Surah Yusuf — Joseph

Surah Yusuf (Joseph) is chapter 12 of the Quran, with 111 verses. This page presents the Arabic text with a Chichewa translation, verse by verse.

الٓرۚ تِلۡكَ ءَايَٰتُ ٱلۡكِتَٰبِ ٱلۡمُبِينِ

Alif Lam Ra. Awa ndi mawu a Buku lofotokoza bwino

Ayah 1

إِنَّآ أَنزَلۡنَٰهُ قُرۡءَٰنًا عَرَبِيࣰّ ا لَّعَلَّكُمۡ تَعۡقِلُونَ

Ndithudi Ife talivumbulutsa ilo ngati Korani ya Chiarabu kuti mukhale ozindikira

Ayah 2

نَحۡنُ نَقُصُّ عَلَيۡكَ أَحۡسَنَ ٱلۡقَصَصِ بِمَآ أَوۡحَيۡنَآ إِلَيۡكَ هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانَ وَإِن كُنتَ مِن قَبۡلِهِۦ لَمِنَ ٱلۡغَٰفِلِينَ

Ife tili kukuuza iwe nkhani zabwino kudzera m’Korani ino. Ndipo isanafike iwe udali m’gulu la anthu amene samadziwa za ilo

Ayah 3

إِذۡ قَالَ يُوسُفُ لِأَبِيهِ يَٰٓأَبَتِ إِنِّي رَأَيۡتُ أَحَدَ عَشَرَ كَوۡكَبࣰ ا وَٱلشَّمۡسَ وَٱلۡقَمَرَ رَأَيۡتُهُمۡ لِي سَٰجِدِينَ

PameneYosefe adawauzaabamboakekuti,“Ohabambo anga! Ndithudi ine ndaona nyenyezi khumi ndi imodzi ndiponso dzuwa ndi mwezi zonsezi zili kundigwadira ine.”

Ayah 4

قَالَ يَٰبُنَيَّ لَا تَقۡصُصۡ رُءۡيَاكَ عَلَىٰٓ إِخۡوَتِكَ فَيَكِيدُواْ لَكَ كَيۡدًاۖ إِنَّ ٱلشَّيۡطَٰنَ لِلۡإِنسَٰنِ عَدُوࣱّ مُّبِينࣱ‏

Iye adati, “Oh Mwana wanga! Usauze wina aliyense wa abale ako za maloto ako, chifukwa mwina akhoza kukonza chiwembu choti akuononge iwe. Ndithudi! Satana, kwa munthu, ndi mdani woonekeratu.”

Ayah 5

وَكَذَٰلِكَ يَجۡتَبِيكَ رَبُّكَ وَيُعَلِّمُكَ مِن تَأۡوِيلِ ٱلۡأَحَادِيثِ وَيُتِمُّ نِعۡمَتَهُۥ عَلَيۡكَ وَعَلَىٰٓ ءَالِ يَعۡقُوبَ كَمَآ أَتَمَّهَا عَلَىٰٓ أَبَوَيۡكَ مِن قَبۡلُ إِبۡرَٰهِيمَ وَإِسۡحَٰقَۚ إِنَّ رَبَّكَ عَلِيمٌ حَكِيمࣱ‏

“Kotero Ambuye wako adzakusankha iwe ndikukuphunzitsa kutathauzira maloto ndi kukwaniritsa chisomo chake pa iwe ndiponso kwa ana a Yakobo, monga momwe adakwaniritsira kwa makolo ako Abrahamu ndi Isake kale! Ndithudi Ambuye wako ndi wodziwa zilizonse ndi Wanzeru.”

Ayah 6

۞لَّقَدۡ كَانَ فِي يُوسُفَ وَإِخۡوَتِهِۦٓ ءَايَٰتࣱ لِّلسَّآئِلِينَ

Ndithudi m’mbiri ya Yosefe ndi abale ake muli zizindikiro ndiponso phunziro kwa anthu ofuna kudziwa

Ayah 7

إِذۡ قَالُواْ لَيُوسُفُ وَأَخُوهُ أَحَبُّ إِلَىٰٓ أَبِينَا مِنَّا وَنَحۡنُ عُصۡبَةٌ إِنَّ أَبَانَا لَفِي ضَلَٰلࣲ مُّبِينٍ

Pamene iwo adati, “Yosefe pamodzi ndi m’bale wake amakondedwa kwambiri ndi abambo athu kuposa ife tonse pamene ife tili gulu lamphamvu. Ndithudi, abambo athu ali kulakwa koonekeratu.”

Ayah 8

ٱقۡتُلُواْ يُوسُفَ أَوِ ٱطۡرَحُوهُ أَرۡضࣰ ا يَخۡلُ لَكُمۡ وَجۡهُ أَبِيكُمۡ وَتَكُونُواْ مِنۢ بَعۡدِهِۦ قَوۡمࣰ ا صَٰلِحِينَ

“Mumuphe Yosefe kapena mukamutaye ku dziko lakutali kuti chikondi cha bambo anu chikhale pa inu nokha ndipo pambuyo pa izi inu mudzakhale anthu abwino.”

Ayah 9

قَالَ قَآئِلࣱ مِّنۡهُمۡ لَا تَقۡتُلُواْ يُوسُفَ وَأَلۡقُوهُ فِي غَيَٰبَتِ ٱلۡجُبِّ يَلۡتَقِطۡهُ بَعۡضُ ٱلسَّيَّارَةِ إِن كُنتُمۡ فَٰعِلِينَ

Mmodzi mwa iwo adati, “Musamuphe Yosefe ayi koma ngati mufuna kuchita china chake kamuponyeni m’chitsime chakuya chamdima kapena anthu apaulendo adzamutola iye ngati mungathe kutero.”

Ayah 10

قَالُواْ يَٰٓأَبَانَا مَا لَكَ لَا تَأۡمَ۬نَّا عَلَىٰ يُوسُفَ وَإِنَّا لَهُۥ لَنَٰصِحُونَ

Iwo adati, “Abambo athu! Kodi chifukwa chiyani inu simutikhulupirira ndi Yosefe pamene ife timamufunira iye zabwino?”

Ayah 11

أَرۡسِلۡهُ مَعَنَا غَدࣰ ا يَرۡتَعۡ وَيَلۡعَبۡ وَإِنَّا لَهُۥ لَحَٰفِظُونَ

“Mtumizeni iye pamodzi ndi ife mawa kuti akasangalale ndi kusewera ndipo, ndithudi, Ife tidzamusamalira iye.”

Ayah 12

قَالَ إِنِّي لَيَحۡزُنُنِيٓ أَن تَذۡهَبُواْ بِهِۦ وَأَخَافُ أَن يَأۡكُلَهُ ٱلذِّئۡبُ وَأَنتُمۡ عَنۡهُ غَٰفِلُونَ

Iye adati, “Ndithudi zikundidandaulitsa ine kuti mupite naye. Ine ndikuopa kuti mmbulu ukhoza kukamudya iye inu mutamuiwala iye.”

Ayah 13

قَالُواْ لَئِنۡ أَكَلَهُ ٱلذِّئۡبُ وَنَحۡنُ عُصۡبَةٌ إِنَّآ إِذࣰ ا لَّخَٰسِرُونَ

Iwo adati, “Ngati mmbulu ungamudye pamene ife tili gulu lamphamvu, ndiye kuti tidzakhala olephera.”

Ayah 14

فَلَمَّا ذَهَبُواْ بِهِۦ وَأَجۡمَعُوٓاْ أَن يَجۡعَلُوهُ فِي غَيَٰبَتِ ٱلۡجُبِّۚ وَأَوۡحَيۡنَآ إِلَيۡهِ لَتُنَبِّئَنَّهُم بِأَمۡرِهِمۡ هَٰذَا وَهُمۡ لَا يَشۡعُرُونَ

Ndipo pamene iwo adapita naye, iwo adagwirizana zomuponya m’chitsime chamdima ndipo Ife tidamuuza iye kuti, “Iwe udzawauza zonsezi nthawi ina pamene iwo sakudziwa.”

Ayah 15

وَجَآءُوٓ أَبَاهُمۡ عِشَآءࣰ يَبۡكُونَ

Ndipo iwo adabwera kwa abambo awo ali kulira nthawi ya madzulo

Ayah 16

قَالُواْ يَٰٓأَبَانَآ إِنَّا ذَهَبۡنَا نَسۡتَبِقُ وَتَرَكۡنَا يُوسُفَ عِندَ مَتَٰعِنَا فَأَكَلَهُ ٱلذِّئۡبُۖ وَمَآ أَنتَ بِمُؤۡمِنࣲ لَّنَا وَلَوۡ كُنَّا صَٰدِقِينَ

Iwo adati, “oh bambo wathu! Ife tinapita kukathamangitsana ndipo tinamusiya Yosefe pa katundu wathu ndipo mmbulu wamudya iye, koma inu simutikhulupirira ayi ngakhale kuti ife tili kunena choonadi.”

