Surah An-Naba — The Announcement

Surah An-Naba (The Announcement) is chapter 78 of the Quran, with 40 verses. This page presents the Arabic text with a Chichewa translation, verse by verse.

عَمَّ يَتَسَآءَلُونَ

Kodi akufunsana nkhani zotani

Ayah 1

عَنِ ٱلنَّبَإِ ٱلۡعَظِيمِ

Ali kufunsana za nkhani ija yaikulu

Ayah 2

ٱلَّذِي هُمۡ فِيهِ مُخۡتَلِفُونَ

Nkhani imene akusiyana maganizo pakati pawo

Ayah 3

كَلَّا سَيَعۡلَمُونَ

Iyayi, iwo adzadziwa posachedwa

Ayah 4

ثُمَّ كَلَّا سَيَعۡلَمُونَ

Iyayi, iwo adzadziwa posachedwapa

Ayah 5

أَلَمۡ نَجۡعَلِ ٱلۡأَرۡضَ مِهَٰدࣰ ا

Kodi Ife sitidapange dziko lapansi monga ngati kama

Ayah 6

وَٱلۡجِبَالَ أَوۡتَادࣰ ا

Ndi mapiri ngati zikhomo

Ayah 7

وَخَلَقۡنَٰكُمۡ أَزۡوَٰجࣰ ا

Ndipo Ife tidakulengani inu awiri awiri

Ayah 8

وَجَعَلۡنَا نَوۡمَكُمۡ سُبَاتࣰ ا

Ndipo tidapanga tulo kukhala ngati mpumulo wanu

Ayah 9

وَجَعَلۡنَا ٱلَّيۡلَ لِبَاسࣰ ا

Ndipo tidapanga usiku kukhala chophimba

Ayah 10

وَجَعَلۡنَا ٱلنَّهَارَ مَعَاشࣰ ا

Ndipo tinapanga usana kukhala kopezera zofuna zanu

Ayah 11

وَبَنَيۡنَا فَوۡقَكُمۡ سَبۡعࣰ ا شِدَادࣰ ا

Ndipo tidamanga mlengalenga miyamba isanu ndi iwiri

Ayah 12

وَجَعَلۡنَا سِرَاجࣰ ا وَهَّاجࣰ ا

Ndipo tidakhazikitsa mmenemo nyali yowala

Ayah 13

وَأَنزَلۡنَا مِنَ ٱلۡمُعۡصِرَٰتِ مَآءࣰ ثَجَّاجࣰ ا

Ndipo tidatumiza mvula yambiri kuchokera ku mitambo ya mvula

Ayah 14

لِّنُخۡرِجَ بِهِۦ حَبࣰّ ا وَنَبَاتࣰ ا

Kuti timeretse chakudya ndi mbewu

Ayah 15

وَجَنَّٰتٍ أَلۡفَافًا

Ndipo minda ya zomera zothinana

Ayah 16

إِنَّ يَوۡمَ ٱلۡفَصۡلِ كَانَ مِيقَٰتࣰ ا

Ndithudi tsiku la chiweruzo lidakhazikitsidwa kale

Ayah 17

يَوۡمَ يُنفَخُ فِي ٱلصُّورِ فَتَأۡتُونَ أَفۡوَاجࣰ ا

Tsiku limene lipenga lidzalira ndipo inu mudzadza mu magulumagulu

Ayah 18

وَفُتِحَتِ ٱلسَّمَآءُ فَكَانَتۡ أَبۡوَٰبࣰ ا

Ndipomumlengalengamudzatsegulidwa ndipo mudzakhala ngati makomo

Ayah 19

وَسُيِّرَتِ ٱلۡجِبَالُ فَكَانَتۡ سَرَابًا

Ndipo mapiri onse adzayendetsedwa ndi kukhala ngati nthunzi yamadzi

Ayah 20

إِنَّ جَهَنَّمَ كَانَتۡ مِرۡصَادࣰ ا

Ndithudi Gahena ili kuwayembekezera

Ayah 21

لِّلطَّٰغِينَ مَـَٔابࣰ ا

Mudzi wa anthu ophwanya malamulo

Ayah 22

لَّٰبِثِينَ فِيهَآ أَحۡقَابࣰ ا

Kumeneko ndiko kumene adzakhale mpaka kalekale

Ayah 23

لَّا يَذُوقُونَ فِيهَا بَرۡدࣰ ا وَلَا شَرَابًا

Kumeneko sadzalawa chozizira kapena kumwa china chilichonse

Ayah 24

