Surah Ash-Shams — The Sun
Surah Ash-Shams (The Sun) is chapter 91 of the Quran, with 15 verses. This page presents the Arabic text with a Chichewa translation, verse by verse.
وَٱلشَّمۡسِ وَضُحَىٰهَا
Pali dzuwa ndi kuwala kwake
Ayah 1وَٱلۡقَمَرِ إِذَا تَلَىٰهَا
Ndi pali mwezi umene umatuluka dzuwa litalowa
Ayah 2وَٱلنَّهَارِ إِذَا جَلَّىٰهَا
Ndi masana pamene kumayera
Ayah 3وَٱلَّيۡلِ إِذَا يَغۡشَىٰهَا
Ndi pali usiku umene umabisa
Ayah 4وَٱلسَّمَآءِ وَمَا بَنَىٰهَا
Ndi pali Kumwamba ndi Iye amene adakulenga
Ayah 5وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا طَحَىٰهَا
Ndi pali dziko lapansi ndi Iye amene analitambasula
Ayah 6وَنَفۡسࣲ وَمَا سَوَّىٰهَا
Ndi pali mzimu ndi Iye amene adaulenga
Ayah 7فَأَلۡهَمَهَا فُجُورَهَا وَتَقۡوَىٰهَا
Ndi kumupatsa iye nzeru zodziwa choipa ndi chabwino
Ayah 8قَدۡ أَفۡلَحَ مَن زَكَّىٰهَا
Ndithudi wopambana ndi amene amadziyeretsa
Ayah 9وَقَدۡ خَابَ مَن دَسَّىٰهَا
Ndipo wolephera ndiye amene wadzidetsa
Ayah 10كَذَّبَتۡ ثَمُودُ بِطَغۡوَىٰهَآ
Anthu a Thamoud adakana Mtumwi wawo poukiramoyerekedwa
Ayah 11إِذِ ٱنۢبَعَثَ أَشۡقَىٰهَا
Pamenemunthuolakwakwambiri adayambitsa chipolowe
Ayah 12فَقَالَ لَهُمۡ رَسُولُ ٱللَّهِ نَاقَةَ ٱللَّهِ وَسُقۡيَٰهَا
Ndipo Mthenga wa Mulungu anati kwa iwo: “Samalirani ngamira ya ikazi ya Mulungu ndi tsiku lake lomwa madzi!”
Ayah 13فَكَذَّبُوهُ فَعَقَرُوهَا فَدَمۡدَمَ عَلَيۡهِمۡ رَبُّهُم بِذَنۢبِهِمۡ فَسَوَّىٰهَا
Iwo sadakhulupirire ayi ndipo ngamirayo adaipha. Motero Ambuye wawo adawaononga chifukwa cha machimo awo ndipo adafafaniza onse mosasankha
Ayah 14وَلَا يَخَافُ عُقۡبَٰهَا
Iye sadaope chotsatira chake
Ayah 15