Ayah 17

وَجَآءُو عَلَىٰ قَمِيصِهِۦ بِدَمࣲ كَذِبࣲۚ قَالَ بَلۡ سَوَّلَتۡ لَكُمۡ أَنفُسُكُمۡ أَمۡرࣰ اۖ فَصَبۡرࣱ جَمِيلࣱۖ وَٱللَّهُ ٱلۡمُسۡتَعَانُ عَلَىٰ مَا تَصِفُونَ

Ndipo iwo adabweretsa malaya ake ali ndi magazi omwe sanali a Yosefe. Iye adati, “Iyayi! Inu mwapeka nokha nkhani koma kupirira ndi kwabwino. Ndi Mulungu yekha amene ayenera kupemphedwa chithandizo choteteza zimene mukunena.”

Ayah 18

وَجَآءَتۡ سَيَّارَةࣱ فَأَرۡسَلُواْ وَارِدَهُمۡ فَأَدۡلَىٰ دَلۡوَهُۥۖ قَالَ يَٰبُشۡرَىٰ هَٰذَا غُلَٰمࣱۚ وَأَسَرُّوهُ بِضَٰعَةࣰۚ وَٱللَّهُ عَلِيمُۢ بِمَا يَعۡمَلُونَ

Ndipo gulu la anthu a paulendo lidabwera ndipo lidatumiza mmodzi wa anthu otunga madzi, ndipo adaponya ndowa yake, Iye adafuula nati, “Imvani nkhani yabwino! Uyu mnyamata.” Ndipo iwo adamutenga iye namubisa iye ngati katundu wawo wa malonda. Koma Mulungu anali kudziwa zonse zimene iwo anali kuchita

Ayah 19

وَشَرَوۡهُ بِثَمَنِۭ بَخۡسࣲ دَرَٰهِمَ مَعۡدُودَةࣲ وَكَانُواْ فِيهِ مِنَ ٱلزَّٰهِدِينَ

Ndipo iwo adamugulitsa pa mtengo wotsika wa ndalama zowerengeka za siliva. Iwo sanalabadire china chilichonse cha iye

Ayah 20

وَقَالَ ٱلَّذِي ٱشۡتَرَىٰهُ مِن مِّصۡرَ لِٱمۡرَأَتِهِۦٓ أَكۡرِمِي مَثۡوَىٰهُ عَسَىٰٓ أَن يَنفَعَنَآ أَوۡ نَتَّخِذَهُۥ وَلَدࣰ اۚ وَكَذَٰلِكَ مَكَّنَّا لِيُوسُفَ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَلِنُعَلِّمَهُۥ مِن تَأۡوِيلِ ٱلۡأَحَادِيثِۚ وَٱللَّهُ غَالِبٌ عَلَىٰٓ أَمۡرِهِۦ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَ ٱلنَّاسِ لَا يَعۡلَمُونَ

Ndipo munthu wa mtundu wa Aiguputo, amene adamugula iye, adati kwa mkazi wake, “Mupatseni malo aulemu mwina angatithandize kapena tikhoza kumutenga kuti akhale mwana wathu.” Chomwecho Ife tidamukhazikitsira malo okhalaYosefe, kuti timuphunzitse kutanthauzira maloto. Ndipo Mulungu ali ndi mphamvu ndi ulamuliro pa zinthu zake, koma anthu ambiri sadziwa

Ayah 21

وَلَمَّا بَلَغَ أَشُدَّهُۥٓ ءَاتَيۡنَٰهُ حُكۡمࣰ ا وَعِلۡمࣰ اۚ وَكَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلۡمُحۡسِنِينَ

Ndipo pamene iye adakula, tidamupatsa luntha ndi nzeru. Chomwecho timalipira anthu ochita zabwino

Ayah 22

وَرَٰوَدَتۡهُ ٱلَّتِي هُوَ فِي بَيۡتِهَا عَن نَّفۡسِهِۦ وَغَلَّقَتِ ٱلۡأَبۡوَٰبَ وَقَالَتۡ هَيۡتَ لَكَۚ قَالَ مَعَاذَ ٱللَّهِۖ إِنَّهُۥ رَبِّيٓ أَحۡسَنَ مَثۡوَايَۖ إِنَّهُۥ لَا يُفۡلِحُ ٱلظَّٰلِمُونَ

Ndipo mkazi wam’nyumba imene Yosefe anali kukhala adamunyengerera kuti agone naye, ndipo adatseka zitseko ndipo adati kwa iye, “Bwera kuno iwe.” Iye adati, “Ndilikupempha chitetezo kwa Mulungu! Ndithudi iye ndi bwana wanga amene amandisamalira bwino. Ndithudi ochita zoipa sapambana ayi.”

Ayah 23

وَلَقَدۡ هَمَّتۡ بِهِۦۖ وَهَمَّ بِهَا لَوۡلَآ أَن رَّءَا بُرۡهَٰنَ رَبِّهِۦۚ كَذَٰلِكَ لِنَصۡرِفَ عَنۡهُ ٱلسُّوٓءَ وَٱلۡفَحۡشَآءَۚ إِنَّهُۥ مِنۡ عِبَادِنَا ٱلۡمُخۡلَصِينَ

Ndithudi mkazi adamufunitsitsa Yosefe ndipo nayenso akadamufuna iye pakadapanda kuti adaona umboni wochokera kwa Ambuye ake. Ife tidatero ndi cholinga chomuteteza ku chinthu chochititsa manyazi ndiponso choipa. Ndithudi iye adali mmodzi wa akapolo athu otsogozedwa

Ayah 24

وَٱسۡتَبَقَا ٱلۡبَابَ وَقَدَّتۡ قَمِيصَهُۥ مِن دُبُرࣲ وَأَلۡفَيَا سَيِّدَهَا لَدَا ٱلۡبَابِۚ قَالَتۡ مَا جَزَآءُ مَنۡ أَرَادَ بِأَهۡلِكَ سُوٓءًا إِلَّآ أَن يُسۡجَنَ أَوۡ عَذَابٌ أَلِيمࣱ‏

Ndipo onse adathamangitsana mpaka ku khomo ndipo mkazi uja adamung’ambira Yosefe malaya ake kumbuyo. Ndipo onse atafika pa khomo, adakumana ndi mwamuna wake wa mkaziyo. Mkazi adati, “Kodi ndi malipilo otani amene angaperekedwe kwa iye amene amafuna kuchita zoipa mkazi wako kupatula kumangidwa kapena chilango chowawakwambiri

Ayah 25

قَالَ هِيَ رَٰوَدَتۡنِي عَن نَّفۡسِيۚ وَشَهِدَ شَاهِدࣱ مِّنۡ أَهۡلِهَآ إِن كَانَ قَمِيصُهُۥ قُدَّ مِن قُبُلࣲ فَصَدَقَتۡ وَهُوَ مِنَ ٱلۡكَٰذِبِينَ

Yosefe adati,“Sindinekomamkaziyu ndiye amene amandifuna ine.” Ndipo munthu wina, wachibalendimkaziyo, adaikiraumboninati,“Ngatimalaya ake ang’ambika kumimba ndiye kuti mkaziyu ali kunena zoona, ndipo kuti iye ndi wabodza.”

Ayah 26

وَإِن كَانَ قَمِيصُهُۥ قُدَّ مِن دُبُرࣲ فَكَذَبَتۡ وَهُوَ مِنَ ٱلصَّٰدِقِينَ

“Koma ngati malaya ake ang’ambika kumbuyo, ndiye kuti mkaziyu wanama ndi kuti iye ali kunena zoona.”

Ayah 27

فَلَمَّا رَءَا قَمِيصَهُۥ قُدَّ مِن دُبُرࣲ قَالَ إِنَّهُۥ مِن كَيۡدِكُنَّۖ إِنَّ كَيۡدَكُنَّ عَظِيمࣱ‏

Ndipo pamene mwamuna wake adaona kuti malaya ake adang’ambika kumbuyo, iye adati, “Ichi ndi chimodzi cha ukamberembere wanu wa amayi. Ndithudi ukamberembere wanu ndi waukulu.”

Ayah 28

يُوسُفُ أَعۡرِضۡ عَنۡ هَٰذَاۚ وَٱسۡتَغۡفِرِي لِذَنۢبِكِۖ إِنَّكِ كُنتِ مِنَ ٱلۡخَاطِـِٔينَ

“oh Yosefe! Usayankhulenso china chilichonse pankhani izi. Iwe mkazi pempha chikhululukiro cha machimo ako. Ndithudi iwe ndiwe mmodzi wa olakwa zedi.”

Ayah 29

۞وَقَالَ نِسۡوَةࣱ فِي ٱلۡمَدِينَةِ ٱمۡرَأَتُ ٱلۡعَزِيزِ تُرَٰوِدُ فَتَىٰهَا عَن نَّفۡسِهِۦۖ قَدۡ شَغَفَهَا حُبًّاۖ إِنَّا لَنَرَىٰهَا فِي ضَلَٰلࣲ مُّبِينࣲ‏

Ndipo amai a mumzinda muja adati: “Mkazi wa Mfumu alikunyenga mnyamata wake. Ndithudi iye anali kumulakalaka zedi. Ndithudi ife tili kuona kuti mkaziyu wasochera kwambiri.”

