Surah Taa-Haa
Surah Taa-Haa is chapter 20 of the Quran, with 135 verses. This page presents the Arabic text with a Chichewa translation, verse by verse.
طه
Ta Ha
Ayah 1مَآ أَنزَلۡنَا عَلَيۡكَ ٱلۡقُرۡءَانَ لِتَشۡقَىٰٓ
Ife sitidavumbulutse Korani ino kwa iwe ndi cholinga choti uvutike
Ayah 2إِلَّا تَذۡكِرَةࣰ لِّمَن يَخۡشَىٰ
Koma kuti chikhale chilangizo kwa anthu oopa Mulungu
Ayah 3تَنزِيلࣰ ا مِّمَّنۡ خَلَقَ ٱلۡأَرۡضَ وَٱلسَّمَٰوَٰتِ ٱلۡعُلَى
Ndi chivumbulutso chochokera kwa Iye amene adalenga dziko lapansi ndi kumwamba kwenikweniko
Ayah 4ٱلرَّحۡمَٰنُ عَلَى ٱلۡعَرۡشِ ٱسۡتَوَىٰ
Mwini chisoni chosatha amene adaoneka ali pamwamba pa Mpando wa Chifumu
Ayah 5لَهُۥ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَا وَمَا تَحۡتَ ٱلثَّرَىٰ
Zake ndi zonse zimene zili kumwamba ndi pa dziko lapansi ndi zonse zimene zimakhala m’menemo ndiponso zimene zili pansi pa nthaka
Ayah 6وَإِن تَجۡهَرۡ بِٱلۡقَوۡلِ فَإِنَّهُۥ يَعۡلَمُ ٱلسِّرَّ وَأَخۡفَى
Ngati iwe utchula mawu mokweza, ndithudi Iye amadziwa chinsinsi ndiponso chobisika
Ayah 7ٱللَّهُ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَۖ لَهُ ٱلۡأَسۡمَآءُ ٱلۡحُسۡنَىٰ
Mulungu! Kulibe wina wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye yekha. Ake ndi mayina okongola
Ayah 8وَهَلۡ أَتَىٰكَ حَدِيثُ مُوسَىٰٓ
Kodi udamva za mbiri ya Mose
Ayah 9إِذۡ رَءَا نَارࣰ ا فَقَالَ لِأَهۡلِهِ ٱمۡكُثُوٓاْ إِنِّيٓ ءَانَسۡتُ نَارࣰ ا لَّعَلِّيٓ ءَاتِيكُم مِّنۡهَا بِقَبَسٍ أَوۡ أَجِدُ عَلَى ٱلنَّارِ هُدࣰ ى
Pamene iye adaona moto adawauza abale ake kuti, “Dikirani! Ndithudi ine ndaona moto. Mwina ndikubweretserani muuni kuti ndipeze ulangizi pa motopo.”
Ayah 10فَلَمَّآ أَتَىٰهَا نُودِيَ يَٰمُوسَىٰٓ
Pamene iye adafika pafupi ndi moto, adaitanidwa pomutchula dzina lake kuti, “Oh Mose!”
Ayah 11إِنِّيٓ أَنَا۠ رَبُّكَ فَٱخۡلَعۡ نَعۡلَيۡكَ إِنَّكَ بِٱلۡوَادِ ٱلۡمُقَدَّسِ طُوࣰ ى
“Ndithudi, Ine ndine Ambuye wako! Motero chotsa nsapato zako. Ndithudi iwe uli m’dambo lodalitsika la Tuwa.”
Ayah 12وَأَنَا ٱخۡتَرۡتُكَ فَٱسۡتَمِعۡ لِمَا يُوحَىٰٓ
“Ndipo Ine ndakusankha iwe. Kotero mvetsera chimene chikuvumbulutsidwa kwa iwe.”
Ayah 13إِنَّنِيٓ أَنَا ٱللَّهُ لَآ إِلَٰهَ إِلَّآ أَنَا۠ فَٱعۡبُدۡنِي وَأَقِمِ ٱلصَّلَوٰةَ لِذِكۡرِيٓ
Ndithudi Ine ndine Mulungu. Palibe wina wopembedzedwa mwachoonadi koma Ine ndekha motero ndipembedze Ine ndipo pitiriza mapemphero pondikumbukira Ine.”
Ayah 14إِنَّ ٱلسَّاعَةَ ءَاتِيَةٌ أَكَادُ أُخۡفِيهَا لِتُجۡزَىٰ كُلُّ نَفۡسِۭ بِمَا تَسۡعَىٰ
“Ndithudi ola lili nkudza ndipo cholinga changa ndi kulibisa kuti mzimu ulionse udzalipidwe malipiro molingana ndi ntchito zake.”
Ayah 15فَلَا يَصُدَّنَّكَ عَنۡهَا مَن لَّا يُؤۡمِنُ بِهَا وَٱتَّبَعَ هَوَىٰهُ فَتَرۡدَىٰ
“Ndipo usalole kuti munthu amene sakhulupirira za olali ndipo yemwe amachita zimene mtima wake umafuna kuti akusocheretse chifukwa ukhoza kuonongeka.”
Ayah 16وَمَا تِلۡكَ بِيَمِينِكَ يَٰمُوسَىٰ
“Kodi ndi chiyani chimene chili m’dzanja lako la manja iwe Mose?”
Ayah 17قَالَ هِيَ عَصَايَ أَتَوَكَّؤُاْ عَلَيۡهَا وَأَهُشُّ بِهَا عَلَىٰ غَنَمِي وَلِيَ فِيهَا مَـَٔارِبُ أُخۡرَىٰ
Iye adati, “Iyi ndi ndodo yanga, ndi iyoyi ine ndimayedzamira ndipo ndimagwetsera masamba akudya nyama zanga. Imeneyi imandithandiza pa ntchito zambiri kuonjezera pa zimenezi.”
Ayah 18قَالَ أَلۡقِهَا يَٰمُوسَىٰ
Mulungu adati, “Ndodoyo iponye pansi iwe Mose.”
Ayah 19فَأَلۡقَىٰهَا فَإِذَا هِيَ حَيَّةࣱ تَسۡعَىٰ
Mose adaiponya pansi, ndipo taonani! Iyo idasanduka njoka yoyenda mwaliwiro
Ayah 20قَالَ خُذۡهَا وَلَا تَخَفۡۖ سَنُعِيدُهَا سِيرَتَهَا ٱلۡأُولَىٰ
Mulungu adati, “Igwire ndipo usachite mantha ayi. Ife tidzaibwezera monga momwe idalili poyamba.”
Ayah 21وَٱضۡمُمۡ يَدَكَ إِلَىٰ جَنَاحِكَ تَخۡرُجۡ بَيۡضَآءَ مِنۡ غَيۡرِ سُوٓءٍ ءَايَةً أُخۡرَىٰ
“Tsopano kanikiza dzanja lako m’khwapa mwako. Ilo lidzasanduka loyera lopanda matenda ngati chizindikiro china.”
