Surah Al-Mutaffifin — Defrauding

Surah Al-Mutaffifin (Defrauding) is chapter 83 of the Quran, with 36 verses. This page presents the Arabic text with a Chichewa translation, verse by verse.

وَيۡلࣱ لِّلۡمُطَفِّفِينَ

Tsoka kwa iwo onse amene amagulitsa malonda awo monyenga

Ayah 1

ٱلَّذِينَ إِذَا ٱكۡتَالُواْ عَلَى ٱلنَّاسِ يَسۡتَوۡفُونَ

Iwo amene amati ena akamawayesera zinthu amafuna kuti zikwanire muyeso wake

Ayah 2

وَإِذَا كَالُوهُمۡ أَو وَّزَنُوهُمۡ يُخۡسِرُونَ

Koma pamene iwo ayesa kapena awayesera anthu ena amawanyenga

Ayah 3

أَلَا يَظُنُّ أُوْلَٰٓئِكَ أَنَّهُم مَّبۡعُوثُونَ

Kodi iwo saganiza kuti adzaukitsidwa kwa akufa

Ayah 4

لِيَوۡمٍ عَظِيمࣲ‏

Patsiku lalikulu

Ayah 5

يَوۡمَ يَقُومُ ٱلنَّاسُ لِرَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ

Tsiku limene anthu a mitundu yonse adzaima pamaso pa Ambuye wa zolengedwa zonse

Ayah 6

كَلَّآ إِنَّ كِتَٰبَ ٱلۡفُجَّارِ لَفِي سِجِّينࣲ‏

Iyayi! Ndithudi chiwerengero cha anthu onse oipa chili mu Sijjin

Ayah 7

وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا سِجِّينࣱ‏

Kodi udzadziwa bwanji Sijjin ndi chiyani

Ayah 8

كِتَٰبࣱ مَّرۡقُومࣱ‏

Ili ndi Buku lolembedwa

Ayah 9

وَيۡلࣱ يَوۡمَئِذࣲ لِّلۡمُكَذِّبِينَ

Tsoka pa tsikuli kwa anthu osakhulupirira

Ayah 10

ٱلَّذِينَ يُكَذِّبُونَ بِيَوۡمِ ٱلدِّينِ

Iwo amene amakana kuti kuli tsiku lachiweruzo

Ayah 11

وَمَا يُكَذِّبُ بِهِۦٓ إِلَّا كُلُّ مُعۡتَدٍ أَثِيمٍ

Palibe wina amene amalikana tsikuli kupatula munthu wogona m’machimo

Ayah 12

إِذَا تُتۡلَىٰ عَلَيۡهِ ءَايَٰتُنَا قَالَ أَسَٰطِيرُ ٱلۡأَوَّلِينَ

Pamene chivumbulutso chathu chinenedwa kwa iye, iye amati: “Izi ndizo nthano za anthu akale.”

Ayah 13

كَلَّاۖ بَلۡۜ رَانَ عَلَىٰ قُلُوبِهِم مَّا كَانُواْ يَكۡسِبُونَ

Iyayi! Koma m’mitima mwawo ndi mokutidwa ndi zintchito zimene amachita

Ayah 14

كَلَّآ إِنَّهُمۡ عَن رَّبِّهِمۡ يَوۡمَئِذࣲ لَّمَحۡجُوبُونَ

Iyayi! Ndithudi iwo sadzaloledwa kuona Ambuye wawo pa tsikuli

Ayah 15

ثُمَّ إِنَّهُمۡ لَصَالُواْ ٱلۡجَحِيمِ

Ndipo iwo adzalowa ndi kulawa moto ku Gahena

Ayah 16

ثُمَّ يُقَالُ هَٰذَا ٱلَّذِي كُنتُم بِهِۦ تُكَذِّبُونَ

Ndipo kudzanenedwa kwa iwo kuti: “Chimenechi ndicho chilango chija munkachinena kuti sichidzakhalako.”