Ayah 30

فَلَمَّا سَمِعَتۡ بِمَكۡرِهِنَّ أَرۡسَلَتۡ إِلَيۡهِنَّ وَأَعۡتَدَتۡ لَهُنَّ مُتَّكَـࣰٔ ا وَءَاتَتۡ كُلَّ وَٰحِدَةࣲ مِّنۡهُنَّ سِكِّينࣰ ا وَقَالَتِ ٱخۡرُجۡ عَلَيۡهِنَّۖ فَلَمَّا رَأَيۡنَهُۥٓ أَكۡبَرۡنَهُۥ وَقَطَّعۡنَ أَيۡدِيَهُنَّ وَقُلۡنَ حَٰشَ لِلَّهِ مَا هَٰذَا بَشَرًا إِنۡ هَٰذَآ إِلَّا مَلَكࣱ كَرِيمࣱ‏

Ndipo pamene iye adamva zokamba zawo, adawatumizira uthenga owaitana ndi kuwakonzera chakudya ndipo kwa aliyense, adamupatsa mpeni wodyera. Ndipo adati kwa Yosefe, “Tulukira kumene kuli iwo.” Ndipo pamene iwo adamuona iye, onse adamulemekeza ndipo adadzicheka manja awo. Ndipo iwo adati, “Mulungu ayeretsedwe! Uyu si munthu ayi koma mngelo wolemekezeka.”

Ayah 31

قَالَتۡ فَذَٰلِكُنَّ ٱلَّذِي لُمۡتُنَّنِي فِيهِۖ وَلَقَدۡ رَٰوَدتُّهُۥ عَن نَّفۡسِهِۦ فَٱسۡتَعۡصَمَۖ وَلَئِن لَّمۡ يَفۡعَلۡ مَآ ءَامُرُهُۥ لَيُسۡجَنَنَّ وَلَيَكُونࣰ ا مِّنَ ٱلصَّٰغِرِينَ

Mkazi uja adati, “Uyu ndiye mnyamata uja amene nonsenu munali kundidzudzula naye. Ndithudi ine ndidamunyenga koma iye adakanitsitsa. Tsopano ngati iye sachita zimene ndikumulamulira, ndithudi, adzaponyedwa ku ndende ndipo adzakhala mmodziwaanthuonyozedwa.”

Ayah 32

قَالَ رَبِّ ٱلسِّجۡنُ أَحَبُّ إِلَيَّ مِمَّا يَدۡعُونَنِيٓ إِلَيۡهِۖ وَإِلَّا تَصۡرِفۡ عَنِّي كَيۡدَهُنَّ أَصۡبُ إِلَيۡهِنَّ وَأَكُن مِّنَ ٱلۡجَٰهِلِينَ

Yosefe adati,“ohAmbuye wanga! Ndende ndi yabwino kwa ine kuposa zimene akundiitanira. Ngati inu simunditchinjiriza kuchiwembu chawo ine ndidzapendekera kwa iwo ndikukhala mmodzi wa anthu osadziwa.”

Ayah 33

فَٱسۡتَجَابَ لَهُۥ رَبُّهُۥ فَصَرَفَ عَنۡهُ كَيۡدَهُنَّۚ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡعَلِيمُ

Motero Ambuye wake adamva pempho lake ndipo adam’phwetsera chiwembu chawo pa iye. Ndithudi Iye amamva zonse ndipo amadziwa chilichonse

Ayah 34

ثُمَّ بَدَا لَهُم مِّنۢ بَعۡدِ مَا رَأَوُاْ ٱلۡأٓيَٰتِ لَيَسۡجُنُنَّهُۥ حَتَّىٰ حِينࣲ‏

Ndipo zidaonekera kwa iwo, atatha kuona zizindikiro, kuti iye am’mange mwakanthawi kochepa

Ayah 35

وَدَخَلَ مَعَهُ ٱلسِّجۡنَ فَتَيَانِۖ قَالَ أَحَدُهُمَآ إِنِّيٓ أَرَىٰنِيٓ أَعۡصِرُ خَمۡرࣰ اۖ وَقَالَ ٱلۡأٓخَرُ إِنِّيٓ أَرَىٰنِيٓ أَحۡمِلُ فَوۡقَ رَأۡسِي خُبۡزࣰ ا تَأۡكُلُ ٱلطَّيۡرُ مِنۡهُۖ نَبِّئۡنَا بِتَأۡوِيلِهِۦٓۖ إِنَّا نَرَىٰكَ مِنَ ٱلۡمُحۡسِنِينَ

Ndipo anyamata awiri adalowa m’ndende pamodzi ndi iye. Mmodzi wa iwo adati, “Ndithudi ine ndalota ndili kutcheza vinyo” Ndipo wina adanena kuti, “Ine ndinalota nditanyamula pamutu panga mkate umene mbalame zimadya. Tiuze matanthauzo ake. Ndithudi ife tikukuona iwe kuti uli mmodzi wa anthu wochita zabwino.”

Ayah 36

قَالَ لَا يَأۡتِيكُمَا طَعَامࣱ تُرۡزَقَانِهِۦٓ إِلَّا نَبَّأۡتُكُمَا بِتَأۡوِيلِهِۦ قَبۡلَ أَن يَأۡتِيَكُمَاۚ ذَٰلِكُمَا مِمَّا عَلَّمَنِي رَبِّيٓۚ إِنِّي تَرَكۡتُ مِلَّةَ قَوۡمࣲ لَّا يُؤۡمِنُونَ بِٱللَّهِ وَهُم بِٱلۡأٓخِرَةِ هُمۡ كَٰفِرُونَ

Yosefe adati, “Palibe chakudya chimene mumalandira, ngati chakudya chanu, chimene chidze kwa inu ine ndisanamasulire tanthauzo lake. Ichi ndicho chimene Ambuye wanga adandiphunzitsa. Ndithudi ine ndasiya chipembedzo cha anthu osakhulupirira mwa Mulungu ndiponso m’moyo umene uli nkudza.”

Ayah 37

وَٱتَّبَعۡتُ مِلَّةَ ءَابَآءِيٓ إِبۡرَٰهِيمَ وَإِسۡحَٰقَ وَيَعۡقُوبَۚ مَا كَانَ لَنَآ أَن نُّشۡرِكَ بِٱللَّهِ مِن شَيۡءࣲۚ ذَٰلِكَ مِن فَضۡلِ ٱللَّهِ عَلَيۡنَا وَعَلَى ٱلنَّاسِ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَ ٱلنَّاسِ لَا يَشۡكُرُونَ

“Ine ndidatsatira chipembedzo cha makolo anga, Abrahamu, Isake ndi Yakobo. Sikuli koyenera kwa ife kum’phatikiza Mulungu ndi chilichonse. Ichi ndi chisomo cha Mulungu kwa ife ndi kwa anthu a mitundu yonse, koma anthu ambiri sayamika ayi.”

Ayah 38

يَٰصَٰحِبَيِ ٱلسِّجۡنِ ءَأَرۡبَابࣱ مُّتَفَرِّقُونَ خَيۡرٌ أَمِ ٱللَّهُ ٱلۡوَٰحِدُ ٱلۡقَهَّارُ

“Oh inu anzanga awiri a m’mndende! Kodi milungu yosiyanasiyana ndi yabwino kapena wabwino ndi Mulungu mmodziyekhamwinimphamvuzonse?”

Ayah 39

مَا تَعۡبُدُونَ مِن دُونِهِۦٓ إِلَّآ أَسۡمَآءࣰ سَمَّيۡتُمُوهَآ أَنتُمۡ وَءَابَآؤُكُم مَّآ أَنزَلَ ٱللَّهُ بِهَا مِن سُلۡطَٰنٍۚ إِنِ ٱلۡحُكۡمُ إِلَّا لِلَّهِ أَمَرَ أَلَّا تَعۡبُدُوٓاْ إِلَّآ إِيَّاهُۚ ذَٰلِكَ ٱلدِّينُ ٱلۡقَيِّمُ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَ ٱلنَّاسِ لَا يَعۡلَمُونَ

“Palibechimene mumapembedza kuonjezera pa Iye, koma mayina chabe amene inu ndi makolo anu mudapeka, amene Mulungu sadatumize umboni wa mayinawo. Chiweruzo chili m’manja mwa Mulungu yekha. Iye adakulamulirani kuti inu musamapembedze wina koma Iye yekha. Chimenecho ndicho chipembedzo changwiro, koma anthu ambiri sazindikira.”

Ayah 40

يَٰصَٰحِبَيِ ٱلسِّجۡنِ أَمَّآ أَحَدُكُمَا فَيَسۡقِي رَبَّهُۥ خَمۡرࣰ اۖ وَأَمَّا ٱلۡأٓخَرُ فَيُصۡلَبُ فَتَأۡكُلُ ٱلطَّيۡرُ مِن رَّأۡسِهِۦۚ قُضِيَ ٱلۡأَمۡرُ ٱلَّذِي فِيهِ تَسۡتَفۡتِيَانِ

“Oh inu akaidi anzanga awiri! Mmodzi wa inu adzaperekera kwa Ambuye wake vinyo kuti amwe ndipo wina adzapachikidwa pa mtanda ndipo mbalame zizidzadya kuchokera pamutu pake. Motero lamulo laperekedwa pa zinthu zimene munali kufunsa.”