Ayah 22لِنُرِيَكَ مِنۡ ءَايَٰتِنَا ٱلۡكُبۡرَى
“Kuti tikusonyeze zizindikiro zathu zazikulu.”
Ayah 23ٱذۡهَبۡ إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ إِنَّهُۥ طَغَىٰ
“Pita kwa Farawo! Ndithudi iye wadumpha malire onse.”
Ayah 24قَالَ رَبِّ ٱشۡرَحۡ لِي صَدۡرِي
Mose adati, “Ambuye tsekulani chifuwa changa”
Ayah 25وَيَسِّرۡ لِيٓ أَمۡرِي
“Ndipo pepukitsani ntchito yanga.”
Ayah 26وَٱحۡلُلۡ عُقۡدَةࣰ مِّن لِّسَانِي
“Masulani lilime langa ku chibwibwi.”
Ayah 27يَفۡقَهُواْ قَوۡلِي
“Kuti anthu azindikire zonena zanga.”
Ayah 28وَٱجۡعَل لِّي وَزِيرࣰ ا مِّنۡ أَهۡلِي
“Ndipo ndisankhileni munthu wondithandiza kuchokera ku banja langa.”
Ayah 29هَٰرُونَ أَخِي
“Aroni m’bale wanga.”
Ayah 30ٱشۡدُدۡ بِهِۦٓ أَزۡرِي
“Onjezereni mphamvu zanga ndi iye.”
Ayah 31وَأَشۡرِكۡهُ فِيٓ أَمۡرِي
“Ndipo muloleni nayenso kugwira ntchito yanga.”
Ayah 32كَيۡ نُسَبِّحَكَ كَثِيرࣰ ا
“Kuti tizikulemekezani kwambiri.”
Ayah 33وَنَذۡكُرَكَ كَثِيرًا
“Ndi kukukumbukirani kwambiri.”
Ayah 34إِنَّكَ كُنتَ بِنَا بَصِيرࣰ ا
“Ndithudi! Inu muli kutiona nthawi zonse.”
Ayah 35قَالَ قَدۡ أُوتِيتَ سُؤۡلَكَ يَٰمُوسَىٰ
Mulungu adati, “Pempho lako lalandiridwa, iwe Mose.”
Ayah 36وَلَقَدۡ مَنَنَّا عَلَيۡكَ مَرَّةً أُخۡرَىٰٓ
“Ndithudi Ife tidakuonetsa chifundo chathu nthawi ina.”
Ayah 37إِذۡ أَوۡحَيۡنَآ إِلَىٰٓ أُمِّكَ مَا يُوحَىٰٓ
“Pamene tidawauza Amayi ako mawu athu.”
Ayah 38أَنِ ٱقۡذِفِيهِ فِي ٱلتَّابُوتِ فَٱقۡذِفِيهِ فِي ٱلۡيَمِّ فَلۡيُلۡقِهِ ٱلۡيَمُّ بِٱلسَّاحِلِ يَأۡخُذۡهُ عَدُوࣱّ لِّي وَعَدُوࣱّ لَّهُۥۚ وَأَلۡقَيۡتُ عَلَيۡكَ مَحَبَّةࣰ مِّنِّي وَلِتُصۡنَعَ عَلَىٰ عَيۡنِيٓ
Ponena kuti, “Ika mwana wako m’bokosi ndipo umuponye mu mtsinje ndipo mtsinje udzamulavula iye pa mtunda ndipo adzatoledwa ndi mdani wanga ndiponso ndi mdani wake. Ndipo Ine ndidaonetsa chikondi changa pa iwe kuti uleredwa moyang’aniridwa ndi Ine.”
Ayah 39إِذۡ تَمۡشِيٓ أُخۡتُكَ فَتَقُولُ هَلۡ أَدُلُّكُمۡ عَلَىٰ مَن يَكۡفُلُهُۥۖ فَرَجَعۡنَٰكَ إِلَىٰٓ أُمِّكَ كَيۡ تَقَرَّ عَيۡنُهَا وَلَا تَحۡزَنَۚ وَقَتَلۡتَ نَفۡسࣰ ا فَنَجَّيۡنَٰكَ مِنَ ٱلۡغَمِّ وَفَتَنَّٰكَ فُتُونࣰ اۚ فَلَبِثۡتَ سِنِينَ فِيٓ أَهۡلِ مَدۡيَنَ ثُمَّ جِئۡتَ عَلَىٰ قَدَرࣲ يَٰمُوسَىٰ
“Ndipo pamene mlongo wako adapita kwa iwo ndi kunena kuti, Kodi ndikusonyezeni Mayi amene akhoza kumusamala iye? M’menemo ndi mmene tidakubwezera kwa Amayi ako kuti mtima wawo ukhoza kukhazikika ndipo kuti asakhumudwe. Ndipo pamene iwe udapha munthu, Ife tidakupulumutsa ku mavuto ako, ndipo tidakuyesa ndi mayeso ena. Iwe udakhala pakati pa anthu a ku Midiyani zaka zambiri ndipo pomaliza, iwe Mose, udabwera kuno monga momwe zidakonzedwera.”
Ayah 40وَٱصۡطَنَعۡتُكَ لِنَفۡسِي
“Ine ndakusankha iwe kuti unditumikire Ine.”
Ayah 41ٱذۡهَبۡ أَنتَ وَأَخُوكَ بِـَٔايَٰتِي وَلَا تَنِيَا فِي ذِكۡرِي
“Pita iwe ndi m’bale wako ndi zizindikiro zanga ndipo musatope pondikumbukira Ine.”
Ayah 42ٱذۡهَبَآ إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ إِنَّهُۥ طَغَىٰ
“Pitani, nonsenu, kwa Farawo yemwe wadumpha malire.”
Ayah 43فَقُولَا لَهُۥ قَوۡلࣰ ا لَّيِّنࣰ ا لَّعَلَّهُۥ يَتَذَكَّرُ أَوۡ يَخۡشَىٰ
“Ndipo mukayankhule naye ndi mawu oleza kuti mwina akhoza kumva chenjezo kapena kuopa Mulungu.”
Ayah 44قَالَا رَبَّنَآ إِنَّنَا نَخَافُ أَن يَفۡرُطَ عَلَيۡنَآ أَوۡ أَن يَطۡغَىٰ
Iwo adati, “Ambuye wathu! Ndithudi! Ife tiopa kuti abweretsa chilango chake msanga kapena achita zoipa zambiri kwa ife.”
Ayah 45قَالَ لَا تَخَافَآۖ إِنَّنِي مَعَكُمَآ أَسۡمَعُ وَأَرَىٰ
Iye adati, “Musaope! Ndithudi! Ine ndili pamodzi ndi inu. Ine ndimamva zonse ndipo ndimaona.”
