاسِۖ وَمَا يَعۡقِلُهَآ إِلَّا ٱلۡعَٰلِمُونَ
Ndipo zitsanzozi tili kuziulula chifukwa cha anthu koma palibe amene amazizindikira koma ophunzira okha
Ayah 43خَلَقَ ٱللَّهُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ بِٱلۡحَقِّۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةࣰ لِّلۡمُؤۡمِنِينَ
Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi mwachoonadi. Ndithudi muli phunziro mu zimenezi kwa anthu okhulupirira
Ayah 44ٱتۡلُ مَآ أُوحِيَ إِلَيۡكَ مِنَ ٱلۡكِتَٰبِ وَأَقِمِ ٱلصَّلَوٰةَۖ إِنَّ ٱلصَّلَوٰةَ تَنۡهَىٰ عَنِ ٱلۡفَحۡشَآءِ وَٱلۡمُنكَرِۗ وَلَذِكۡرُ ٱللَّهِ أَكۡبَرُۗ وَٱللَّهُ يَعۡلَمُ مَا تَصۡنَعُونَ
Lakatula zimene zavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera m’Bukundipopitirizakupemphera. Ndithudimapemphero amateteza munthu ku machimo ndi zinthu zoipa. Ndithudi kukumbukira Mulungu ndi chinthu chachikulu ndipo Mulungu amadziwa zonse zimene mumachita
Ayah 45۞وَلَا تُجَٰدِلُوٓاْ أَهۡلَ ٱلۡكِتَٰبِ إِلَّا بِٱلَّتِي هِيَ أَحۡسَنُ إِلَّا ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ مِنۡهُمۡۖ وَقُولُوٓاْ ءَامَنَّا بِٱلَّذِيٓ أُنزِلَ إِلَيۡنَا وَأُنزِلَ إِلَيۡكُمۡ وَإِلَٰهُنَا وَإِلَٰهُكُمۡ وَٰحِدࣱ وَنَحۡنُ لَهُۥ مُسۡلِمُونَ
Ndipo musatsutsane ndi anthu okhulupirira za m’Buku pokhapokha kutakhala koyenera kutero, kupatula okhawo amene amachita zoipa. Nena, “Ife timakhulupirira mu izo zimene zavumbulutsidwa kwa ife ndi zimene zidavumbulutsidwa kwa inu ndipo Mulungu wathu ndi Mulungu wanu ndi mmodzi ndipo ife tadzipereka kwa Iye.”
Ayah 46وَكَذَٰلِكَ أَنزَلۡنَآ إِلَيۡكَ ٱلۡكِتَٰبَۚ فَٱلَّذِينَ ءَاتَيۡنَٰهُمُ ٱلۡكِتَٰبَ يُؤۡمِنُونَ بِهِۦۖ وَمِنۡ هَٰٓؤُلَآءِ مَن يُؤۡمِنُ بِهِۦۚ وَمَا يَجۡحَدُ بِـَٔايَٰتِنَآ إِلَّا ٱلۡكَٰفِرُونَ
Ndipokotero Ifetavumbulutsa Bukulolemekezekakwa iwe. Kotero onse amene tawapatsa Buku amakhulupirira mwa ilo ndipo palibe amene amakana chivumbulutso chathu kupatula anthu osalungama
Ayah 47وَمَا كُنتَ تَتۡلُواْ مِن قَبۡلِهِۦ مِن كِتَٰبࣲ وَلَا تَخُطُّهُۥ بِيَمِينِكَۖ إِذࣰ ا لَّٱرۡتَابَ ٱلۡمُبۡطِلُونَ
Ndipo iwe siudalakatule za m’Buku lina ili lisanadze. Ndipo iwe siudalembe Buku lina lililonse ndi manja ako. Zikadatero, ndithudi, anthu oyankhula zachabechabe akadakayika
Ayah 48بَلۡ هُوَ ءَايَٰتُۢ بَيِّنَٰتࣱ فِي صُدُورِ ٱلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡعِلۡمَۚ وَمَا يَجۡحَدُ بِـَٔايَٰتِنَآ إِلَّا ٱلظَّٰلِمُونَ
Iyayi! Izi ndi ziphunzitso zomveka zimene zili m’mitima ya iwo amene adapatsidwa nzeru ndipo palibe amene amakana chiphunzitso chathu kupatula wosalungama
Ayah 49وَقَالُواْ لَوۡلَآ أُنزِلَ عَلَيۡهِ ءَايَٰتࣱ مِّن رَّبِّهِۦۚ قُلۡ إِنَّمَا ٱلۡأٓيَٰتُ عِندَ ٱللَّهِ وَإِنَّمَآ أَنَا۠ نَذِيرࣱ مُّبِينٌ
Iwo amati, “Bwanji Ambuye wake sadamupatse zizindikiro?” Nena, ” Zizindikiro zonse zili ndi Mulungu ndipo ine ndine mchenjezi chabe.”