Ayah 41

وَقَالَ لِلَّذِي ظَنَّ أَنَّهُۥ نَاجࣲ مِّنۡهُمَا ٱذۡكُرۡنِي عِندَ رَبِّكَ فَأَنسَىٰهُ ٱلشَّيۡطَٰنُ ذِكۡرَ رَبِّهِۦ فَلَبِثَ فِي ٱلسِّجۡنِ بِضۡعَ سِنِينَ

Ndipo iye adati kwa mmodzi amene iye adamuganizira kuti adzapulumuka, “Ukandikumbukire ine kwa Ambuye wako.” Koma Satana adamuiwalitsa kuti anene za Yosefe kwa Mfumu. Kotero iye adakhala kundende zaka zingapo

Ayah 42

وَقَالَ ٱلۡمَلِكُ إِنِّيٓ أَرَىٰ سَبۡعَ بَقَرَٰتࣲ سِمَانࣲ يَأۡكُلُهُنَّ سَبۡعٌ عِجَافࣱ وَسَبۡعَ سُنۢبُلَٰتٍ خُضۡرࣲ وَأُخَرَ يَابِسَٰتࣲۖ يَٰٓأَيُّهَا ٱلۡمَلَأُ أَفۡتُونِي فِي رُءۡيَٰيَ إِن كُنتُمۡ لِلرُّءۡيَا تَعۡبُرُونَ

Ndipo Mfumu idati, “Ndithudi ine ndalota ndili kuona ng’ombe zisanu ndi ziwiri zonenepa, zimene zinali kudyedwa ndi ng’ombe zisanu ndi ziwiri zoonda ndiponso ngala zina zisanu ndi ziwiri zaziwisi ndi ngala zisanu ndi ziwiri zouma. Oh inu nduna zanga! Ndiuzeni tanthauzo la maloto anga, ngati inu mungathe kutanthauzira maloto.”

Ayah 43

قَالُوٓاْ أَضۡغَٰثُ أَحۡلَٰمࣲۖ وَمَا نَحۡنُ بِتَأۡوِيلِ ٱلۡأَحۡلَٰمِ بِعَٰلِمِينَ

Iwo adati, “Awa ndi maloto opanda ntchito ndipo ife sititha kutanthauzira maloto.”

Ayah 44

وَقَالَ ٱلَّذِي نَجَا مِنۡهُمَا وَٱدَّكَرَ بَعۡدَ أُمَّةٍ أَنَا۠ أُنَبِّئُكُم بِتَأۡوِيلِهِۦ فَأَرۡسِلُونِ

Ndipo munthu amene adatulutsidwa m’ndende, adakumbukira patapita nthawi yaitali ndipo adati, “Ine ndikuuzani kutanthauzira kwake koma nditumizeni kuti ndipite.”

Ayah 45

يُوسُفُ أَيُّهَا ٱلصِّدِّيقُ أَفۡتِنَا فِي سَبۡعِ بَقَرَٰتࣲ سِمَانࣲ يَأۡكُلُهُنَّ سَبۡعٌ عِجَافࣱ وَسَبۡعِ سُنۢبُلَٰتٍ خُضۡرࣲ وَأُخَرَ يَابِسَٰتࣲ لَّعَلِّيٓ أَرۡجِعُ إِلَى ٱلنَّاسِ لَعَلَّهُمۡ يَعۡلَمُونَ

“Oh Yosefe munthu wa choonadi! Tiuzeni za ng’ombe zisanu ndi ziwiri zonenepa zimene zinali kudyedwa ndi ng’ombe zisanu ndi ziwiri zoonda ndiponso za ngala zisanu ndi ziwiri zaziwisi ndi ngala zisanu ndi ziwiri zouma, kuti ndibwerere ndikawauze anthu kuti akadziwe tanthauzo lake?”

Ayah 46

قَالَ تَزۡرَعُونَ سَبۡعَ سِنِينَ دَأَبࣰ ا فَمَا حَصَدتُّمۡ فَذَرُوهُ فِي سُنۢبُلِهِۦٓ إِلَّا قَلِيلࣰ ا مِّمَّا تَأۡكُلُونَ

Yosefe adati, “Inu mudzabzala zaka zisanu ndi ziwiri monga momwe mumachitira ndipo zimene muzikolola muzizisiya mumakoko ake kupatula pang’ono zomwe muzidya.”

Ayah 47

ثُمَّ يَأۡتِي مِنۢ بَعۡدِ ذَٰلِكَ سَبۡعࣱ شِدَادࣱ يَأۡكُلۡنَ مَا قَدَّمۡتُمۡ لَهُنَّ إِلَّا قَلِيلࣰ ا مِّمَّا تُحۡصِنُونَ

“Ndipo potha izi kudzadza zaka zisanu ndi ziwiri za chilala pamene mudzadya zimene mudasunga kupatula pang’ono zimene mudzasunge.”

Ayah 48

ثُمَّ يَأۡتِي مِنۢ بَعۡدِ ذَٰلِكَ عَامࣱ فِيهِ يُغَاثُ ٱلنَّاسُ وَفِيهِ يَعۡصِرُونَ

“Ndipo pambuyo pa izi kudzabwera chaka chimene anthu adzalandira mvula yambiri, ndipo m’chaka chimenecho azidzafinya zipatso.”

Ayah 49

وَقَالَ ٱلۡمَلِكُ ٱئۡتُونِي بِهِۦۖ فَلَمَّا جَآءَهُ ٱلرَّسُولُ قَالَ ٱرۡجِعۡ إِلَىٰ رَبِّكَ فَسۡـَٔلۡهُ مَا بَالُ ٱلنِّسۡوَةِ ٱلَّٰتِي قَطَّعۡنَ أَيۡدِيَهُنَّۚ إِنَّ رَبِّي بِكَيۡدِهِنَّ عَلِيمࣱ‏

Ndipo Mfumu idati, “Mubweretseni pamaso panga.” Koma pamene Kazembe wa Mfumu anadza kwa iye, Yosefe adati, “Bwerera kwa Ambuye wako ndipo ukamufunse za amayi amene adacheka manja awo. Ndithudi Ambuye wanga adziwa za ukachenjede wawo.”

Ayah 50

قَالَ مَا خَطۡبُكُنَّ إِذۡ رَٰوَدتُّنَّ يُوسُفَ عَن نَّفۡسِهِۦۚ قُلۡنَ حَٰشَ لِلَّهِ مَا عَلِمۡنَا عَلَيۡهِ مِن سُوٓءࣲۚ قَالَتِ ٱمۡرَأَتُ ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡـَٰٔنَ حَصۡحَصَ ٱلۡحَقُّ أَنَا۠ رَٰوَدتُّهُۥ عَن نَّفۡسِهِۦ وَإِنَّهُۥ لَمِنَ ٱلصَّٰدِقِينَ

Iyo inati, “Kodi cholinga chanu chinali chotani pamene inu munali kufuna kumunyenga Yosefe?” Amai anati, “Mulungu atiletse! Ife sitidziwa choipa chilichonse chimene iye anachita.” Mkazi wa mfumu adati, “Tsopano choonadi chadziwika. Ndine amene ndimamufuna ndipo iye, ndithudi, ndi wachilungamo.”

Ayah 51

ذَٰلِكَ لِيَعۡلَمَ أَنِّي لَمۡ أَخُنۡهُ بِٱلۡغَيۡبِ وَأَنَّ ٱللَّهَ لَا يَهۡدِي كَيۡدَ ٱلۡخَآئِنِينَ

“Kuchokera mu izi bwana wanga adzadziwa kuti sindidachite chinyengo pamene iye kunalibe ndiponso kuti Mulungu satsogolera ntchito za anthu a chinyengo.”

Ayah 52

۞وَمَآ أُبَرِّئُ نَفۡسِيٓۚ إِنَّ ٱلنَّفۡسَ لَأَمَّارَةُۢ بِٱلسُّوٓءِ إِلَّا مَا رَحِمَ رَبِّيٓۚ إِنَّ رَبِّي غَفُورࣱ رَّحِيمࣱ‏

“Ine sindili kudziyeretsa, ndithudi, mtima wa munthu umakonda zoipa kupatula pamene Ambuye wanga aonetsa chisomo chake. Ndithudi Ambuye wanga amakhululukira ndiponso ndi Wachisoni chosatha.”

Ayah 53

وَقَالَ ٱلۡمَلِكُ ٱئۡتُونِي بِهِۦٓ أَسۡتَخۡلِصۡهُ لِنَفۡسِيۖ فَلَمَّا كَلَّمَهُۥ قَالَ إِنَّكَ ٱلۡيَوۡمَ لَدَيۡنَا مَكِينٌ أَمِينࣱ‏

Mfumu idati, “Mubweretseni iye kwa ine kuti ndimusankhe iye kukhala munthu wanga.” Ndipo atayankhula naye, Mfumu idati, “Ndithudi iwe udzakhala ndi ife kuyambira lero ndipo udzakhala wolemekezeka ndiponso wokhulupirika.”