Ayah 46فَأۡتِيَاهُ فَقُولَآ إِنَّا رَسُولَا رَبِّكَ فَأَرۡسِلۡ مَعَنَا بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ وَلَا تُعَذِّبۡهُمۡۖ قَدۡ جِئۡنَٰكَ بِـَٔايَةࣲ مِّن رَّبِّكَۖ وَٱلسَّلَٰمُ عَلَىٰ مَنِ ٱتَّبَعَ ٱلۡهُدَىٰٓ
“Motero pitani nonse kwa iye ndipo mukati, ‘Ndithudi ife ndife Atumwi Ambuye wako motero aleke ana a Israyeli kuti apite ndi ife ndipo usawazunzenso ayi. Ndithudi ife takubweretsera zizindikiro zochokera kwa Ambuye wako! Ndipo mtendere udzakhala kwa iye amene atsatira langizo.”
Ayah 47إِنَّا قَدۡ أُوحِيَ إِلَيۡنَآ أَنَّ ٱلۡعَذَابَ عَلَىٰ مَن كَذَّبَ وَتَوَلَّىٰ
“Ndithudi zavumbulutsidwa kwa ife kuti chilango chake chidzagwa pa iye amene amakana zizindikiro zake ndipo sazimvera ayi.”
Ayah 48قَالَ فَمَن رَّبُّكُمَا يَٰمُوسَىٰ
Farawo adati, “Kodi Mose, Ambuye wanu ndani?”
Ayah 49قَالَ رَبُّنَا ٱلَّذِيٓ أَعۡطَىٰ كُلَّ شَيۡءٍ خَلۡقَهُۥ ثُمَّ هَدَىٰ
Iye adati, “Ambuye wathu ndiye amene adapereka maonekedwe osiyanasiyana ku zolengedwa zake ndipo adazilangiza bwinobwino.”
Ayah 50قَالَ فَمَا بَالُ ٱلۡقُرُونِ ٱلۡأُولَىٰ
Farawo adati, “Nanga zinali bwanji ndi anthu a masiku akale?”
Ayah 51قَالَ عِلۡمُهَا عِندَ رَبِّي فِي كِتَٰبࣲۖ لَّا يَضِلُّ رَبِّي وَلَا يَنسَى
Iye adati, “Ambuye wanga yekha ndiye amene adziwa zimenezo ndipo zidalembedwa mu Buku lake. Iye salakwa ndiponso saiwala.”
Ayah 52ٱلَّذِي جَعَلَ لَكُمُ ٱلۡأَرۡضَ مَهۡدࣰ ا وَسَلَكَ لَكُمۡ فِيهَا سُبُلࣰ ا وَأَنزَلَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءࣰ فَأَخۡرَجۡنَا بِهِۦٓ أَزۡوَٰجࣰ ا مِّن نَّبَاتࣲ شَتَّىٰ
Amene adakupangirani dziko lapansi kukhala ngati kama ndipo adakhazikitsa njira zoti inu muziyendamo ndipo watumiza mvula kuchokera kumwamba. Ndipo ameretsa ndi iyo mitundu yosiyanasiyana ya mbewu
Ayah 53كُلُواْ وَٱرۡعَوۡاْ أَنۡعَٰمَكُمۡۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتࣲ لِّأُوْلِي ٱلنُّهَىٰ
Idyani ndiponso dyetsani ziweto zanu. Ndithudi muzimenezi muli zizindikiro kwa anthu ozindikira
Ayah 54۞مِنۡهَا خَلَقۡنَٰكُمۡ وَفِيهَا نُعِيدُكُمۡ وَمِنۡهَا نُخۡرِجُكُمۡ تَارَةً أُخۡرَىٰ
Kuchokera ku dothi tidakulengani inu ndipo ndi ku nthaka kumene tidzakubwezerani ndipo kuchoka ku iyo tidzakuutsani kuti mukhalenso ndi moyo kachiwiri
Ayah 55وَلَقَدۡ أَرَيۡنَٰهُ ءَايَٰتِنَا كُلَّهَا فَكَذَّبَ وَأَبَىٰ
Ndithudi tidamulangiza Farawo zizindikiro ndi umboni wathu koma iye adazikana zonse ndipo sadamvere ayi
Ayah 56قَالَ أَجِئۡتَنَا لِتُخۡرِجَنَا مِنۡ أَرۡضِنَا بِسِحۡرِكَ يَٰمُوسَىٰ
Iye adati, “Kodi iwe Mose wadza kudzatichotsa m’dziko lathu ndi matsenga ako?”
Ayah 57فَلَنَأۡتِيَنَّكَ بِسِحۡرࣲ مِّثۡلِهِۦ فَٱجۡعَلۡ بَيۡنَنَا وَبَيۡنَكَ مَوۡعِدࣰ ا لَّا نُخۡلِفُهُۥ نَحۡنُ وَلَآ أَنتَ مَكَانࣰ ا سُوࣰ ى
“Ndithudi ife tikhoza kukubweretsera matsenga olingana ndi ako. Motero sankha tsiku limene ife kapena iwe siudzalephera kusunga loti tidzakumane iwe ndi ife, pa bwalo pamene tonse tidzakhala ndi mwai wofanana.”
Ayah 58قَالَ مَوۡعِدُكُمۡ يَوۡمُ ٱلزِّينَةِ وَأَن يُحۡشَرَ ٱلنَّاسُ ضُحࣰ ى
Mose adati, “Tsiku lokumana lidzakhale tsiku la chisangalalo ndipo anthu adzasonkhanitsidwe nthawi ya ku m’mawa dzuwa litakwera pang’ono.”
Ayah 59فَتَوَلَّىٰ فِرۡعَوۡنُ فَجَمَعَ كَيۡدَهُۥ ثُمَّ أَتَىٰ
Farawo adachokapo ndipo adasonkhanitsa a matsenga ake ndipo adadza nawo kwa Mose
Ayah 60قَالَ لَهُم مُّوسَىٰ وَيۡلَكُمۡ لَا تَفۡتَرُواْ عَلَى ٱللَّهِ كَذِبࣰ ا فَيُسۡحِتَكُم بِعَذَابࣲۖ وَقَدۡ خَابَ مَنِ ٱفۡتَرَىٰ
Mose adati kwa iwo, “Tsoka kwa inu! Musapeke mabodza okhudza Mulungu chifukwa akhoza kukuonongani ndi chilango. Ndipo, ndithudi, aliyense amene apeka bodza adzalephera mochititsa manyazi
Ayah 61فَتَنَٰزَعُوٓاْ أَمۡرَهُم بَيۡنَهُمۡ وَأَسَرُّواْ ٱلنَّجۡوَىٰ
Anthu a matsenga adakambirana wina ndi mnzake pa zimene angachite ndipo adasunga zokambirana zawo
Ayah 62قَالُوٓاْ إِنۡ هَٰذَٰنِ لَسَٰحِرَٰنِ يُرِيدَانِ أَن يُخۡرِجَاكُم مِّنۡ أَرۡضِكُم بِسِحۡرِهِمَا وَيَذۡهَبَا بِطَرِيقَتِكُمُ ٱلۡمُثۡلَىٰ
Iwo adati, “Anthu awiriwa ndi anthu a matsenga amene afuna kuti akuchotseni m’dziko lanu pogwiritsa ntchito matsenga awo ndikugonjetsa mafumu ndi anthu anu aulemu wawo.”