Ayah 50أَوَلَمۡ يَكۡفِهِمۡ أَنَّآ أَنزَلۡنَا عَلَيۡكَ ٱلۡكِتَٰبَ يُتۡلَىٰ عَلَيۡهِمۡۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَرَحۡمَةࣰ وَذِكۡرَىٰ لِقَوۡمࣲ يُؤۡمِنُونَ
Kodi sizidakwanire kuti tavumbulutsa Buku lolemekezeka kwa iwe limene lili kuwerengedwa kwa iwo? Ndithudi m’Bukuli muli chifundo ndi chikumbutso kwa anthu okhulupirira
Ayah 51قُلۡ كَفَىٰ بِٱللَّهِ بَيۡنِي وَبَيۡنَكُمۡ شَهِيدࣰ اۖ يَعۡلَمُ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۗ وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ بِٱلۡبَٰطِلِ وَكَفَرُواْ بِٱللَّهِ أُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡخَٰسِرُونَ
Nena, “Mulungu ndi mboni yokwana pakati pa ine ndi inu. Iye amadziwa chimene chili kumwamba ndi pa dziko lapansi.” Ndipo iwo amene amakhulupirira zabodza, ndiponso sakhulupirira mwa Mulungu, amenewa, ndi anthu olephera
Ayah 52وَيَسۡتَعۡجِلُونَكَ بِٱلۡعَذَابِ وَلَوۡلَآ أَجَلࣱ مُّسَمࣰّ ى لَّجَآءَهُمُ ٱلۡعَذَابُۚ وَلَيَأۡتِيَنَّهُم بَغۡتَةࣰ وَهُمۡ لَا يَشۡعُرُونَ
Iwo amakukakamiza kuti ubweretse chilango msanga. Ndipo zikadakhala kuti nthawi yake siidakhazikitsidwe kale, ndithudi, chilango chikadakhala chitadza kale pa iwo. Ndithudi icho chidzadza pa iwo mwadzidzidzi pamene iwo sali kuchiganizira
Ayah 53يَسۡتَعۡجِلُونَكَ بِٱلۡعَذَابِ وَإِنَّ جَهَنَّمَ لَمُحِيطَةُۢ بِٱلۡكَٰفِرِينَ
Iwo ali kukukakamiza kuti ubweretse chilango. Ndithudi Gahena idzadzadza ndi anthu osakhulupirira
Ayah 54يَوۡمَ يَغۡشَىٰهُمُ ٱلۡعَذَابُ مِن فَوۡقِهِمۡ وَمِن تَحۡتِ أَرۡجُلِهِمۡ وَيَقُولُ ذُوقُواْ مَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ
Patsiku limene chilango chidzadza pa iwo kuchokera kumwamba ndi padziko lapansi mawu adzati, “Lawani inu zipatso za ntchito zanu.”
Ayah 55يَٰعِبَادِيَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ إِنَّ أَرۡضِي وَٰسِعَةࣱ فَإِيَّٰيَ فَٱعۡبُدُونِ
oh inu akapolo anga amene mwakhulupirira! Ndithudi dziko langa lili ndi malo ambiri. Kotero ndipembedzeni Ine ndekha
Ayah 56كُلُّ نَفۡسࣲ ذَآئِقَةُ ٱلۡمَوۡتِۖ ثُمَّ إِلَيۡنَا تُرۡجَعُونَ
Mzimu uliwonse udzalawa imfa. Pomaliza nonse mudzabwererakwa Ife
Ayah 57وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ لَنُبَوِّئَنَّهُم مِّنَ ٱلۡجَنَّةِ غُرَفࣰ ا تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ خَٰلِدِينَ فِيهَاۚ نِعۡمَ أَجۡرُ ٱلۡعَٰمِلِينَ
Ndipoiwoameneamakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, otere tidzawapatsa malo kumwamba amene pansi pake pamayenda mitsinje kuti akhale m’menemo mpaka kale kale. Eti kukoma mphotho ya iwo amene amachita zabwino
Ayah 58ٱلَّذِينَ صَبَرُواْ وَعَلَىٰ رَبِّهِمۡ يَتَوَكَّلُونَ
Iwo amapirira ndipo amaika chikhulupiriro chawo mwa Ambuye wawo ndi Mtetezi wawo
Ayah 59وَكَأَيِّن مِّن دَآبَّةࣲ لَّا تَحۡمِلُ رِزۡقَهَا ٱللَّهُ يَرۡزُقُهَا وَإِيَّاكُمۡۚ وَهُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡعَلِيمُ
Kodi zilipo zolengedwa zingati zimene sizisunga chakudya chawo? Ndi Mulungu amene amazidyetsa izo pamodzi ndi inu nomwe. Ndipo Iye ndi wakumva ndi wodziwa