Ayah 54

قَالَ ٱجۡعَلۡنِي عَلَىٰ خَزَآئِنِ ٱلۡأَرۡضِۖ إِنِّي حَفِيظٌ عَلِيمࣱ‏

Yosefe adati, “Ndiikeni pa udindo woyang’anira nkhokwe za m’dziko. Ine, ndithudi, ndidzazisunga bwino.”

Ayah 55

وَكَذَٰلِكَ مَكَّنَّا لِيُوسُفَ فِي ٱلۡأَرۡضِ يَتَبَوَّأُ مِنۡهَا حَيۡثُ يَشَآءُۚ نُصِيبُ بِرَحۡمَتِنَا مَن نَّشَآءُۖ وَلَا نُضِيعُ أَجۡرَ ٱلۡمُحۡسِنِينَ

Mmenemo ndi mmene tidamupatsira Yosefe udindo mdziko ndipo adakhala paliponse pamene amafuna. Ife timampatsa chisomo amene tamufuna ndipo sitisokoneza mphotho za anthu ochita zabwino

Ayah 56

وَلَأَجۡرُ ٱلۡأٓخِرَةِ خَيۡرࣱ لِّلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَكَانُواْ يَتَّقُونَ

Ndipo, ndithudi, mphotho ya m’moyo umene uli nkudza ndi yabwino kwa anthu okhulupirira ndi amene anali kuopa Mulungu

Ayah 57

وَجَآءَ إِخۡوَةُ يُوسُفَ فَدَخَلُواْ عَلَيۡهِ فَعَرَفَهُمۡ وَهُمۡ لَهُۥ مُنكِرُونَ

Ndipo abale ake a Yosefe adadza, nalowa kwa iye. Iye adawazindikira koma iwo sadamuzindikire iye

Ayah 58

وَلَمَّا جَهَّزَهُم بِجَهَازِهِمۡ قَالَ ٱئۡتُونِي بِأَخࣲ لَّكُم مِّنۡ أَبِيكُمۡۚ أَلَا تَرَوۡنَ أَنِّيٓ أُوفِي ٱلۡكَيۡلَ وَأَنَا۠ خَيۡرُ ٱلۡمُنزِلِينَ

Ndipo pamene iye adawakonzera chakudya chawo, iye adati, “Ndibweretsereni m’bale wanu mwa abambo anu. Kodi inu simukuona kuti ine ndikukwaniritsa muyeso ndiponso ndimalandira bwino alendo?”

Ayah 59

فَإِن لَّمۡ تَأۡتُونِي بِهِۦ فَلَا كَيۡلَ لَكُمۡ عِندِي وَلَا تَقۡرَبُونِ

“Koma ngati inu simudzabwera naye kwa ine inu simudzalandira muyeso wa chakudya kuchokera kwa ine ndiponso simudzandiyandikira.”

Ayah 60

قَالُواْ سَنُرَٰوِدُ عَنۡهُ أَبَاهُ وَإِنَّا لَفَٰعِلُونَ

Iwo adati, “Ife tikawanyengerera abambo ake kuti akamulole kuti adzabwere nafe. Ichi, ndithudi, tikachita.”

Ayah 61

وَقَالَ لِفِتۡيَٰنِهِ ٱجۡعَلُواْ بِضَٰعَتَهُمۡ فِي رِحَالِهِمۡ لَعَلَّهُمۡ يَعۡرِفُونَهَآ إِذَا ٱنقَلَبُوٓاْ إِلَىٰٓ أَهۡلِهِمۡ لَعَلَّهُمۡ يَرۡجِعُونَ

Yosefe adawauza anyamata a ntchito ake kuti aike ndalama zawo m’matumba mwawo kuti akazindikire akakafika kwa abale awo kuti mwina akabwerenso

Ayah 62

فَلَمَّا رَجَعُوٓاْ إِلَىٰٓ أَبِيهِمۡ قَالُواْ يَٰٓأَبَانَا مُنِعَ مِنَّا ٱلۡكَيۡلُ فَأَرۡسِلۡ مَعَنَآ أَخَانَا نَكۡتَلۡ وَإِنَّا لَهُۥ لَحَٰفِظُونَ

Pamene iwo adabwerera kwa abambo awo iwo adati, “oh inu abambo athu! Kwaletsedwa kwa ife kugula muyeso wachakudya. Motero mtumizeni m’bale wathu pamodzi ndi ife kuti ife tikapeze muyeso wa chakudya. Ndipo ife tikamusamala.”

Ayah 63

قَالَ هَلۡ ءَامَنُكُمۡ عَلَيۡهِ إِلَّا كَمَآ أَمِنتُكُمۡ عَلَىٰٓ أَخِيهِ مِن قَبۡلُ فَٱللَّهُ خَيۡرٌ حَٰفِظࣰ اۖ وَهُوَ أَرۡحَمُ ٱلرَّٰحِمِينَ

Yakobo adati, “Kodi ine ndikukhulupirireni pokupatsani uyu monga momwe ndidakukhulupirirani kale ndi m’bale wake uja? Komatu Mulungu ndiye Msungi wabwino ndipo Iye ndiye wachifundo mwa achifundo onse.”

Ayah 64

وَلَمَّا فَتَحُواْ مَتَٰعَهُمۡ وَجَدُواْ بِضَٰعَتَهُمۡ رُدَّتۡ إِلَيۡهِمۡۖ قَالُواْ يَٰٓأَبَانَا مَا نَبۡغِيۖ هَٰذِهِۦ بِضَٰعَتُنَا رُدَّتۡ إِلَيۡنَاۖ وَنَمِيرُ أَهۡلَنَا وَنَحۡفَظُ أَخَانَا وَنَزۡدَادُ كَيۡلَ بَعِيرࣲۖ ذَٰلِكَ كَيۡلࣱ يَسِيرࣱ‏

Ndipo pamene iwo adatsekula katundu wawo, adapeza kuti ndalama zawo zabwezedwa kwa iwo. Iwo adati, “oh Atate athu! Kodi ndi chiyani chimene tingafunenso? Nazi ndalama zathu zabwezedwa kwa ife motero tidzapeza chakudya chambiri cha mabanja athu. Ndiponso tidzamusamala m’bale wathu ndi kuonjezera muyeso wokwana kunyamulidwa ndi ngamira imodzi. Umenewu ndiwo muyeso wochepa.”

Ayah 65

قَالَ لَنۡ أُرۡسِلَهُۥ مَعَكُمۡ حَتَّىٰ تُؤۡتُونِ مَوۡثِقࣰ ا مِّنَ ٱللَّهِ لَتَأۡتُنَّنِي بِهِۦٓ إِلَّآ أَن يُحَاطَ بِكُمۡۖ فَلَمَّآ ءَاتَوۡهُ مَوۡثِقَهُمۡ قَالَ ٱللَّهُ عَلَىٰ مَا نَقُولُ وَكِيلࣱ‏

Iye adati, “Ine sindidzamutumiza iye pamodzi ndi inu pokhapokha ngati mutandipatsalonjezoM’dzinalaMulungu,kutimudzabwera naye kwa ine kupatula ngati mutagonjetsedwa.” Ndipo pamene iwo adapereka lonjezo lawo, iye adanena kuti, “Pa zonse zimene tikunena, Mulungu akhale mboni.”

Ayah 66

وَقَالَ يَٰبَنِيَّ لَا تَدۡخُلُواْ مِنۢ بَابࣲ وَٰحِدࣲ وَٱدۡخُلُواْ مِنۡ أَبۡوَٰبࣲ مُّتَفَرِّقَةࣲۖ وَمَآ أُغۡنِي عَنكُم مِّنَ ٱللَّهِ مِن شَيۡءٍۖ إِنِ ٱلۡحُكۡمُ إِلَّا لِلَّهِۖ عَلَيۡهِ تَوَكَّلۡتُۖ وَعَلَيۡهِ فَلۡيَتَوَكَّلِ ٱلۡمُتَوَكِّلُونَ

Ndipo iye adati, “E inu ana anga! Musakalowere khomo limodzi koma kaloweni m’makomo osiyanasiyana ndipo ine sindingakuthandizeni chilichonse polimbana ndi Mulungu. Zoonadi chiweruzo ndi cha Mulungu yekha. Mwa Iye yekha ine ndimaika chikhulupiriro changa ndipo onse amene amakhulupirira aike chikhulupiriro chawo mwa Iye.”