Ayah 63فَأَجۡمِعُواْ كَيۡدَكُمۡ ثُمَّ ٱئۡتُواْ صَفࣰّ اۚ وَقَدۡ أَفۡلَحَ ٱلۡيَوۡمَ مَنِ ٱسۡتَعۡلَىٰ
“Motero konzekani ndipo muime mu mzere. Iwo amene apambane lero, ndithudi, adzakhala opambanadi.”
Ayah 64قَالُواْ يَٰمُوسَىٰٓ إِمَّآ أَن تُلۡقِيَ وَإِمَّآ أَن نَّكُونَ أَوَّلَ مَنۡ أَلۡقَىٰ
Iwo adati, “Iwe Mose! Kodi udzayamba ndiwe kuponya ndodo yako kapena tiyambe ndife kuponya ndodo zathu?”
Ayah 65قَالَ بَلۡ أَلۡقُواْۖ فَإِذَا حِبَالُهُمۡ وَعِصِيُّهُمۡ يُخَيَّلُ إِلَيۡهِ مِن سِحۡرِهِمۡ أَنَّهَا تَسۡعَىٰ
Iye adati, “Iyayi. Ponyani zanu poyamba.” Ndipo taona ndi mphamvu ya matsenga awo, zingwe ndi ndodo zawo zidaoneka, m’maso mwa Mose, kuti zinali kuyenda mofulumira
Ayah 66فَأَوۡجَسَ فِي نَفۡسِهِۦ خِيفَةࣰ مُّوسَىٰ
Motero Mose adachita mantha mu mtima mwake
Ayah 67قُلۡنَا لَا تَخَفۡ إِنَّكَ أَنتَ ٱلۡأَعۡلَىٰ
Koma Ife tidamuuza kuti, “Usaope! Ndithudi iwe udzapambana.”
Ayah 68وَأَلۡقِ مَا فِي يَمِينِكَ تَلۡقَفۡ مَا صَنَعُوٓاْۖ إِنَّمَا صَنَعُواْ كَيۡدُ سَٰحِرࣲۖ وَلَا يُفۡلِحُ ٱلسَّاحِرُ حَيۡثُ أَتَىٰ
“Ndipo ponya chimene chili m’dzanja lako la manja. Icho chidzameza zinthu zimene iwo akonza chimene ndi chinyengo cha matsenga ndipo munthu wa matsenga sadzapambana ngakhale atakhala odziwa chotani.”
Ayah 69فَأُلۡقِيَ ٱلسَّحَرَةُ سُجَّدࣰ ا قَالُوٓاْ ءَامَنَّا بِرَبِّ هَٰرُونَ وَمُوسَىٰ
Anthu a matsenga adagwa pansi kulambira nati, “Ife takhulupirira mwa Ambuye wa Aroni ndi Mose.”
Ayah 70قَالَ ءَامَنتُمۡ لَهُۥ قَبۡلَ أَنۡ ءَاذَنَ لَكُمۡۖ إِنَّهُۥ لَكَبِيرُكُمُ ٱلَّذِي عَلَّمَكُمُ ٱلسِّحۡرَۖ فَلَأُقَطِّعَنَّ أَيۡدِيَكُمۡ وَأَرۡجُلَكُم مِّنۡ خِلَٰفࣲ وَلَأُصَلِّبَنَّكُمۡ فِي جُذُوعِ ٱلنَّخۡلِ وَلَتَعۡلَمُنَّ أَيُّنَآ أَشَدُّ عَذَابࣰ ا وَأَبۡقَىٰ
Farawo adati, “Kodi inu mukumukhulupirira iye wopanda chilolezo changa? Ndithudi munthu uyu ayenera kukhala mkulu wanu amene adakuphunzitsani matsenga. Ndithudi ine ndidzadula manja anu ndi miyendo yanu mosiyanitsa ndipo, ndithudi, ine ndidzakupachikani pa thunthu la mtengo wa mgwalangwa. Ndipo, ndithudi, inu mudzadziwa kuti ndani mwa ife amene akhoza kupereka chilango chowawa kwambiri ndiponso chosatha.”
Ayah 71قَالُواْ لَن نُّؤۡثِرَكَ عَلَىٰ مَا جَآءَنَا مِنَ ٱلۡبَيِّنَٰتِ وَٱلَّذِي فَطَرَنَاۖ فَٱقۡضِ مَآ أَنتَ قَاضٍۖ إِنَّمَا تَقۡضِي هَٰذِهِ ٱلۡحَيَوٰةَ ٱلدُّنۡيَآ
Iwo adati, “Ife sitifuna iwe kuposa zizindikiro zimene zadza kwa ife ndi Iye amene adatilenga ife. Kotero iwe chita chimene ufuna kuchita chifukwa iwe ukhoza kulamulira za m’moyo uno zokha.”
Ayah 72إِنَّآ ءَامَنَّا بِرَبِّنَا لِيَغۡفِرَ لَنَا خَطَٰيَٰنَا وَمَآ أَكۡرَهۡتَنَا عَلَيۡهِ مِنَ ٱلسِّحۡرِۗ وَٱللَّهُ خَيۡرࣱ وَأَبۡقَىٰٓ
“Ndithudi ife taika chikhulupiriro chathumwaAmbuyewathukutiatikhululukireifemachimo athu ndiponso pa matsenga amene udatikakamiza kuti tichite ndipo malipiro a Mulungu ndi abwino ndiponso osatha pofanizira ndi malipiro ako.”
Ayah 73إِنَّهُۥ مَن يَأۡتِ رَبَّهُۥ مُجۡرِمࣰ ا فَإِنَّ لَهُۥ جَهَنَّمَ لَا يَمُوتُ فِيهَا وَلَا يَحۡيَىٰ
Ndithudi! Aliyense amene adza pamaso pa Ambuye wake ali wamachimo, ndithudi, iye adzaponyedwa ku Gahena kumene sadzakhala ndi moyo kapena imfa
Ayah 74وَمَن يَأۡتِهِۦ مُؤۡمِنࣰ ا قَدۡ عَمِلَ ٱلصَّٰلِحَٰتِ فَأُوْلَٰٓئِكَ لَهُمُ ٱلدَّرَجَٰتُ ٱلۡعُلَىٰ
Koma iye amene adza kwa Iye ndi chikhulupiriro choonadi ndiponso ntchito zabwino, adzakhala ndi ulemerero wapamwamba zedi
Ayah 75جَنَّٰتُ عَدۡنࣲ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ خَٰلِدِينَ فِيهَاۚ وَذَٰلِكَ جَزَآءُ مَن تَزَكَّىٰ
Minda yamuyaya yomwe pansi pake pamayenda mitsinje m’menemo iwo adzakhalamo nthawi zonse. Amenewa ndiwo malipiro a iwo amene amadziyeretsa
Ayah 76وَلَقَدۡ أَوۡحَيۡنَآ إِلَىٰ مُوسَىٰٓ أَنۡ أَسۡرِ بِعِبَادِي فَٱضۡرِبۡ لَهُمۡ طَرِيقࣰ ا فِي ٱلۡبَحۡرِ يَبَسࣰ ا لَّا تَخَٰفُ دَرَكࣰ ا وَلَا تَخۡشَىٰ
Ndithudi Ife tidamuuza Mose kuti, “Nyamuka nthawi yausiku pamodzi ndi akapolo anga ndipo uwatsekulire njira pakati pa nyanja ndipo usaope kuti akupeza, kapena kumira m’nyanja.”
