Surah Al-Qiyaama — The Resurrection
Surah Al-Qiyaama (The Resurrection) is chapter 75 of the Quran, with 40 verses. This page presents the Arabic text with a Chichewa translation, verse by verse.
لَآ أُقۡسِمُ بِيَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِ
Ine ndilumbira pali tsiku lachiweruzo
Ayah 1وَلَآ أُقۡسِمُ بِٱلنَّفۡسِ ٱللَّوَّامَةِ
Ndipo ndilumbira pali munthu amene amadzidzudzula yekha
Ayah 2أَيَحۡسَبُ ٱلۡإِنسَٰنُ أَلَّن نَّجۡمَعَ عِظَامَهُۥ
Kodi munthu amaganiza kuti Ife sitidzalumikiza mafupa ake
Ayah 3بَلَىٰ قَٰدِرِينَ عَلَىٰٓ أَن نُّسَوِّيَ بَنَانَهُۥ
Inde Ife tikhoza kulumikiza mwaubwino nsonga za zala zake
Ayah 4بَلۡ يُرِيدُ ٱلۡإِنسَٰنُ لِيَفۡجُرَ أَمَامَهُۥ
Ngakhale tero, munthu amafuna kupitiliza kuchita zoipa
Ayah 5يَسۡـَٔلُ أَيَّانَ يَوۡمُ ٱلۡقِيَٰمَةِ
Iye amafunsa: “Kodi zimenezi zidzachitika liti?”
Ayah 6فَإِذَا بَرِقَ ٱلۡبَصَرُ
Motero pamene maso adzathodwa
Ayah 7وَخَسَفَ ٱلۡقَمَرُ
Ndipo pamene mwezi udetsedwa
Ayah 8وَجُمِعَ ٱلشَّمۡسُ وَٱلۡقَمَرُ
Pamene dzuwa ndi mwezi zidzakumana
Ayah 9يَقُولُ ٱلۡإِنسَٰنُ يَوۡمَئِذٍ أَيۡنَ ٱلۡمَفَرُّ
Patsikuli munthu adzafunsa kuti: “Kodi ndithawira kuti tsopano?”
Ayah 10كَلَّا لَا وَزَرَ
Iai! Kulibe malo othawirako
Ayah 11إِلَىٰ رَبِّكَ يَوۡمَئِذٍ ٱلۡمُسۡتَقَرُّ
Ndi kwa Ambuye wako kokha kumene kudzakhala kothawira
Ayah 12يُنَبَّؤُاْ ٱلۡإِنسَٰنُ يَوۡمَئِذِۭ بِمَا قَدَّمَ وَأَخَّرَ
Patsiku limeneli, munthu adzauzidwa zonse zimene adachita kuyambira poyamba mpaka pomaliza
Ayah 13بَلِ ٱلۡإِنسَٰنُ عَلَىٰ نَفۡسِهِۦ بَصِيرَةࣱ
Iai! Munthu adzadzichitira umboni wodzineneza yekha
Ayah 14وَلَوۡ أَلۡقَىٰ مَعَاذِيرَهُۥ
Ngakhale kuti iye azidzayesa kudzipulumutsa yekha
Ayah 15لَا تُحَرِّكۡ بِهِۦ لِسَانَكَ لِتَعۡجَلَ بِهِۦٓ
Usagwedeze lilime lako zokhudza Korani ponena mofulumira
Ayah 16إِنَّ عَلَيۡنَا جَمۡعَهُۥ وَقُرۡءَانَهُۥ
Ndi udindo wathu kuisonkhanitsa ndi kukupatsa nzeru kuilakatula iyo
Ayah 17فَإِذَا قَرَأۡنَٰهُ فَٱتَّبِعۡ قُرۡءَانَهُۥ
Ndipo pamene talakatula, tsatira mwandondomeko kalakatulidwe kake
Ayah 18ثُمَّ إِنَّ عَلَيۡنَا بَيَانَهُۥ
Ndi udindo wathu kukufotokozera tanthauzo lake