Ayah 17

كَلَّآ إِنَّ كِتَٰبَ ٱلۡأَبۡرَارِ لَفِي عِلِّيِّينَ

Iyayi! Ndithudi chiwerengero cha anthu olungama chimasungidwa mu Illiyyun

Ayah 18

وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا عِلِّيُّونَ

Kodi mudzadziwa bwanji kuti Illiyin wapamwambayo ndi chiyani

Ayah 19

كِتَٰبࣱ مَّرۡقُومࣱ‏

Ndi Al Mutaffifin 645 Buku lochita kulembedwa

Ayah 20

يَشۡهَدُهُ ٱلۡمُقَرَّبُونَ

Limene limaonedwa ndi iwo okhawo amene ali kufupi ndi zofuna za Mulungu

Ayah 21

إِنَّ ٱلۡأَبۡرَارَ لَفِي نَعِيمٍ

Ndithudi anthu onse olungama adzakhala ku malo a mtendere

Ayah 22

عَلَى ٱلۡأَرَآئِكِ يَنظُرُونَ

Atakhala pa mipando ya wofowofo ndipo ali kuyang’ana uku ndi uku

Ayah 23

تَعۡرِفُ فِي وُجُوهِهِمۡ نَضۡرَةَ ٱلنَّعِيمِ

Ndipo udzaona chisangalalo pa nkhope zawo

Ayah 24

يُسۡقَوۡنَ مِن رَّحِيقࣲ مَّخۡتُومٍ

Iwo adzapatsidwa kuti amwe vinyo weniweni amene sanatsegulidwepo

Ayah 25

خِتَٰمُهُۥ مِسۡكࣱۚ وَفِي ذَٰلِكَ فَلۡيَتَنَافَسِ ٱلۡمُتَنَٰفِسُونَ

Womaliza wake adzakhala ndi fungo labwino ndipo pachifukwa cha ichi, aleke onse amene afuna kulimbikira kuti alimbike

Ayah 26

وَمِزَاجُهُۥ مِن تَسۡنِيمٍ

Wosakanizidwa ndi madzi a Tasnim

Ayah 27

عَيۡنࣰ ا يَشۡرَبُ بِهَا ٱلۡمُقَرَّبُونَ

Kasupe amene anthu odala adzakhala ali kumwa

Ayah 28

إِنَّ ٱلَّذِينَ أَجۡرَمُواْ كَانُواْ مِنَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ يَضۡحَكُونَ

Ndithudi! Anthu amene amachita zoipa, anali kuwaseka anthu amene anakhulupirira

Ayah 29

وَإِذَا مَرُّواْ بِهِمۡ يَتَغَامَزُونَ

Ndi kumacheulana iwo akamadutsa pakati pawo

Ayah 30

وَإِذَا ٱنقَلَبُوٓاْ إِلَىٰٓ أَهۡلِهِمُ ٱنقَلَبُواْ فَكِهِينَ

Ndipo iwo amati akabwerera kwa anthu awo amabwera ali kunyoza

Ayah 31

وَإِذَا رَأَوۡهُمۡ قَالُوٓاْ إِنَّ هَٰٓؤُلَآءِ لَضَآلُّونَ

Ndipo amati akawaona iwo amati: “Ndithudi awa ndiwo anthu osochera.”

Ayah 32

وَمَآ أُرۡسِلُواْ عَلَيۡهِمۡ حَٰفِظِينَ

Pamene iwo sadalamulidwe kuti akhale owayang’anira

Ayah 33

فَٱلۡيَوۡمَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ مِنَ ٱلۡكُفَّارِ يَضۡحَكُونَ

Koma pa tsikuli anthu okhulupirira adzaseka anthu osakhulupirira

Ayah 34

عَلَى ٱلۡأَرَآئِكِ يَنظُرُونَ

Ali pa mipando yawofowofo ndi kumayang’ana

Ayah 35

هَلۡ ثُوِّبَ ٱلۡكُفَّارُ مَا كَانُواْ يَفۡعَلُونَ

Kodi anthu osakhulupirira, sanalipidwe mphotho yawo molingana ndi ntchito zawo

Ayah 36