Ayah 77فَأَتۡبَعَهُمۡ فِرۡعَوۡنُ بِجُنُودِهِۦ فَغَشِيَهُم مِّنَ ٱلۡيَمِّ مَا غَشِيَهُمۡ
Ndipo Farawo adawatsatira ndi asirikali ake koma madzi adawamiza onse
Ayah 78وَأَضَلَّ فِرۡعَوۡنُ قَوۡمَهُۥ وَمَا هَدَىٰ
Farawo adasocheretsa anthu ake ndipo sadawatsogolere ayi
Ayah 79يَٰبَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ قَدۡ أَنجَيۡنَٰكُم مِّنۡ عَدُوِّكُمۡ وَوَٰعَدۡنَٰكُمۡ جَانِبَ ٱلطُّورِ ٱلۡأَيۡمَنَ وَنَزَّلۡنَا عَلَيۡكُمُ ٱلۡمَنَّ وَٱلسَّلۡوَىٰ
oh Inu ana a Israyeli! Ife tidakupulumutsani inu kwa adani anu ndipo tidachita lonjezo ndi inu pambali yakumanja kwa Phiri ndipo tidakutsitsirani manna ndi mbalame zokoma
Ayah 80كُلُواْ مِن طَيِّبَٰتِ مَا رَزَقۡنَٰكُمۡ وَلَا تَطۡغَوۡاْ فِيهِ فَيَحِلَّ عَلَيۡكُمۡ غَضَبِيۖ وَمَن يَحۡلِلۡ عَلَيۡهِ غَضَبِي فَقَدۡ هَوَىٰ
Idyani zinthu zabwino zimene tidakupatsani ndipo musaswe malamulo chifukwa mkwiyo wanga ungagwe pa inu. Ndipo yense amene umpeza mkwiyo wanga ndithudi watha
Ayah 81وَإِنِّي لَغَفَّارࣱ لِّمَن تَابَ وَءَامَنَ وَعَمِلَ صَٰلِحࣰ ا ثُمَّ ٱهۡتَدَىٰ
Ndipo, ndithudi, Ine ndimakhululukira aliyense amene alapa, akhulupirira ndipo achita ntchito zabwino ndiponso apitiriza kuzichita
Ayah 82۞وَمَآ أَعۡجَلَكَ عَن قَوۡمِكَ يَٰمُوسَىٰ
“Kodi Mose chakufulumizitsa kubwera kuno ndi kusiya anthu ako ndi chiyani?”
Ayah 83قَالَ هُمۡ أُوْلَآءِ عَلَىٰٓ أَثَرِي وَعَجِلۡتُ إِلَيۡكَ رَبِّ لِتَرۡضَىٰ
Mose adati, “Iwo ali kumbuyo kwangaku akunditsatira. Ndadza mofulumira kwa Inu, Ambuye, kuti musangalale.”
Ayah 84قَالَ فَإِنَّا قَدۡ فَتَنَّا قَوۡمَكَ مِنۢ بَعۡدِكَ وَأَضَلَّهُمُ ٱلسَّامِرِيُّ
Mulungu adati, “Ndithudi! Ife tawayesa mayeso anthu ako popembedza ng’ombe pamene iwe unachoka ndipo Msamiri wawasocheretsa.”
Ayah 85فَرَجَعَ مُوسَىٰٓ إِلَىٰ قَوۡمِهِۦ غَضۡبَٰنَ أَسِفࣰ اۚ قَالَ يَٰقَوۡمِ أَلَمۡ يَعِدۡكُمۡ رَبُّكُمۡ وَعۡدًا حَسَنًاۚ أَفَطَالَ عَلَيۡكُمُ ٱلۡعَهۡدُ أَمۡ أَرَدتُّمۡ أَن يَحِلَّ عَلَيۡكُمۡ غَضَبࣱ مِّن رَّبِّكُمۡ فَأَخۡلَفۡتُم مَّوۡعِدِي
Mose adabwerera kwa anthu ake ndi mkwiyo ndiponso mwachisoni. Iye adati, “Anthu anga! Kodi Ambuye wanu sadakulonjezeni lonjezo labwino? Kodi munaona nthawi ya lonjezo kutalika? Kapena chinali cholinga chanu kuti mkwiyo wa Ambuye wanu udze pa inu ndipo inu muphwanye lonjezo lanu kwa ine?”
Ayah 86قَالُواْ مَآ أَخۡلَفۡنَا مَوۡعِدَكَ بِمَلۡكِنَا وَلَٰكِنَّا حُمِّلۡنَآ أَوۡزَارࣰ ا مِّن زِينَةِ ٱلۡقَوۡمِ فَقَذَفۡنَٰهَا فَكَذَٰلِكَ أَلۡقَى ٱلسَّامِرِيُّ
Iwo adati, “Ife sitinaphwanye lonjezo lako pa chifukwa chathu ayi. Koma ife anatinyamulitsa katundu wa anthu, ndolo, ndipo tinaziponya pa moto. Zimenezo ndizo zimene Msamiri anatiuza.”
Ayah 87فَأَخۡرَجَ لَهُمۡ عِجۡلࣰ ا جَسَدࣰ ا لَّهُۥ خُوَارࣱ فَقَالُواْ هَٰذَآ إِلَٰهُكُمۡ وَإِلَٰهُ مُوسَىٰ فَنَسِيَ
Ndipo iye adawatulutsira iwo chifanizo cha thupi la ng’ombe chimene chidali ndi mawu. Iwo adati, “Uyu ndi mulungu wanu ndi mulungu wa Mose yemwe adamuiwala.”
Ayah 88أَفَلَا يَرَوۡنَ أَلَّا يَرۡجِعُ إِلَيۡهِمۡ قَوۡلࣰ ا وَلَا يَمۡلِكُ لَهُمۡ ضَرࣰّ ا وَلَا نَفۡعࣰ ا
Kodi iwo sanaone kuti sichidawayankhe china chilichonse ndipo kuti chinalibe mphamvu yowapweteka kapena kuwathandiza iwo
Ayah 89وَلَقَدۡ قَالَ لَهُمۡ هَٰرُونُ مِن قَبۡلُ يَٰقَوۡمِ إِنَّمَا فُتِنتُم بِهِۦۖ وَإِنَّ رَبَّكُمُ ٱلرَّحۡمَٰنُ فَٱتَّبِعُونِي وَأَطِيعُوٓاْ أَمۡرِي
Ndithudi Aroni adawauza iwo poyamba kuti, “Oh Anthu anga! Inu muli kungoyesedwa nacho ichi koma, ndithudi, Ambuye wanu ndiye Mwini chisoni chosatha motero tsatireni ine ndipo mverani malamulo anga.”