Ayah 67

وَلَمَّا دَخَلُواْ مِنۡ حَيۡثُ أَمَرَهُمۡ أَبُوهُم مَّا كَانَ يُغۡنِي عَنۡهُم مِّنَ ٱللَّهِ مِن شَيۡءٍ إِلَّا حَاجَةࣰ فِي نَفۡسِ يَعۡقُوبَ قَضَىٰهَاۚ وَإِنَّهُۥ لَذُو عِلۡمࣲ لِّمَا عَلَّمۡنَٰهُ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَ ٱلنَّاسِ لَا يَعۡلَمُونَ

Pamene iwo adalowa, monga momwe atate awo adawalangizira, sizidawathandize chilichonse kwa Mulungu. Ichi sichinali china chilichonse koma kungokwaniritsa chifuniro chimene Yakobo adali nacho. Ndithudi iye adali ndi nzeru chifukwa Ife tidamuphunzitsa, koma anthu ambiri sadziwa

Ayah 68

وَلَمَّا دَخَلُواْ عَلَىٰ يُوسُفَ ءَاوَىٰٓ إِلَيۡهِ أَخَاهُۖ قَالَ إِنِّيٓ أَنَا۠ أَخُوكَ فَلَا تَبۡتَئِسۡ بِمَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ

NdipopameneiwoadalowakwaYosefe,iyeadamutenga m’bale wake pambali nati, “Ndithudi ine ndine m’bale wako ndipo usadandaule ndi zimene iwo adali kuchita.”

Ayah 69

فَلَمَّا جَهَّزَهُم بِجَهَازِهِمۡ جَعَلَ ٱلسِّقَايَةَ فِي رَحۡلِ أَخِيهِ ثُمَّ أَذَّنَ مُؤَذِّنٌ أَيَّتُهَا ٱلۡعِيرُ إِنَّكُمۡ لَسَٰرِقُونَ

Ndipo pamene iye adawakonzera chakudya chawo,iye adaika mbale m’nthumba, la m’bale wake. Ndipo woitana adafuula kwa iwo nati, “oh inu apaulendo! Ndithudi inu ndinu akuba!”

Ayah 70

قَالُواْ وَأَقۡبَلُواْ عَلَيۡهِم مَّاذَا تَفۡقِدُونَ

Iwo adatembenuka nati, “Kodi mwasowa chiyani?”

Ayah 71

قَالُواْ نَفۡقِدُ صُوَاعَ ٱلۡمَلِكِ وَلِمَن جَآءَ بِهِۦ حِمۡلُ بَعِيرࣲ وَأَنَا۠ بِهِۦ زَعِيمࣱ‏

Iwo adati, “Tikusowa mbale ya Mfumu ndipo aliyense amene abweretse mbale adzalandira katundu wokwana kunyamula ndi ngamira imodzi. Ndipo ine ndine mboni.”

Ayah 72

قَالُواْ تَٱللَّهِ لَقَدۡ عَلِمۡتُم مَّا جِئۡنَا لِنُفۡسِدَ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَمَا كُنَّا سَٰرِقِينَ

Iwo adanena kuti, “Pali Mulungu! Ndithudi inu muli kudziwa kuti ife sitinadze kudzaononga m’dziko lanu ndipo sindife mbala ayi!”

Ayah 73

قَالُواْ فَمَا جَزَٰٓؤُهُۥٓ إِن كُنتُمۡ كَٰذِبِينَ

Iwo adati, “Kodi chilango chake ndi chotani, ngati inu mukunena zabodza?”

Ayah 74

قَالُواْ جَزَٰٓؤُهُۥ مَن وُجِدَ فِي رَحۡلِهِۦ فَهُوَ جَزَٰٓؤُهُۥۚ كَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلظَّٰلِمِينَ

Iwo adati: “Aliyense amene m’thumba mwake mupezeke mbale, iyeyo ndiye adzalandira chilango cha mbaleyo. Kotero ndimo mmene ife timalangira athu ochita zoipa.”

Ayah 75

فَبَدَأَ بِأَوۡعِيَتِهِمۡ قَبۡلَ وِعَآءِ أَخِيهِ ثُمَّ ٱسۡتَخۡرَجَهَا مِن وِعَآءِ أَخِيهِۚ كَذَٰلِكَ كِدۡنَا لِيُوسُفَۖ مَا كَانَ لِيَأۡخُذَ أَخَاهُ فِي دِينِ ٱلۡمَلِكِ إِلَّآ أَن يَشَآءَ ٱللَّهُۚ نَرۡفَعُ دَرَجَٰتࣲ مَّن نَّشَآءُۗ وَفَوۡقَ كُلِّ ذِي عِلۡمٍ عَلِيمࣱ‏

Ndipo iye adayamba kusanthula matumba awo asadasanthule thumba la mng’ono wake. Ndipo pomaliza iye adaitulutsa mbale ija m’thumba la mng’ono wakeyo. Mmenemo ndimo tidamphunzitsira nzeru Yosefe chifukwa ndi ulamulo wa m’dziko limenelo sakadatha kusunga m’bale wake pokhapokha ngati Mulungu akadafuna kuti zichitike motero. Ife timakweza paudindo amene tamufuna; koma pamwamba pa iwo amene ali ndi nzeru, alipo ena amene ndi odziwa kwambiri

Ayah 76

۞قَالُوٓاْ إِن يَسۡرِقۡ فَقَدۡ سَرَقَ أَخࣱ لَّهُۥ مِن قَبۡلُۚ فَأَسَرَّهَا يُوسُفُ فِي نَفۡسِهِۦ وَلَمۡ يُبۡدِهَا لَهُمۡۚ قَالَ أَنتُمۡ شَرࣱّ مَّكَانࣰ اۖ وَٱللَّهُ أَعۡلَمُ بِمَا تَصِفُونَ

Iwo adati, “Ngati iye waba, ndiye kuti panali m’bale wake wina amene adabanso kale.” Koma Yosefe adasunga chinsinsi ndipo sadawauze iwo ayi. Iye adaganiza kuti “Inu muli pa mlandu. Mulungu ali kudziwa bwino zonse zimene mukunena.”

Ayah 77

قَالُواْ يَٰٓأَيُّهَا ٱلۡعَزِيزُ إِنَّ لَهُۥٓ أَبࣰ ا شَيۡخࣰ ا كَبِيرࣰ ا فَخُذۡ أَحَدَنَا مَكَانَهُۥٓۖ إِنَّا نَرَىٰكَ مِنَ ٱلۡمُحۡسِنِينَ

Iwo adati, “oh inu Mfumu! Ndithudi iye ali ndi abambo ake wokalamba kwambiri. Motero tengani mmodzi wa ife m’malo mwake. Ndithudi ife tili kukuonani kuti inu ndinu mmodzi wa anthu ochita zabwino.”

Ayah 78

قَالَ مَعَاذَ ٱللَّهِ أَن نَّأۡخُذَ إِلَّا مَن وَجَدۡنَا مَتَٰعَنَا عِندَهُۥٓ إِنَّآ إِذࣰ ا لَّظَٰلِمُونَ

Iye adati, “Mulungu ateteze kuti ife titenge wina wake m’malo mwa munthu amene tam’peza ndi katundu wathu. Ndithudi titatero tikhala opanda chilungamo.”

Ayah 79

فَلَمَّا ٱسۡتَيۡـَٔسُواْ مِنۡهُ خَلَصُواْ نَجِيࣰّ اۖ قَالَ كَبِيرُهُمۡ أَلَمۡ تَعۡلَمُوٓاْ أَنَّ أَبَاكُمۡ قَدۡ أَخَذَ عَلَيۡكُم مَّوۡثِقࣰ ا مِّنَ ٱللَّهِ وَمِن قَبۡلُ مَا فَرَّطتُمۡ فِي يُوسُفَۖ فَلَنۡ أَبۡرَحَ ٱلۡأَرۡضَ حَتَّىٰ يَأۡذَنَ لِيٓ أَبِيٓ أَوۡ يَحۡكُمَ ٱللَّهُ لِيۖ وَهُوَ خَيۡرُ ٱلۡحَٰكِمِينَ

Motero pamene iwo anada nkhawa ndi iye, iwo adakhala paokha ndikunong’onezana. Ndipo wamkulu wawo adati, “Kodi inu simudziwa kuti abambo anu adatenga lonjezo kwa inu, M’dzina la Mulungu ndiponso kuti mudaphwanya chikhulupiriro chanu kale ndi nkhani ya Yosefe? Motero ine sindidzachoka m’dziko muno mpaka pamene abambo anga andilola kapena kufikira pamene Mulungu atapereka chiweruzo chake pa nkhani iyi. Iye ndiye Muweruzi wabwino pa aweruzi onse.”

Ayah 80

ٱرۡجِعُوٓاْ إِلَىٰٓ أَبِيكُمۡ فَقُولُواْ يَٰٓأَبَانَآ إِنَّ ٱبۡنَكَ سَرَقَ وَمَا شَهِدۡنَآ إِلَّا بِمَا عَلِمۡنَا وَمَا كُنَّا لِلۡغَيۡبِ حَٰفِظِينَ

“Bwererani kwa atate wanu ndipo mukawauze kuti, “Oh Bambo wathu! Ndithudi mwana wanu waba ndipo ife sitiikira umboni kupatula pa zimene tikudziwa. Ndipo ife sitikadadziwa zinthu zobisika!”

Ayah 81

وَسۡـَٔلِ ٱلۡقَرۡيَةَ ٱلَّتِي كُنَّا فِيهَا وَٱلۡعِيرَ ٱلَّتِيٓ أَقۡبَلۡنَا فِيهَاۖ وَإِنَّا لَصَٰدِقُونَ

“Ndipo funsani anthu a mumzinda umene tidali ndiponso apaulendo amene tafika nawo, ndipo ndithudi ife tili kunena zoonadi.”

