Surah Al-A'raaf — The Heights

Surah Al-A'raaf (The Heights) is chapter 7 of the Quran, with 206 verses. This page presents the Arabic text with a Chichewa translation, verse by verse.

الٓمٓصٓ

Alif Lam Mim Sad

Ayah 1

كِتَٰبٌ أُنزِلَ إِلَيۡكَ فَلَا يَكُن فِي صَدۡرِكَ حَرَجࣱ مِّنۡهُ لِتُنذِرَ بِهِۦ وَذِكۡرَىٰ لِلۡمُؤۡمِنِينَ

Buku ili lavumbulutsidwa kwa iwe, mtima wako usavutike ndi kuti uchenjeze ndi ilo ndipo ndi chikumbutso kwa anthu okhulupirira

Ayah 2

ٱتَّبِعُواْ مَآ أُنزِلَ إِلَيۡكُم مِّن رَّبِّكُمۡ وَلَا تَتَّبِعُواْ مِن دُونِهِۦٓ أَوۡلِيَآءَۗ قَلِيلࣰ ا مَّا تَذَكَّرُونَ

Tsatirani zonse zimene zadza kwa inu kuchokera kwa Ambuye wanu ndipo musatsatire wina powonjezerapa Iye. Ndizochepazimenemumakumbukira

Ayah 3

وَكَم مِّن قَرۡيَةٍ أَهۡلَكۡنَٰهَا فَجَآءَهَا بَأۡسُنَا بَيَٰتًا أَوۡ هُمۡ قَآئِلُونَ

Ndipo mizinda ndi yambiri imene Ife tidaononga! Chilango chathu chidadza pa iwo usiku kapena pamene iwo adali kugona nthawi ya masana

Ayah 4

فَمَا كَانَ دَعۡوَىٰهُمۡ إِذۡ جَآءَهُم بَأۡسُنَآ إِلَّآ أَن قَالُوٓاْ إِنَّا كُنَّا ظَٰلِمِينَ

Iwo sadalire mwa mtundu wina uli wonse pamene chilango chathu chinadza kupatula kuti: “Ndithudi ife tidali anthu olakwa.”

Ayah 5

فَلَنَسۡـَٔلَنَّ ٱلَّذِينَ أُرۡسِلَ إِلَيۡهِمۡ وَلَنَسۡـَٔلَنَّ ٱلۡمُرۡسَلِينَ

Ndithudi Ife tidzawafunsa onse amene uthenga wathu udatumizidwa ndipo, ndithudi, Ife tidzafunsa Atumwi

Ayah 6

فَلَنَقُصَّنَّ عَلَيۡهِم بِعِلۡمࣲۖ وَمَا كُنَّا غَآئِبِينَ

Ndipo, ndithudi, tidzawauza modziwa ndipo, ndithudi, sikuti Ife padalibe

Ayah 7

وَٱلۡوَزۡنُ يَوۡمَئِذٍ ٱلۡحَقُّۚ فَمَن ثَقُلَتۡ مَوَٰزِينُهُۥ فَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡمُفۡلِحُونَ

Pa tsiku limenelo muyeso udzakhala wachilungamo. Motero iwo amene muyeso wawo udzakhala wolemera amenewo adzakhala opambana

Ayah 8

وَمَنۡ خَفَّتۡ مَوَٰزِينُهُۥ فَأُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ خَسِرُوٓاْ أَنفُسَهُم بِمَا كَانُواْ بِـَٔايَٰتِنَا يَظۡلِمُونَ

Koma iwo amene muyeso wawo udzakhala wopepuka amenewo ndi olephera chifukwa ankakana chivumbulutso chathu

Ayah 9

وَلَقَدۡ مَكَّنَّٰكُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَجَعَلۡنَا لَكُمۡ فِيهَا مَعَٰيِشَۗ قَلِيلࣰ ا مَّا تَشۡكُرُونَ

Ndipo Ife tidakupatsani ulamuliro padziko ndipo tidakuikirani zofunikira mu moyo wanu koma kuthokoza kwanu ndi kochepa

Ayah 10

وَلَقَدۡ خَلَقۡنَٰكُمۡ ثُمَّ صَوَّرۡنَٰكُمۡ ثُمَّ قُلۡنَا لِلۡمَلَٰٓئِكَةِ ٱسۡجُدُواْ لِأٓدَمَ فَسَجَدُوٓاْ إِلَّآ إِبۡلِيسَ لَمۡ يَكُن مِّنَ ٱلسَّٰجِدِينَ