Ayah 90قَالُواْ لَن نَّبۡرَحَ عَلَيۡهِ عَٰكِفِينَ حَتَّىٰ يَرۡجِعَ إِلَيۡنَا مُوسَىٰ
Iwo adati, “Ife sitidzasiya kuchipembedza ichi mpaka pamene Mose adza kwa ife.”
Ayah 91قَالَ يَٰهَٰرُونُ مَا مَنَعَكَ إِذۡ رَأَيۡتَهُمۡ ضَلُّوٓاْ
Mose adati, “oh Aroni! Kodi chidakuletsa ndi chiyani kuwatsutsa iwo pamene udaona kuti ali kusochera?”
Ayah 92أَلَّا تَتَّبِعَنِۖ أَفَعَصَيۡتَ أَمۡرِي
“Kuti siunanditsatire ine. Kodi waswa lamulo langa?”
Ayah 93قَالَ يَبۡنَؤُمَّ لَا تَأۡخُذۡ بِلِحۡيَتِي وَلَا بِرَأۡسِيٓۖ إِنِّي خَشِيتُ أَن تَقُولَ فَرَّقۡتَ بَيۡنَ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ وَلَمۡ تَرۡقُبۡ قَوۡلِي
Aroni adati, “Mwana wa Amayi anga! Usandikoke ndevu zanga kapena tsitsi langa! Ndithudi! Ine ndidali ndi mantha kuti mwina iwe ukhoza kudzanena kuti, iwe wabzala mpatuko pakati pa ana a Israyeli ndipo siunalemekeze mau anga.”
Ayah 94قَالَ فَمَا خَطۡبُكَ يَٰسَٰمِرِيُّ
Mose adati, “Iwe Msamiri, kodi chifukwa chiyani udachita izi?”
Ayah 95قَالَ بَصُرۡتُ بِمَا لَمۡ يَبۡصُرُواْ بِهِۦ فَقَبَضۡتُ قَبۡضَةࣰ مِّنۡ أَثَرِ ٱلرَّسُولِ فَنَبَذۡتُهَا وَكَذَٰلِكَ سَوَّلَتۡ لِي نَفۡسِي
Iye adati, “Ine ndidaona zimene iwo sanali kuona. Motero ine ndidatenga dothi lodzala m’manja kuchokera ku fumbi lochokera ku phazi la Mtumwi ndi kulitaya. Kotero mzimu wanga udandikakamiza.”
Ayah 96قَالَ فَٱذۡهَبۡ فَإِنَّ لَكَ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ أَن تَقُولَ لَا مِسَاسَۖ وَإِنَّ لَكَ مَوۡعِدࣰ ا لَّن تُخۡلَفَهُۥۖ وَٱنظُرۡ إِلَىٰٓ إِلَٰهِكَ ٱلَّذِي ظَلۡتَ عَلَيۡهِ عَاكِفࣰ اۖ لَّنُحَرِّقَنَّهُۥ ثُمَّ لَنَنسِفَنَّهُۥ فِي ٱلۡيَمِّ نَسۡفًا
Mose adati, “Choka! Ndithudi chilango chako m’moyo uno ndi chakuti udzanena kuti, ‘Musandikhudze.’ Ndithudi iwe uli ndi lonjezo limene siliphwanyidwa ayi. Taona mulungu wako amene wamutumikira ndi mtima wako wonse. Ife tidzaliotcha m’moto ndipo tidzamwaza phulusa lake pa nyanja.”
Ayah 97إِنَّمَآ إِلَٰهُكُمُ ٱللَّهُ ٱلَّذِي لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَۚ وَسِعَ كُلَّ شَيۡءٍ عِلۡمࣰ ا
Mulungu wanu ndi Mulungu mmodzi yekha. Iye amadziwa chilichonse
Ayah 98كَذَٰلِكَ نَقُصُّ عَلَيۡكَ مِنۡ أَنۢبَآءِ مَا قَدۡ سَبَقَۚ وَقَدۡ ءَاتَيۡنَٰكَ مِن لَّدُنَّا ذِكۡرࣰ ا
Kotero Ife tili kukufotokozerani mbiri ya zinthu zimene zidachitika kale. Ndithudi takupatsa chikumbutso
Ayah 99مَّنۡ أَعۡرَضَ عَنۡهُ فَإِنَّهُۥ يَحۡمِلُ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ وِزۡرًا
Iwo amene adzachikana ndithudi adzanyamula katundu wolemera wamachimo pa tsiku la kuuka kwa akufa
Ayah 100خَٰلِدِينَ فِيهِۖ وَسَآءَ لَهُمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ حِمۡلࣰ ا
Iwo adzakhala m’menemo mpaka kalekale ndipo zidzakhala zoipa kwambiri kwa iwo osenza katundu wotereyu tsiku la kuuka kwa kufa
Ayah 101يَوۡمَ يُنفَخُ فِي ٱلصُّورِۚ وَنَحۡشُرُ ٱلۡمُجۡرِمِينَ يَوۡمَئِذࣲ زُرۡقࣰ ا
Tsiku limene lipenga lidzaimbidwa, patsiku limene Ife tidzasonkhanitsa anthu onse ochimwa, maso awo adzakhala obiriwira ndi nkhope zakuda
Ayah 102يَتَخَٰفَتُونَ بَيۡنَهُمۡ إِن لَّبِثۡتُمۡ إِلَّا عَشۡرࣰ ا
Monong’onezana adzakhala ali nkuyankhulana nati, “Inu simunakhale padziko lapansi kupatula masiku khumi okha.”
Ayah 103نَّحۡنُ أَعۡلَمُ بِمَا يَقُولُونَ إِذۡ يَقُولُ أَمۡثَلُهُمۡ طَرِيقَةً إِن لَّبِثۡتُمۡ إِلَّا يَوۡمࣰ ا
Ife tili kudziwa kwambiri zimene adzayankhula, pamene anthu awo angwiro ndi anzeru adzati, “Inu simunakhale padziko kupatula tsiku limodzi lokha.”
Ayah 104وَيَسۡـَٔلُونَكَ عَنِ ٱلۡجِبَالِ فَقُلۡ يَنسِفُهَا رَبِّي نَسۡفࣰ ا
“Ndipo iwo ali kukufunsa za mapiri. Nena, “Ambuye wanga adzawachotsa iwo ndi kuwamwaza ngati fumbi la dothi.”
Ayah 105فَيَذَرُهَا قَاعࣰ ا صَفۡصَفࣰ ا
“Ndipo iye adzawasiya kukhala ngati bwalo lasesese.”
Ayah 106لَّا تَرَىٰ فِيهَا عِوَجࣰ ا وَلَآ أَمۡتࣰ ا
“M’menemo sudzaona malo otsika kapena okwera.”