Ayah 82

قَالَ بَلۡ سَوَّلَتۡ لَكُمۡ أَنفُسُكُمۡ أَمۡرࣰ اۖ فَصَبۡرࣱ جَمِيلٌۖ عَسَى ٱللَّهُ أَن يَأۡتِيَنِي بِهِمۡ جَمِيعًاۚ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلۡعَلِيمُ ٱلۡحَكِيمُ

Yakobo adati, “Iyayi! Mizimu yanu yakunyengani kuchita zoipa. Koma kupirira ndi kwabwino. Mwina Mulungu adzawabweretsa onse awiri kwa ine. Ndithudi Iye yekha amadziwa zinthu zonse ndiponso ndi waluntha.”

Ayah 83

وَتَوَلَّىٰ عَنۡهُمۡ وَقَالَ يَٰٓأَسَفَىٰ عَلَىٰ يُوسُفَ وَٱبۡيَضَّتۡ عَيۡنَاهُ مِنَ ٱلۡحُزۡنِ فَهُوَ كَظِيمࣱ‏

Ndipo iye adayang’ana kumbali nati, “Kalanga! Ine ndili ndi chisoni ndi Yosefe!” Maso ake adachita khungu chifukwachachisonichachikuluchimenechinalimumtima mwake

Ayah 84

قَالُواْ تَٱللَّهِ تَفۡتَؤُاْ تَذۡكُرُ يُوسُفَ حَتَّىٰ تَكُونَ حَرَضًا أَوۡ تَكُونَ مِنَ ٱلۡهَٰلِكِينَ

Ana ake adati, “Pali Mulungu! Inu simudzasiya kumukumbukira Yosefe mpaka mufoka ndi ukalamba kapena mufa.”

Ayah 85

قَالَ إِنَّمَآ أَشۡكُواْ بَثِّي وَحُزۡنِيٓ إِلَى ٱللَّهِ وَأَعۡلَمُ مِنَ ٱللَّهِ مَا لَا تَعۡلَمُونَ

Iye adati, “Ine ndili kudandaula kwa Mulungu za chisoni changa ndipo ndilikudziwa kuchokera kwa Mulungu zimene inu simukuzidziwa.”

Ayah 86

يَٰبَنِيَّ ٱذۡهَبُواْ فَتَحَسَّسُواْ مِن يُوسُفَ وَأَخِيهِ وَلَا تَاْيۡـَٔسُواْ مِن رَّوۡحِ ٱللَّهِۖ إِنَّهُۥ لَا يَاْيۡـَٔسُ مِن رَّوۡحِ ٱللَّهِ إِلَّا ٱلۡقَوۡمُ ٱلۡكَٰفِرُونَ

“oh ana anga!, Pitani mukafufuze za Yosefe pamodzi ndi m’bale wake, ndipo musataye mtima ndi chisomo cha Mulungu. Ndithudi palibe amene amataya mtima ndi chisomo cha Mulungu kupatula anthu osakhulupirira.”

Ayah 87

فَلَمَّا دَخَلُواْ عَلَيۡهِ قَالُواْ يَٰٓأَيُّهَا ٱلۡعَزِيزُ مَسَّنَا وَأَهۡلَنَا ٱلضُّرُّ وَجِئۡنَا بِبِضَٰعَةࣲ مُّزۡجَىٰةࣲ فَأَوۡفِ لَنَا ٱلۡكَيۡلَ وَتَصَدَّقۡ عَلَيۡنَآۖ إِنَّ ٱللَّهَ يَجۡزِي ٱلۡمُتَصَدِّقِينَ

Ndipo pamene iwo adalowa kwa Yosefe, iwo adati, “Oh inu Mfumu yolemekezeka! Ife pamodzi ndi anthu athu tapeza mavuto, ndipo ife tabweretsa ndalama zochepa motero tiyesereni chakudya chokwanira ndipo tipatseni china chaulere. Ndithudi Mulungu amalipira anthu ochita zabwino.”

Ayah 88

قَالَ هَلۡ عَلِمۡتُم مَّا فَعَلۡتُم بِيُوسُفَ وَأَخِيهِ إِذۡ أَنتُمۡ جَٰهِلُونَ

Iye adati, “Kodi inu muli kudziwa zimene mudamuchitira Yosefe ndi m’bale wake pamene inu simumadziwa?”

Ayah 89

قَالُوٓاْ أَءِنَّكَ لَأَنتَ يُوسُفُۖ قَالَ أَنَا۠ يُوسُفُ وَهَٰذَآ أَخِيۖ قَدۡ مَنَّ ٱللَّهُ عَلَيۡنَآۖ إِنَّهُۥ مَن يَتَّقِ وَيَصۡبِرۡ فَإِنَّ ٱللَّهَ لَا يُضِيعُ أَجۡرَ ٱلۡمُحۡسِنِينَ

Iwo adati, “Kodi iwe ndiwedi Yosefe?” Iye adati, “Ine ndine Yosefe ndipo uyu ndi m’bale wanga. Mulungu, ndithudi, watikomera mtima ife. Ndithudi iye amene amaopa Mulungu ndi kupirira molimba ndithudi Mulungu sasokoneza malipiro a anthu ochita zabwino.”

Ayah 90

قَالُواْ تَٱللَّهِ لَقَدۡ ءَاثَرَكَ ٱللَّهُ عَلَيۡنَا وَإِن كُنَّا لَخَٰطِـِٔينَ

Iwo adati, “Pali Mulungu, ndithudi, Mulungu wakulemekezani inu kuposa ife ndipo, ndithudi, ife tidali olakwa.”

Ayah 91

قَالَ لَا تَثۡرِيبَ عَلَيۡكُمُ ٱلۡيَوۡمَۖ يَغۡفِرُ ٱللَّهُ لَكُمۡۖ وَهُوَ أَرۡحَمُ ٱلرَّٰحِمِينَ

Iye adati, “Palibe chidzudzulo kwa inu tsiku lalero ndipo Mulungu akukhululukireni inu. Iye ndiye wokhululukira mwa okhululukira onse.”

Ayah 92

ٱذۡهَبُواْ بِقَمِيصِي هَٰذَا فَأَلۡقُوهُ عَلَىٰ وَجۡهِ أَبِي يَأۡتِ بَصِيرࣰ ا وَأۡتُونِي بِأَهۡلِكُمۡ أَجۡمَعِينَ

“Pitani ndi malaya angawa ndipo mukawaponye pamaso pa abambo anga ndipo maso awo adzayambanso kuona. Ndipo mukabwere, ndi abale anu onse kwa ine.”

Ayah 93

وَلَمَّا فَصَلَتِ ٱلۡعِيرُ قَالَ أَبُوهُمۡ إِنِّي لَأَجِدُ رِيحَ يُوسُفَۖ لَوۡلَآ أَن تُفَنِّدُونِ

Ndipo pamene gulu la a paulendo lidanyamuka, atate awo adati, “Ndikumva fungo la Yosefe ngati inu muganiza kuti nzeru zanga zatha.”

Ayah 94

قَالُواْ تَٱللَّهِ إِنَّكَ لَفِي ضَلَٰلِكَ ٱلۡقَدِيمِ

Iwo adati, “Pali Mulungu! Iwe ndiwe wosokonekera kuyambira kale.”

Ayah 95

فَلَمَّآ أَن جَآءَ ٱلۡبَشِيرُ أَلۡقَىٰهُ عَلَىٰ وَجۡهِهِۦ فَٱرۡتَدَّ بَصِيرࣰ اۖ قَالَ أَلَمۡ أَقُل لَّكُمۡ إِنِّيٓ أَعۡلَمُ مِنَ ٱللَّهِ مَا لَا تَعۡلَمُونَ

Ndipo pamene mthenga wa nkhani zabwino adadza iye adaponya malaya a Yosefe pamaso pake, ndipo nthawi yomweyo adayambanso kupenya. Iye adati, “Kodi ine sindidakuuzeni kuti ine ndinali kudziwa, kuchokera kwa Mulungu, zinthu zimene inu simuzidziwa?”

Ayah 96

قَالُواْ يَٰٓأَبَانَا ٱسۡتَغۡفِرۡ لَنَا ذُنُوبَنَآ إِنَّا كُنَّا خَٰطِـِٔينَ

Iwo adati, “oh abambo athu! Tipempherenichikhululukirochamachimoathu, ndithudi, ife tidali ochimwa.”

Ayah 97

قَالَ سَوۡفَ أَسۡتَغۡفِرُ لَكُمۡ رَبِّيٓۖ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلۡغَفُورُ ٱلرَّحِيمُ

Iye adati, “Ine ndidzakupempherani chikhululukiro kwa Ambuye wanga. Ndithudi Iye ndi wokhululukira ndiponso ndi Wachisoni chosatha.”