Ayah 19كَلَّا بَلۡ تُحِبُّونَ ٱلۡعَاجِلَةَ
Iyayi!Komainumukondamoyowothamsanga
Ayah 20وَتَذَرُونَ ٱلۡأٓخِرَةَ
Ndipo simufuna kulabadira za moyo umene uli nkudza
Ayah 21وُجُوهࣱ يَوۡمَئِذࣲ نَّاضِرَةٌ
Nkhope zina, pa tsiku limeneli, zidzakhala zowala ndi chisangalalo
Ayah 22إِلَىٰ رَبِّهَا نَاظِرَةࣱ
Zili kuyang’ana kwa Ambuye wawo
Ayah 23وَوُجُوهࣱ يَوۡمَئِذِۭ بَاسِرَةࣱ
Ndipo nkhope zina, patsiku limeneli, zidzakhala zachisoni
Ayah 24تَظُنُّ أَن يُفۡعَلَ بِهَا فَاقِرَةࣱ
Pozindikira kuti chilango chowawa chidzagwa pa iwo
Ayah 25كَلَّآ إِذَا بَلَغَتِ ٱلتَّرَاقِيَ
Iyayi, pamene ufika mpaka pa khosi
Ayah 26وَقِيلَ مَنۡۜ رَاقࣲ
Ndipo kudzanenedwa kuti: “Kodi palibe woti angamuchize ndi kumupulumutsa ku imfa?”
Ayah 27وَظَنَّ أَنَّهُ ٱلۡفِرَاقُ
Ndipo iye adzadziwa kuti awa ndi mathero a moyo wake
Ayah 28وَٱلۡتَفَّتِ ٱلسَّاقُ بِٱلسَّاقِ
Ndipo mwendo udzatembenuzika pa unzake
Ayah 29إِلَىٰ رَبِّكَ يَوۡمَئِذٍ ٱلۡمَسَاقُ
Tsiku limeneli zonse zidzabwerera kwa Ambuye wako
Ayah 30فَلَا صَدَّقَ وَلَا صَلَّىٰ
Iye sanali kuvomereza chilungamo kapena kupemphera
Ayah 31وَلَٰكِن كَذَّبَ وَتَوَلَّىٰ
Koma m’malo mwake adakana choonadi ndi kubwerera m’mbuyo
Ayah 32ثُمَّ ذَهَبَ إِلَىٰٓ أَهۡلِهِۦ يَتَمَطَّىٰٓ
Ndipo iye anapita kubanja lake monyada ali kudziyamikila yekha
Ayah 33أَوۡلَىٰ لَكَ فَأَوۡلَىٰ
Tsoka kwa iwe. Ndiponso tsoka kwa iwe
Ayah 34ثُمَّ أَوۡلَىٰ لَكَ فَأَوۡلَىٰٓ
Kachiwiri tsoka lili pafupi ndi iwe, tsopano tsoka lili pafupi
Ayah 35أَيَحۡسَبُ ٱلۡإِنسَٰنُ أَن يُتۡرَكَ سُدًى
Kodi munthu amaganiza kuti tidzangomulekerera kuti azichita chilichonse chimene afuna
Ayah 36أَلَمۡ يَكُ نُطۡفَةࣰ مِّن مَّنِيࣲّ يُمۡنَىٰ
Kodi iye sanali dontho la umuna limene lidatuluka
Ayah 37ثُمَّ كَانَ عَلَقَةࣰ فَخَلَقَ فَسَوَّىٰ
Ndipo iye adakhala kam’bulu ka magazi. Ndipo Mulungu adamuumba ndipo adamukonza m’maonekedwe okongola
Ayah 38فَجَعَلَ مِنۡهُ ٱلزَّوۡجَيۡنِ ٱلذَّكَرَ وَٱلۡأُنثَىٰٓ
Ndipo adamulenga m’mitundu iwiri, mwamuna ndi mkazi
Ayah 39أَلَيۡسَ ذَٰلِكَ بِقَٰدِرٍ عَلَىٰٓ أَن يُحۡـِۧيَ ٱلۡمَوۡتَىٰ
Kodi Iye alibe mphamvu yopereka moyo kwa anthu akufa
Ayah 40