Ayah 107يَوۡمَئِذࣲ يَتَّبِعُونَ ٱلدَّاعِيَ لَا عِوَجَ لَهُۥۖ وَخَشَعَتِ ٱلۡأَصۡوَاتُ لِلرَّحۡمَٰنِ فَلَا تَسۡمَعُ إِلَّا هَمۡسࣰ ا
Pa tsiku limeneli, anthu adzatsatira woitana wa Mulungu, mopanda chinyengo. Ndipo mawu onse adzachepetsedwa chifukwa cha Mwini chisoni ndipo iwe siudzamva china kupatula mgugu wochepa wa mapazi awo
Ayah 108يَوۡمَئِذࣲ لَّا تَنفَعُ ٱلشَّفَٰعَةُ إِلَّا مَنۡ أَذِنَ لَهُ ٱلرَّحۡمَٰنُ وَرَضِيَ لَهُۥ قَوۡلࣰ ا
Patsiku limeneli, palibe wina amene adzakhala ndi mphamvu yoyankhula m’malo mwawo kupatula yekhayo amene adzalandire chilolezo cha Mwini chisoni ndiponso amene mawu ake ngolandiridwa kwa Iye
Ayah 109يَعۡلَمُ مَا بَيۡنَ أَيۡدِيهِمۡ وَمَا خَلۡفَهُمۡ وَلَا يُحِيطُونَ بِهِۦ عِلۡمࣰ ا
Amadziwa zonse zimene zili kutsogolo kwawo ndiponso zimene zili kumbuyo kwawo ndi zimene zili nkudza pamene iwo sadziwa china chilichonse cha Iye
Ayah 110۞وَعَنَتِ ٱلۡوُجُوهُ لِلۡحَيِّ ٱلۡقَيُّومِۖ وَقَدۡ خَابَ مَنۡ حَمَلَ ظُلۡمࣰ ا
Ndipo nkhope zonse zidzachepetsedwa pamaso pa Mwini moyo wa nthawi zonse amene amateteza china chilichonse. Ndipo yense amene analakwa, ndithudi, ndi olephera
Ayah 111وَمَن يَعۡمَلۡ مِنَ ٱلصَّٰلِحَٰتِ وَهُوَ مُؤۡمِنࣱ فَلَا يَخَافُ ظُلۡمࣰ ا وَلَا هَضۡمࣰ ا
Ndipo iye amene achita ntchito zabwino ndipo ndi munthu wokhulupirira, iye sadzaopa kuponderezedwa kapena kumanidwa malipiro
Ayah 112وَكَذَٰلِكَ أَنزَلۡنَٰهُ قُرۡءَانًا عَرَبِيࣰّ ا وَصَرَّفۡنَا فِيهِ مِنَ ٱلۡوَعِيدِ لَعَلَّهُمۡ يَتَّقُونَ أَوۡ يُحۡدِثُ لَهُمۡ ذِكۡرࣰ ا
Motero Ife tidatumiza Korani mu Chiarabu ndipo tafotokoza m’menemo mowirikiza machenjezo kuti iwo akhale oopa Mulungu kapena kuti Koraniyo iwapatse chiphunzitso kuchokera mu ilo
Ayah 113فَتَعَٰلَى ٱللَّهُ ٱلۡمَلِكُ ٱلۡحَقُّۗ وَلَا تَعۡجَلۡ بِٱلۡقُرۡءَانِ مِن قَبۡلِ أَن يُقۡضَىٰٓ إِلَيۡكَ وَحۡيُهُۥۖ وَقُل رَّبِّ زِدۡنِي عِلۡمࣰ ا
Wolemekezeka ndi Mulungu, Mfumu ya choonadi! Ndipo usafulumire kulakatula Korani, chivumbulutso chake chisanathe koma uyenera kunena kuti, “Ambuye ndionjezereni nzeru.”
Ayah 114وَلَقَدۡ عَهِدۡنَآ إِلَىٰٓ ءَادَمَ مِن قَبۡلُ فَنَسِيَ وَلَمۡ نَجِدۡ لَهُۥ عَزۡمࣰ ا
Ndithudi IfetidachitalonjezondiAdamukalekomaiye adaiwala ndipo sitinapeze chipiriro kwa iye
Ayah 115وَإِذۡ قُلۡنَا لِلۡمَلَٰٓئِكَةِ ٱسۡجُدُواْ لِأٓدَمَ فَسَجَدُوٓاْ إِلَّآ إِبۡلِيسَ أَبَىٰ
Pamenepo Ife tidawauza angelo kuti, “Mugwadireni Adamu.” Ndipo onse adamugwadira koma Satana adakana
Ayah 116فَقُلۡنَا يَٰٓـَٔادَمُ إِنَّ هَٰذَا عَدُوࣱّ لَّكَ وَلِزَوۡجِكَ فَلَا يُخۡرِجَنَّكُمَا مِنَ ٱلۡجَنَّةِ فَتَشۡقَىٰٓ
Ife tidati, “oh iwe Adamu! Ndithudi uyu ndi mdani wako ndiponso mdani wa mkazi wako. Musalole kuti akutulutseni ku Paradiso ndi kukukhazikani m’mavuto.”
Ayah 117إِنَّ لَكَ أَلَّا تَجُوعَ فِيهَا وَلَا تَعۡرَىٰ
Ndithudi muli ndi lonjezo lathu kuti kumeneko inu simudzamva njala kapena kukhala wamaliseche
Ayah 118وَأَنَّكَ لَا تَظۡمَؤُاْ فِيهَا وَلَا تَضۡحَىٰ
Ndiponso inu simudzamva ludzu m’menemo kapena kutentha kwa dzuwa
Ayah 119فَوَسۡوَسَ إِلَيۡهِ ٱلشَّيۡطَٰنُ قَالَ يَٰٓـَٔادَمُ هَلۡ أَدُلُّكَ عَلَىٰ شَجَرَةِ ٱلۡخُلۡدِ وَمُلۡكࣲ لَّا يَبۡلَىٰ
Koma Satana adamunong’oneza nati, “Oh iwe Adamu! Kodi ndingakulangize mtengo wa moyo wosatha ndiponso ufumu wosatha?”
Ayah 120فَأَكَلَا مِنۡهَا فَبَدَتۡ لَهُمَا سَوۡءَٰتُهُمَا وَطَفِقَا يَخۡصِفَانِ عَلَيۡهِمَا مِن وَرَقِ ٱلۡجَنَّةِۚ وَعَصَىٰٓ ءَادَمُ رَبَّهُۥ فَغَوَىٰ
Ndipo onse adadya chipatso cha mumtengo uja kotero udaonekera umaliseche wawo ndipo adayamba kudziveka masamba a m’munda muja. Kotero Adamu adanyoza lamulo la Ambuye wake ndipo adasochera
Ayah 121ثُمَّ ٱجۡتَبَٰهُ رَبُّهُۥ فَتَابَ عَلَيۡهِ وَهَدَىٰ
Ndipo Ambuye wake adamusankha iye ndipo adamukhululukira ndi kumutsogolera kunjira yoyenera
Ayah 122قَالَ ٱهۡبِطَا مِنۡهَا جَمِيعَۢاۖ بَعۡضُكُمۡ لِبَعۡضٍ عَدُوࣱّۖ فَإِمَّا يَأۡتِيَنَّكُم مِّنِّي هُدࣰ ى فَمَنِ ٱتَّبَعَ هُدَايَ فَلَا يَضِلُّ وَلَا يَشۡقَىٰ
Mulungu adati, “Chokani inu m’menemo, nonse awiri, ndipo inu mudzakhala adani a wina ndi mnzake. Pamene ulangizi wanga udzavumbulutsidwa kwa inu, iye amene adzautsatira sadzasochera kapena kuona mavuto.”