Ndithudi ife tidakulengani inu ndipo tidakupatsani maonekedwe ndipo Ife tidati kwa angelo: “Mugwadireni Adamu” ndipo onse adamugwadira iye kupatula Iblis amene adakana kukhala mmodzi mwa ogwada

Ayah 11

قَالَ مَا مَنَعَكَ أَلَّا تَسۡجُدَ إِذۡ أَمَرۡتُكَۖ قَالَ أَنَا۠ خَيۡرࣱ مِّنۡهُ خَلَقۡتَنِي مِن نَّارࣲ وَخَلَقۡتَهُۥ مِن طِينࣲ‏

Mulungu adati: “Kodi chakuletsa ndi chiyani kuti umugwadire iye pamene Ine nditakulamula kutero?” Iye adati: “Ine ndine wolemekezeka kuposa Adamu. Inu mudandilenga ine kuchokera ku moto pamene iye mudamulenga kuchokera ku dothi.”

Ayah 12

قَالَ فَٱهۡبِطۡ مِنۡهَا فَمَا يَكُونُ لَكَ أَن تَتَكَبَّرَ فِيهَا فَٱخۡرُجۡ إِنَّكَ مِنَ ٱلصَّٰغِرِينَ

Mulungu adati: “Choka kumene kuno. Ano simalo okhalako munthu wa mtudzu ayi. Choka! Chifukwa iwe ndiwe mmodzi wa anthu onyozedwa.”

Ayah 13

قَالَ أَنظِرۡنِيٓ إِلَىٰ يَوۡمِ يُبۡعَثُونَ

Satana adati, “Mundisunge mpaka pa tsiku la kuuka kwa akufa.”

Ayah 14

قَالَ إِنَّكَ مِنَ ٱلۡمُنظَرِينَ

Mulungu adati, “Iwe ndiwe mmodzi wa iwo amene apatsidwa nthawi.”

Ayah 15

قَالَ فَبِمَآ أَغۡوَيۡتَنِي لَأَقۡعُدَنَّ لَهُمۡ صِرَٰطَكَ ٱلۡمُسۡتَقِيمَ

Satana adati: “Chifukwa chakuti Inu mwandisocheretsa, ine ndidzawadikira pa njira yanu yoyenera.”

Ayah 16

ثُمَّ لَأٓتِيَنَّهُم مِّنۢ بَيۡنِ أَيۡدِيهِمۡ وَمِنۡ خَلۡفِهِمۡ وَعَنۡ أَيۡمَٰنِهِمۡ وَعَن شَمَآئِلِهِمۡۖ وَلَا تَجِدُ أَكۡثَرَهُمۡ شَٰكِرِينَ

“Ndipo ine ndidzabuka patsogolo ndi pambuyo pawo ndipo kuchokera ku mbali ya dzanja lamanja ndi mbali ya dzanja lamanzere ndipo Inu simudzawapeza ambiri a iwo ali othokoza.”

Ayah 17

قَالَ ٱخۡرُجۡ مِنۡهَا مَذۡءُومࣰ ا مَّدۡحُورࣰ اۖ لَّمَن تَبِعَكَ مِنۡهُمۡ لَأَمۡلَأَنَّ جَهَنَّمَ مِنكُمۡ أَجۡمَعِينَ

Mulungu adati: “Tuluka muno wonyozedwa ndi wothamangitsidwa. Ndipo aliyense amene adzakutsata iwe ndithudi ndidzadzadza Gahena ndi inu nonse.”

Ayah 18

وَيَٰٓـَٔادَمُ ٱسۡكُنۡ أَنتَ وَزَوۡجُكَ ٱلۡجَنَّةَ فَكُلَا مِنۡ حَيۡثُ شِئۡتُمَا وَلَا تَقۡرَبَا هَٰذِهِ ٱلشَّجَرَةَ فَتَكُونَا مِنَ ٱلظَّٰلِمِينَ

“O iwe Adamu! Khala iwe ndi mkazi wako ku Paradiso ndipo idyani mmenemo monga mungafunire, koma inu musadzayandikire mtengo uwu chifukwa nonse mungadzakhale odzipondereza nokha.”

Ayah 19

فَوَسۡوَسَ لَهُمَا ٱلشَّيۡطَٰنُ لِيُبۡدِيَ لَهُمَا مَا وُۥرِيَ عَنۡهُمَا مِن سَوۡءَٰتِهِمَا وَقَالَ مَا نَهَىٰكُمَا رَبُّكُمَا عَنۡ هَٰذِهِ ٱلشَّجَرَةِ إِلَّآ أَن تَكُونَا مَلَكَيۡنِ أَوۡ تَكُونَا مِنَ ٱلۡخَٰلِدِينَ

Ndipo Satana anawanong’oneza iwo onse ndi cholinga choti chionekere kwa iwo chimene chinali chobisika ndi chochititsa manyazi ndipo Satana adati: “Ambuye wanu adakuletsani kuti musayandikire mtengo uwu chifukwa sadafune kuti mukhale angelo kapena anthu a muyaya.”