Ayah 60وَلَئِن سَأَلۡتَهُم مَّنۡ خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ وَسَخَّرَ ٱلشَّمۡسَ وَٱلۡقَمَرَ لَيَقُولُنَّ ٱللَّهُۖ فَأَنَّىٰ يُؤۡفَكُونَ
Ndithudi ngati iwe utawafunsa kuti kodi ndani amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndiponso amene adalamula dzuwa ndi mwezi kumvera malamulo ake? Ndithudi iwo adzayankha kuti ndi Mulungu. Nanga ndi chifukwa chiyani iwo amakana choonadi
Ayah 61ٱللَّهُ يَبۡسُطُ ٱلرِّزۡقَ لِمَن يَشَآءُ مِنۡ عِبَادِهِۦ وَيَقۡدِرُ لَهُۥٓۚ إِنَّ ٱللَّهَ بِكُلِّ شَيۡءٍ عَلِيمࣱ
Mulungu amapereka moolowa manja kwa aliyense amene Iye wamufuna ndipo amamana aliyense amene Iye wamufuna. Ndithudi Mulungu amadziwa chinthu china chilichonse
Ayah 62وَلَئِن سَأَلۡتَهُم مَّن نَّزَّلَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءࣰ فَأَحۡيَا بِهِ ٱلۡأَرۡضَ مِنۢ بَعۡدِ مَوۡتِهَا لَيَقُولُنَّ ٱللَّهُۚ قُلِ ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِۚ بَلۡ أَكۡثَرُهُمۡ لَا يَعۡقِلُونَ
Ngati iwe ungawafunse kuti kodi ndani amene amagwetsa mvula ndipo amapereka moyo ku nthaka imene idali ya kufa? Ndithudi iwo adzayankha kuti, “Ndi Mulungu.” Nena “Kuyamikidwa konse kukhale kwa Iye.” Iyayi, ambiri a iwo sazindikira
Ayah 63وَمَا هَٰذِهِ ٱلۡحَيَوٰةُ ٱلدُّنۡيَآ إِلَّا لَهۡوࣱ وَلَعِبࣱۚ وَإِنَّ ٱلدَّارَ ٱلۡأٓخِرَةَ لَهِيَ ٱلۡحَيَوَانُۚ لَوۡ كَانُواْ يَعۡلَمُونَ
Ndipo moyo wa padziko lapansi siuli kanthu koma masewera ndi kongotayira nthawi. Ukakhala moyo umene uli nkudza, umenewo ndiwo weniweni, iwo akadadziwa
Ayah 64فَإِذَا رَكِبُواْ فِي ٱلۡفُلۡكِ دَعَوُاْ ٱللَّهَ مُخۡلِصِينَ لَهُ ٱلدِّينَ فَلَمَّا نَجَّىٰهُمۡ إِلَى ٱلۡبَرِّ إِذَا هُمۡ يُشۡرِكُونَ
Kotero iwo akamakwera zombo amapempha kwa Mulungu modzipereka ndi modzichepetsa. Koma Iye akawafikitsa pa mtunda mwaubwino, Ah! iwo amamufanizira Iye ndi zina zake
Ayah 65لِيَكۡفُرُواْ بِمَآ ءَاتَيۡنَٰهُمۡ وَلِيَتَمَتَّعُواْۚ فَسَوۡفَ يَعۡلَمُونَ
Kotero iwo amaonetsa kusathokoza pa zimene tawapatsa kuti akhoza kusangalala; ndipo iwo adzazindikira posachedwapa
Ayah 66أَوَلَمۡ يَرَوۡاْ أَنَّا جَعَلۡنَا حَرَمًا ءَامِنࣰ ا وَيُتَخَطَّفُ ٱلنَّاسُ مِنۡ حَوۡلِهِمۡۚ أَفَبِٱلۡبَٰطِلِ يُؤۡمِنُونَ وَبِنِعۡمَةِ ٱللَّهِ يَكۡفُرُونَ
Kodi iwo saona kuti tateteza malo odalitsika pamene anthu ena ali kutengedwa mwankhanza pa malo owazungulira? Kodi iwo adzakhala ali kukhulupirirabe zabodza ndi kukana ubwino wa Mulungu
Ayah 67وَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّنِ ٱفۡتَرَىٰ عَلَى ٱللَّهِ كَذِبًا أَوۡ كَذَّبَ بِٱلۡحَقِّ لَمَّا جَآءَهُۥٓۚ أَلَيۡسَ فِي جَهَنَّمَ مَثۡوࣰ ى لِّلۡكَٰفِرِينَ
Kodi woipitsitsa ndani kuposa munthu amene amapeka bodza lokhudza Mulungu kapena amene amati choonadi ndi chabodza pamene auzidwa za icho? Kodi Gahena siidzakhala malo okhalamo anthu onse osakhulupirira
Ayah 68وَٱلَّذِينَ جَٰهَدُواْ فِينَا لَنَهۡدِيَنَّهُمۡ سُبُلَنَاۚ وَإِنَّ ٱللَّهَ لَمَعَ ٱلۡمُحۡسِنِينَ
Akakhala iwo amene amalimbikira kugwira ntchito yathu,ndithudi, Ife tidzawatsogolera ku njira zathu. Ndithudi Mulungu amakhala ndi iwo amene amachita zabwino
Ayah 69