Ayah 123وَمَنۡ أَعۡرَضَ عَن ذِكۡرِي فَإِنَّ لَهُۥ مَعِيشَةࣰ ضَنكࣰ ا وَنَحۡشُرُهُۥ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ أَعۡمَىٰ
“Koma iye amene safuna kumvera machenjezo anga, ndithudi, adzakhala movutika ndipo tidzamuukitsa ali wakhungu pa tsiku louka kwa akufa.”
Ayah 124قَالَ رَبِّ لِمَ حَشَرۡتَنِيٓ أَعۡمَىٰ وَقَدۡ كُنتُ بَصِيرࣰ ا
Iye adzati, “Ambuye wanga! Bwanji mwandiukitsa wakhungu, pamene ine ndidali wopenya?”
Ayah 125قَالَ كَذَٰلِكَ أَتَتۡكَ ءَايَٰتُنَا فَنَسِيتَهَاۖ وَكَذَٰلِكَ ٱلۡيَوۡمَ تُنسَىٰ
Mulungu adzati, “Chifukwa chakuti pamene chivumbulutso chathu chinadza kwa iwe udachiiwala. Chimodzimodzi tsiku lino nawenso waiwalidwa.”
Ayah 126وَكَذَٰلِكَ نَجۡزِي مَنۡ أَسۡرَفَ وَلَمۡ يُؤۡمِنۢ بِـَٔايَٰتِ رَبِّهِۦۚ وَلَعَذَابُ ٱلۡأٓخِرَةِ أَشَدُّ وَأَبۡقَىٰٓ
Mmenemundimmenetimalipiriramunthu oswa malamulo amene sakhulupirira chivumbulutso cha Ambuye wake. Koma chilango cha m’moyo umene uli nkudza ndi choopsa ndiponso chosatha
Ayah 127أَفَلَمۡ يَهۡدِ لَهُمۡ كَمۡ أَهۡلَكۡنَا قَبۡلَهُم مِّنَ ٱلۡقُرُونِ يَمۡشُونَ فِي مَسَٰكِنِهِمۡۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتࣲ لِّأُوْلِي ٱلنُّهَىٰ
Kodi iwo saona mibadwo ya anthu imene tidaiononga iwo asanadze? Iwo amayenda pakati pa nyumba zimene iwo anali kukhalamo. Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro kwa anthu a nzeru
Ayah 128وَلَوۡلَا كَلِمَةࣱ سَبَقَتۡ مِن رَّبِّكَ لَكَانَ لِزَامࣰ ا وَأَجَلࣱ مُّسَمࣰّ ى
Akadakhala kuti Ambuye wako sadalonjeze ndi kukhazikitsa nthawi, chilango chawo chikanadza kale
Ayah 129فَٱصۡبِرۡ عَلَىٰ مَا يَقُولُونَ وَسَبِّحۡ بِحَمۡدِ رَبِّكَ قَبۡلَ طُلُوعِ ٱلشَّمۡسِ وَقَبۡلَ غُرُوبِهَاۖ وَمِنۡ ءَانَآيِٕ ٱلَّيۡلِ فَسَبِّحۡ وَأَطۡرَافَ ٱلنَّهَارِ لَعَلَّكَ تَرۡضَىٰ
Motero pirira pa zimene ali kunena ndipo lemekeza ndi kutamanda Ambuye wako dzuwa lisanatuluke ndiponso lisanalowe. Ndipo muyamike Iye nthawi yausiku ndi yausana kuti iwe udzasangalale
Ayah 130وَلَا تَمُدَّنَّ عَيۡنَيۡكَ إِلَىٰ مَا مَتَّعۡنَا بِهِۦٓ أَزۡوَٰجࣰ ا مِّنۡهُمۡ زَهۡرَةَ ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا لِنَفۡتِنَهُمۡ فِيهِۚ وَرِزۡقُ رَبِّكَ خَيۡرࣱ وَأَبۡقَىٰ
Usasirire zinthu zimene tawapatsa anthu chifukwa zimenezi ndi zosangalatsa za m’moyo uno. Ife tingofuna kuwayesa nazo. Koma mphotho ya Ambuye wako ndi yabwino ndipo ndi yosatha
Ayah 131وَأۡمُرۡ أَهۡلَكَ بِٱلصَّلَوٰةِ وَٱصۡطَبِرۡ عَلَيۡهَاۖ لَا نَسۡـَٔلُكَ رِزۡقࣰ اۖ نَّحۡنُ نَرۡزُقُكَۗ وَٱلۡعَٰقِبَةُ لِلتَّقۡوَىٰ
Ndipo lamulira banja lako kupemphera ndipo ukhale wopirira pokwaniritsa mapemphero. Ife sitipempha zinthu kwa iwe koma Ife timakupatsa zofuna zako. Ndipo mapeto abwino ndi a anthu oopa Mulungu
Ayah 132وَقَالُواْ لَوۡلَا يَأۡتِينَا بِـَٔايَةࣲ مِّن رَّبِّهِۦٓۚ أَوَلَمۡ تَأۡتِهِم بَيِّنَةُ مَا فِي ٱلصُّحُفِ ٱلۡأُولَىٰ
Iwo adati, “Bwanji iye satipatsa ife chizindikiro chochokera kwa Ambuye wake?” Kodi iwo sadapatsidwe zizindikiro zambiri zimene zili m’mabuku a kale a Mulungu
Ayah 133وَلَوۡ أَنَّآ أَهۡلَكۡنَٰهُم بِعَذَابࣲ مِّن قَبۡلِهِۦ لَقَالُواْ رَبَّنَا لَوۡلَآ أَرۡسَلۡتَ إِلَيۡنَا رَسُولࣰ ا فَنَتَّبِعَ ءَايَٰتِكَ مِن قَبۡلِ أَن نَّذِلَّ وَنَخۡزَىٰ
Ngati Ife tikadawaononga iwo ndi chilango tisadawatumizire ichi, iwo akadati, “Ambuye wathu! Inu mukadatitumizira Mtumwi, ndithudi, ife tikadatsatira chivumbulutso chanu tisadanyozedwe ndi kuchititsidwa manyazi.”
Ayah 134قُلۡ كُلࣱّ مُّتَرَبِّصࣱ فَتَرَبَّصُواْۖ فَسَتَعۡلَمُونَ مَنۡ أَصۡحَٰبُ ٱلصِّرَٰطِ ٱلسَّوِيِّ وَمَنِ ٱهۡتَدَىٰ
Nena, “onse ali kudikira. Nanunso dikirani ndipo inu mudzadziwa kuti ndani amene adatsatira njira yoyenera ndiponso amene ali otsogozedwa.”
Ayah 135