Ayah 98

فَلَمَّا دَخَلُواْ عَلَىٰ يُوسُفَ ءَاوَىٰٓ إِلَيۡهِ أَبَوَيۡهِ وَقَالَ ٱدۡخُلُواْ مِصۡرَ إِن شَآءَ ٱللَّهُ ءَامِنِينَ

Ndipo pamene iwo adalowa kwa Yosefe iye adatenga makolo ake pa yekha nati, “Lowani mu dziko la Aiguputo, ngati Mulungu afuna, mwamtendere.”

Ayah 99

وَرَفَعَ أَبَوَيۡهِ عَلَى ٱلۡعَرۡشِ وَخَرُّواْ لَهُۥ سُجَّدࣰ اۖ وَقَالَ يَٰٓأَبَتِ هَٰذَا تَأۡوِيلُ رُءۡيَٰيَ مِن قَبۡلُ قَدۡ جَعَلَهَا رَبِّي حَقࣰّ اۖ وَقَدۡ أَحۡسَنَ بِيٓ إِذۡ أَخۡرَجَنِي مِنَ ٱلسِّجۡنِ وَجَآءَ بِكُم مِّنَ ٱلۡبَدۡوِ مِنۢ بَعۡدِ أَن نَّزَغَ ٱلشَّيۡطَٰنُ بَيۡنِي وَبَيۡنَ إِخۡوَتِيٓۚ إِنَّ رَبِّي لَطِيفࣱ لِّمَا يَشَآءُۚ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلۡعَلِيمُ ٱلۡحَكِيمُ

Ndipo iye adanyamula makolo ake ndikuwakhazika pa mpando wolemekezeka ndipo onse adagwa pansi kulemekeza iye. Ndipo iye adati, “Oh bambo wanga! Ili ndi tanthauzo la maloto anga aja akale. Ndithudi Ambuye wanga adawapanga kukhala oona. Iye adandichitira ine ubwino pamene adanditulutsa kundende ndipo adakubweretsani inu kuchokera ku midzi pambuyo pakuti satana adakhazikitsa udani pakati pa ine ndi abale anga. Ndithudi Ambuye wanga ndi waulemu ndi wachisoni kwa amene Iye wamufuna. Ndithudi! Iye yekha ndi wodziwa zonse ndi wanzeru.”

Ayah 100

۞رَبِّ قَدۡ ءَاتَيۡتَنِي مِنَ ٱلۡمُلۡكِ وَعَلَّمۡتَنِي مِن تَأۡوِيلِ ٱلۡأَحَادِيثِۚ فَاطِرَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ أَنتَ وَلِيِّۦ فِي ٱلدُّنۡيَا وَٱلۡأٓخِرَةِۖ تَوَفَّنِي مُسۡلِمࣰ ا وَأَلۡحِقۡنِي بِٱلصَّٰلِحِينَ

“Ambuye, Inu ndithudi, mwandipatsa ine ulemerero ndi kundiphunzitsa kutanthauzira maloto. Inu ndinu Namalenga wakumwamba ndi dziko lapansi. Inu ndinu Msungi wanga m’dziko lino ndiponso m’dziko limene lili nkudza. Ndilekeni kuti ndife ndili kukulambirani inu ndipo ndiikeni m’gulu la anthu abwino.”

Ayah 101

ذَٰلِكَ مِنۡ أَنۢبَآءِ ٱلۡغَيۡبِ نُوحِيهِ إِلَيۡكَۖ وَمَا كُنتَ لَدَيۡهِمۡ إِذۡ أَجۡمَعُوٓاْ أَمۡرَهُمۡ وَهُمۡ يَمۡكُرُونَ

Chimene tavumbulutsa kwa iwe ndi mbiri yakale yachinsinsi. Iwe kudalibe pamene abale ake a Yosefe onse adakonza chiwembu

Ayah 102

وَمَآ أَكۡثَرُ ٱلنَّاسِ وَلَوۡ حَرَصۡتَ بِمُؤۡمِنِينَ

Ndipo anthu ambiri sadzakhulupirira ngakhale ungalimbikire motani

Ayah 103

وَمَا تَسۡـَٔلُهُمۡ عَلَيۡهِ مِنۡ أَجۡرٍۚ إِنۡ هُوَ إِلَّا ذِكۡرࣱ لِّلۡعَٰلَمِينَ

Iwe siuwafunsamalipirochifukwachaichi. Ichindichizindikiro ndi chikumbutso kwa anthu a mitundu yonse

Ayah 104

وَكَأَيِّن مِّنۡ ءَايَةࣲ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ يَمُرُّونَ عَلَيۡهَا وَهُمۡ عَنۡهَا مُعۡرِضُونَ

Kodi ndi zizindikiro zingati za mu mlengalenga ndi za m’dziko lapansi zimene iwo amangozipyola osalabadira china chilichonse

Ayah 105

وَمَا يُؤۡمِنُ أَكۡثَرُهُم بِٱللَّهِ إِلَّا وَهُم مُّشۡرِكُونَ

Ndipo ambiri a iwo sakhulupirira mwa Mulungu kupatula kupembedza milungu ina yoonjezera pa Mulungu weniweni

Ayah 106

أَفَأَمِنُوٓاْ أَن تَأۡتِيَهُمۡ غَٰشِيَةࣱ مِّنۡ عَذَابِ ٱللَّهِ أَوۡ تَأۡتِيَهُمُ ٱلسَّاعَةُ بَغۡتَةࣰ وَهُمۡ لَا يَشۡعُرُونَ

Kodi iwo amaganiza kuti ndi otetezedwa ku chilango cha Mulungu kuti chilango chake sichidzadza pa iwo mwadzidzidzi opanda kuzindikira

Ayah 107

قُلۡ هَٰذِهِۦ سَبِيلِيٓ أَدۡعُوٓاْ إِلَى ٱللَّهِۚ عَلَىٰ بَصِيرَةٍ أَنَا۠ وَمَنِ ٱتَّبَعَنِيۖ وَسُبۡحَٰنَ ٱللَّهِ وَمَآ أَنَا۠ مِنَ ٱلۡمُشۡرِكِينَ

Nena, “Iyi ndi njira yanga. Ine mosakayika, ndili kukuitanani ndi nzeru kuti mukhale ndi chikhulupiriro mwa Mulungu, ine pamodzi ndi onditsatira anga. Ulemerero ukhale kwa Mulungu ndipo ine sindine wopembedza mafano ayi.”

Ayah 108

وَمَآ أَرۡسَلۡنَا مِن قَبۡلِكَ إِلَّا رِجَالࣰ ا نُّوحِيٓ إِلَيۡهِم مِّنۡ أَهۡلِ ٱلۡقُرَىٰٓۗ أَفَلَمۡ يَسِيرُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ فَيَنظُرُواْ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡۗ وَلَدَارُ ٱلۡأٓخِرَةِ خَيۡرࣱ لِّلَّذِينَ ٱتَّقَوۡاْۚ أَفَلَا تَعۡقِلُونَ

Ndipo Ife sitinatumizepo iwe usanadze, wina kupatula anthu amene tinawatsogolera kuchokera pakati pa anthu a m’mizinda. Kodi iwo sanayende padziko ndi kuona zimene zidawachitikira amene adalipo kale? Ndipo, ndithudi, moyo umene uli nkudza ndi wabwino kwa anthu amene amaopa Mulungu ndipo amamumvera Iye. Kodi mulibe nzeru

Ayah 109

حَتَّىٰٓ إِذَا ٱسۡتَيۡـَٔسَ ٱلرُّسُلُ وَظَنُّوٓاْ أَنَّهُمۡ قَدۡ كُذِبُواْ جَآءَهُمۡ نَصۡرُنَا فَنُجِّيَ مَن نَّشَآءُۖ وَلَا يُرَدُّ بَأۡسُنَا عَنِ ٱلۡقَوۡمِ ٱلۡمُجۡرِمِينَ

Mpaka pamene Atumwi athu adataya mtima ndipo anali kuganiza kuti kulibe wina aliyense amene akadawakhulupirira iwo, thandizo lathu lidadza pa iwo ndi kupulumutsa aliyense amene Ife tidamufuna. Ndipo chilango chathu sichingabweretsedwe m’mbuyo kwa anthu ochita zoipa

Ayah 110

لَقَدۡ كَانَ فِي قَصَصِهِمۡ عِبۡرَةࣱ لِّأُوْلِي ٱلۡأَلۡبَٰبِۗ مَا كَانَ حَدِيثࣰ ا يُفۡتَرَىٰ وَلَٰكِن تَصۡدِيقَ ٱلَّذِي بَيۡنَ يَدَيۡهِ وَتَفۡصِيلَ كُلِّ شَيۡءࣲ وَهُدࣰ ى وَرَحۡمَةࣰ لِّقَوۡمࣲ يُؤۡمِنُونَ

Ndithudi m’mbiri yawo muli phunziro kwa anthu ozindikira. Iyi si nkhani yopeka ayi koma ndi chitsimikiziro cha ma buku a Mulungu amene adaperekedwa kale, ndipo ndi mfotokozi wa zinthu zonse ndi chilangizo ndiponso madalitso kwa anthu okhulupirira

Ayah 111