Ayah 20

وَقَاسَمَهُمَآ إِنِّي لَكُمَا لَمِنَ ٱلنَّٰصِحِينَ

Ndipo iye adalumbira pali Mulungu nati: “Ndithudi ine ndi mmodzi wa iwo amene amakufunirani inu zabwino.”

Ayah 21

فَدَلَّىٰهُمَا بِغُرُورࣲۚ فَلَمَّا ذَاقَا ٱلشَّجَرَةَ بَدَتۡ لَهُمَا سَوۡءَٰتُهُمَا وَطَفِقَا يَخۡصِفَانِ عَلَيۡهِمَا مِن وَرَقِ ٱلۡجَنَّةِۖ وَنَادَىٰهُمَا رَبُّهُمَآ أَلَمۡ أَنۡهَكُمَا عَن تِلۡكُمَا ٱلشَّجَرَةِ وَأَقُل لَّكُمَآ إِنَّ ٱلشَّيۡطَٰنَ لَكُمَا عَدُوࣱّ مُّبِينࣱ‏

Motero iye adawanyenga iwo. Ndipo pamene iwo adalawa mtengo uja, maliseche awo adaonekera poyera ndipo onse anayamba kuvala masamba a ku Paradiso. Ndipo Ambuye wawo adawaitana nati: “Kodi Ine sindidakuletseni mtengo uwu ndiponso kukuuzani kuti: ‘Ndithudi Satana ndi mdani wanu weniweni?”

Ayah 22

قَالَا رَبَّنَا ظَلَمۡنَآ أَنفُسَنَا وَإِن لَّمۡ تَغۡفِرۡ لَنَا وَتَرۡحَمۡنَا لَنَكُونَنَّ مِنَ ٱلۡخَٰسِرِينَ

Iwo adati: “Ambuye wathu! Ife tachimwa tokha. Ngati Inu simutikhululukira ndikutimvera chisoni, ndithudi ife tidzakhala m’gulu la anthu olephera

Ayah 23

قَالَ ٱهۡبِطُواْ بَعۡضُكُمۡ لِبَعۡضٍ عَدُوࣱّۖ وَلَكُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ مُسۡتَقَرࣱّ وَمَتَٰعٌ إِلَىٰ حِينࣲ‏

Iye adati: “Tsikani pansi, aliyense wa inu adzakhala mdani wa mnzake. Padziko lapansi padzakhala malo anu okhala ndi a chisangalalo cha kanthawi kochepa.”

Ayah 24

قَالَ فِيهَا تَحۡيَوۡنَ وَفِيهَا تَمُوتُونَ وَمِنۡهَا تُخۡرَجُونَ

Iye anati, “Kumeneko mudzakhala ndi moyo, kumeneko mudzafa ndipo kuchokera kumeneko mudzaukitsidwa.”

Ayah 25

يَٰبَنِيٓ ءَادَمَ قَدۡ أَنزَلۡنَا عَلَيۡكُمۡ لِبَاسࣰ ا يُوَٰرِي سَوۡءَٰتِكُمۡ وَرِيشࣰ اۖ وَلِبَاسُ ٱلتَّقۡوَىٰ ذَٰلِكَ خَيۡرࣱۚ ذَٰلِكَ مِنۡ ءَايَٰتِ ٱللَّهِ لَعَلَّهُمۡ يَذَّكَّرُونَ

Oh inu ana a Adamu! Ife takupatsani zovala kuti mubise umaliseche wanu ndi zovala zokukongoletsani ndi chobvala cha chilungamo chimene chili chabwino. Zimenezo ndi zina mwa zizindikiro za Mulungu kuti akhale okumbuka