إِلَّا حَمِيمࣰ ا وَغَسَّاقࣰ ا

Kupatula Al-Naba 637 madzi owira ndi mafinya

Ayah 25

جَزَآءࣰ وِفَاقًا

Mphotho yoyeneradi

Ayah 26

إِنَّهُمۡ كَانُواْ لَا يَرۡجُونَ حِسَابࣰ ا

Chifukwa, ndithudi, iwo sanali kuopa chidzudzulo chathu

Ayah 27

وَكَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا كِذَّابࣰ ا

Ndipo iwo moyerekedwa anali kukana chivumbulutso chathu

Ayah 28

وَكُلَّ شَيۡءٍ أَحۡصَيۡنَٰهُ كِتَٰبࣰ ا

Ndipo Ife tidalemba m’Buku zonse zimene anali kuchita

Ayah 29

فَذُوقُواْ فَلَن نَّزِيدَكُمۡ إِلَّا عَذَابًا

Motero inu lawani! Inu simudzalandira china chilichonse koma manzunzo ochuluka

Ayah 30

إِنَّ لِلۡمُتَّقِينَ مَفَازًا

Ndithudi kwa anthu oopa Mulungu kudzakhala kupambana

Ayah 31

حَدَآئِقَ وَأَعۡنَٰبࣰ ا

Minda ndi m’minda ya mphesa

Ayah 32

وَكَوَاعِبَ أَتۡرَابࣰ ا

Ndi a namwali akulu akulu ofanana zaka

Ayah 33

وَكَأۡسࣰ ا دِهَاقࣰ ا

Ndi chikho chodzadza

Ayah 34

لَّا يَسۡمَعُونَ فِيهَا لَغۡوࣰ ا وَلَا كِذَّٰبࣰ ا

Kumeneko iwo sadzamva mawu opanda pake kapena nkhani zabodza

Ayah 35

جَزَآءࣰ مِّن رَّبِّكَ عَطَآءً حِسَابࣰ ا

Imeneyi ndiyo mphotho yochokera kwa Ambuye wako ndipo ndi mphotho yokwanira

Ayah 36

رَّبِّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَا ٱلرَّحۡمَٰنِۖ لَا يَمۡلِكُونَ مِنۡهُ خِطَابࣰ ا

Ambuye wa Kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili pakati pawo, Mwini chisoni chosatha ndipo iwo sadzatha kulankhula naye

Ayah 37

يَوۡمَ يَقُومُ ٱلرُّوحُ وَٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ صَفࣰّ اۖ لَّا يَتَكَلَّمُونَ إِلَّا مَنۡ أَذِنَ لَهُ ٱلرَّحۡمَٰنُ وَقَالَ صَوَابࣰ ا

Patsiku limene Mzimu ndi angelo adzaima pa mizere ndipo palibe amene adzalankhula kupatula yekhayo amene adzalandira chilolezo cha Mwini chifundo chosatha ndipo adzanena chinthu chimene chili choona

Ayah 38

ذَٰلِكَ ٱلۡيَوۡمُ ٱلۡحَقُّۖ فَمَن شَآءَ ٱتَّخَذَ إِلَىٰ رَبِّهِۦ مَـَٔابًا

Ndithudi tsiku limeneli ndi loona, motero iye amene afuna, mulekeni atsatire njira yobwerera kwa Ambuye wake

Ayah 39

إِنَّآ أَنذَرۡنَٰكُمۡ عَذَابࣰ ا قَرِيبࣰ ا يَوۡمَ يَنظُرُ ٱلۡمَرۡءُ مَا قَدَّمَتۡ يَدَاهُ وَيَقُولُ ٱلۡكَافِرُ يَٰلَيۡتَنِي كُنتُ تُرَٰبَۢا

Ndithudi takuchenjezani za chilango chowawa chimene chili nkudza posachedwa. Tsiku limene munthu adzayang’ana ntchito zimene manja ake adatsogoza, ndipo osakhulupirira adzati: “Kalanga ine, ndikanakhala dothi.”

Ayah 40