Surah Al-Burooj — The Constellations
Surah Al-Burooj (The Constellations) is chapter 85 of the Quran, with 22 verses. This page presents the Arabic text with a Chichewa translation, verse by verse.
وَٱلسَّمَآءِ ذَاتِ ٱلۡبُرُوجِ
Pali kumwamba kumene kuli nyenyezi zikulu zikulu
Ayah 1وَٱلۡيَوۡمِ ٱلۡمَوۡعُودِ
Pali tsiku lolonjezedwa
Ayah 2وَشَاهِدࣲ وَمَشۡهُودࣲ
Pali tsiku la umboni ndi tsiku loperekedwa umboni
Ayah 3قُتِلَ أَصۡحَٰبُ ٱلۡأُخۡدُودِ
wotembereredwa anali anthu amene anakumba ngalande
Ayah 4ٱلنَّارِ ذَاتِ ٱلۡوَقُودِ
Imene munali moto woyaka
Ayah 5إِذۡ هُمۡ عَلَيۡهَا قُعُودࣱ
Pamene akhala moizungulira
Ayah 6وَهُمۡ عَلَىٰ مَا يَفۡعَلُونَ بِٱلۡمُؤۡمِنِينَ شُهُودࣱ
Ndipo iwo adachitira umboni pa zomwe amachitira anthu okhulupirira
Ayah 7وَمَا نَقَمُواْ مِنۡهُمۡ إِلَّآ أَن يُؤۡمِنُواْ بِٱللَّهِ ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡحَمِيدِ
Iwo analibe mlandu wina uliwonse ndi anthuwa kupatula kuti anali kukhulupirira mwa Mulungu mmodzi yekha, Mwini mphamvu zonse, Mwini kuyamikidwa
Ayah 8ٱلَّذِي لَهُۥ مُلۡكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ وَٱللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءࣲ شَهِيدٌ
Mwini Ufumu wakumwamba ndi dziko lapansi! Ndipo Mulungu ndi mboni pa chilichonse
Ayah 9إِنَّ ٱلَّذِينَ فَتَنُواْ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ وَٱلۡمُؤۡمِنَٰتِ ثُمَّ لَمۡ يَتُوبُواْ فَلَهُمۡ عَذَابُ جَهَنَّمَ وَلَهُمۡ عَذَابُ ٱلۡحَرِيقِ
Ndithudi onse amene adazunza amuna okhulupirira, ndi akazi okhulupilira ndipo salapa machimo awo, adzalandira chilango chowawa cha moto woyaka wa ku Gahena
Ayah 10إِنَّ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ لَهُمۡ جَنَّٰتࣱ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُۚ ذَٰلِكَ ٱلۡفَوۡزُ ٱلۡكَبِيرُ
Ndithu onse amene akhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino adzakhala m’minda imene ili ndi mitsinje ya madzi oyenda. Kumeneko ndiko kupambana kwakukulu
Ayah 11إِنَّ بَطۡشَ رَبِّكَ لَشَدِيدٌ
Ndithudi chilango cha Ambuye wako ndi chowawa
Ayah 12إِنَّهُۥ هُوَ يُبۡدِئُ وَيُعِيدُ
Ndithudi Iye ndiye amene amayambitsa chilengedwe ndipo adzachibwereza patsiku louka kwa akufa
Ayah 13وَهُوَ ٱلۡغَفُورُ ٱلۡوَدُودُ
Ndipo Iye ndi wokhululuka ndi wachikondi chodzadza
Ayah 14ذُو ٱلۡعَرۡشِ ٱلۡمَجِيدُ
Mwini wake wa Mpando wachifumu, Wolemekezeka
Ayah 15فَعَّالࣱ لِّمَا يُرِيدُ
Iye amachita chimene afuna
Ayah 16هَلۡ أَتَىٰكَ حَدِيثُ ٱلۡجُنُودِ
Kodi iwe siudamve za asirikali
Ayah 17فِرۡعَوۡنَ وَثَمُودَ
A Farao ndi a Thamoud
Ayah 18بَلِ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ فِي تَكۡذِيبࣲ
Iyayi! Koma anthu osakhulupirira amazikana
Ayah 19وَٱللَّهُ مِن وَرَآئِهِم مُّحِيطُۢ
Ndipo Mulungu amawazungulira onse
Ayah 20بَلۡ هُوَ قُرۡءَانࣱ مَّجِيدࣱ
Iyayi! Ili ndi Buku loyera la Korani
Ayah 21فِي لَوۡحࣲ مَّحۡفُوظِۭ
Lolembedwa m’Buku lotetezedwa
Ayah 22