Ayah 26

يَٰبَنِيٓ ءَادَمَ لَا يَفۡتِنَنَّكُمُ ٱلشَّيۡطَٰنُ كَمَآ أَخۡرَجَ أَبَوَيۡكُم مِّنَ ٱلۡجَنَّةِ يَنزِعُ عَنۡهُمَا لِبَاسَهُمَا لِيُرِيَهُمَا سَوۡءَٰتِهِمَآۚ إِنَّهُۥ يَرَىٰكُمۡ هُوَ وَقَبِيلُهُۥ مِنۡ حَيۡثُ لَا تَرَوۡنَهُمۡۗ إِنَّا جَعَلۡنَا ٱلشَّيَٰطِينَ أَوۡلِيَآءَ لِلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ

oh inu ana a Adamu! Musalole Satana kuti akunyengeni inu monga momwe anawatulutsitsa makolo anu ku Paradiso, kuwavula nsalu zawo ndi kuwaonetsa maliseche awo. Ndithudi iye pamodzi ndi gulu lake, amakuonani inu kuchokera kumalo amene inu simungathe kuwaona. Ndithudi Ife tidawapanga a Satana kukhala othandiza anthu osakhulupirira

Ayah 27

وَإِذَا فَعَلُواْ فَٰحِشَةࣰ قَالُواْ وَجَدۡنَا عَلَيۡهَآ ءَابَآءَنَا وَٱللَّهُ أَمَرَنَا بِهَاۗ قُلۡ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يَأۡمُرُ بِٱلۡفَحۡشَآءِۖ أَتَقُولُونَ عَلَى ٱللَّهِ مَا لَا تَعۡلَمُونَ

Ndipo pamene iwo achita chinthu chochititsa manyazi amati: “Tinapeza makolo athu ali kuchita ndipo Mulungu watilamula ife kutero.” Nena: “Iyayi; Mulungu salamula chinthu chimene chili chonyansa. Kodi inu muli kunena za Mulungu zimene simuzidziwa?”

Ayah 28

قُلۡ أَمَرَ رَبِّي بِٱلۡقِسۡطِۖ وَأَقِيمُواْ وُجُوهَكُمۡ عِندَ كُلِّ مَسۡجِدࣲ وَٱدۡعُوهُ مُخۡلِصِينَ لَهُ ٱلدِّينَۚ كَمَا بَدَأَكُمۡ تَعُودُونَ

Nena, “Ambuye wanga walamula chilungamo ndi kuti muzimupembedza Iye yekha. Mpembedzeni Iye. Monga momwe adakulengerani poyamba kwa Iye mudzabwerera.”

Ayah 29

فَرِيقًا هَدَىٰ وَفَرِيقًا حَقَّ عَلَيۡهِمُ ٱلضَّلَٰلَةُۚ إِنَّهُمُ ٱتَّخَذُواْ ٱلشَّيَٰطِينَ أَوۡلِيَآءَ مِن دُونِ ٱللَّهِ وَيَحۡسَبُونَ أَنَّهُم مُّهۡتَدُونَ

Gulu lina adalitsogolera ndipo gulu lina liyenera kusochera chifukwa, ndithudi, iwo adasankha a Satana kuti akhale owathandiza ndi atetezi awo m’malo mwa Mulungu ndipo anali kuganizira kuti adali otsogolera

Ayah 30

۞يَٰبَنِيٓ ءَادَمَ خُذُواْ زِينَتَكُمۡ عِندَ كُلِّ مَسۡجِدࣲ وَكُلُواْ وَٱشۡرَبُواْ وَلَا تُسۡرِفُوٓاْۚ إِنَّهُۥ لَا يُحِبُّ ٱلۡمُسۡرِفِينَ

oh inu ana a Adamu! Valani moyenera pamene muli kupemphera ndi kuzungulira Kaaba, idyani ndi kumwa koma musapyole muyeso ayi. Iye sakonda anthu owononga

Ayah 31

قُلۡ مَنۡ حَرَّمَ زِينَةَ ٱللَّهِ ٱلَّتِيٓ أَخۡرَجَ لِعِبَادِهِۦ وَٱلطَّيِّبَٰتِ مِنَ ٱلرِّزۡقِۚ قُلۡ هِيَ لِلَّذِينَ ءَامَنُواْ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا خَالِصَةࣰ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِۗ كَذَٰلِكَ نُفَصِّلُ ٱلۡأٓيَٰتِ لِقَوۡمࣲ يَعۡلَمُونَ

Nena, “Kodi ndani adaletsa kuvala zovala zoyenera zimene Mulungu adapatsa akapolo ake ndiponso zakudya zabwino?” Nena, “Zimenezo ndi zololedwa kwa anthu okhulupirira Mulungu pa moyo uno, ndipo zidzakhala zawo zokha pa tsiku la kuuka kwa akufa.” Mmenemo ndi mmene timaululira poyera chivumbulutso chathu kwa anthu ozindikira

Ayah 32

قُلۡ إِنَّمَا حَرَّمَ رَبِّيَ ٱلۡفَوَٰحِشَ مَا ظَهَرَ مِنۡهَا وَمَا بَطَنَ وَٱلۡإِثۡمَ وَٱلۡبَغۡيَ بِغَيۡرِ ٱلۡحَقِّ وَأَن تُشۡرِكُواْ بِٱللَّهِ مَا لَمۡ يُنَزِّلۡ بِهِۦ سُلۡطَٰنࣰ ا وَأَن تَقُولُواْ عَلَى ٱللَّهِ مَا لَا تَعۡلَمُونَ

Nena, “Ambuye wanga adaletsa ntchito zonse zonyansa kaya zooneka poyera kapena zobisika, machimo, kuponderezana popanda chilungamo, kumphatikiza Mulungu ndi zimene sadalamulire ndi kunena za Mulungu zimene inu simuli kuzidziwa.”

Ayah 33

وَلِكُلِّ أُمَّةٍ أَجَلࣱۖ فَإِذَا جَآءَ أَجَلُهُمۡ لَا يَسۡتَأۡخِرُونَ سَاعَةࣰ وَلَا يَسۡتَقۡدِمُونَ

Mtundu uliwonse uli ndi nthawi yake ya chiweruzo, ndipo ngati nthawi yawo ikwana, iwo sangachedwetse kapena kuonjezera ola limodzi

Ayah 34

يَٰبَنِيٓ ءَادَمَ إِمَّا يَأۡتِيَنَّكُمۡ رُسُلࣱ مِّنكُمۡ يَقُصُّونَ عَلَيۡكُمۡ ءَايَٰتِي فَمَنِ ٱتَّقَىٰ وَأَصۡلَحَ فَلَا خَوۡفٌ عَلَيۡهِمۡ وَلَا هُمۡ يَحۡزَنُونَ

oh inu ana a Adamu! Ngati Atumwi a mtundu wanu adzadza kwa inu kudzakulalikirani chivumbulutso changa ndipo aliyense amene akhala olungama ndi kumachita zabwino, iwo sadzaopa china chilichonse kapena kuda nkhawa

Ayah 35

وَٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا وَٱسۡتَكۡبَرُواْ عَنۡهَآ أُوْلَٰٓئِكَ أَصۡحَٰبُ ٱلنَّارِۖ هُمۡ فِيهَا خَٰلِدُونَ

Ndipo onse amene akana chivumbulutso chathu ndi kuchinyoza, iwo adzakhala eni ake a ku moto ndipo adzakhala kumeneko mpaka kalekale

Ayah 36

فَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّنِ ٱفۡتَرَىٰ عَلَى ٱللَّهِ كَذِبًا أَوۡ كَذَّبَ بِـَٔايَٰتِهِۦٓۚ أُوْلَٰٓئِكَ يَنَالُهُمۡ نَصِيبُهُم مِّنَ ٱلۡكِتَٰبِۖ حَتَّىٰٓ إِذَا جَآءَتۡهُمۡ رُسُلُنَا يَتَوَفَّوۡنَهُمۡ قَالُوٓاْ أَيۡنَ مَا كُنتُمۡ تَدۡعُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِۖ قَالُواْ ضَلُّواْ عَنَّا وَشَهِدُواْ عَلَىٰٓ أَنفُسِهِمۡ أَنَّهُمۡ كَانُواْ كَٰفِرِينَ

Kodi wochimwa kwambiri ndani kuposa munthu amene amapeka bodza lokhudza Mulungu kapena amene akana chivumbulutso chake? Anthu otere adzalandira gawo lawo lokonzedwera iwo kuchokera m’Buku mpaka pamene angelo adzadza kudzachotsa miyoyo yawo ndipo iwo adzawauza kuti, “Kodi mafano anu aja ali kuti tsopano, amene mudali kuwapembedza yowonjezera pa Mulungu?” Iwo adzati: “Atithawira.” Ndipo iwo adzadzichitira umboni okha kuti iwo adali anthu osakhulupirira

Ayah 37

قَالَ ٱدۡخُلُواْ فِيٓ أُمَمࣲ قَدۡ خَلَتۡ مِن قَبۡلِكُم مِّنَ ٱلۡجِنِّ وَٱلۡإِنسِ فِي ٱلنَّارِۖ كُلَّمَا دَخَلَتۡ أُمَّةࣱ لَّعَنَتۡ أُخۡتَهَاۖ حَتَّىٰٓ إِذَا ٱدَّارَكُواْ فِيهَا جَمِيعࣰ ا قَالَتۡ أُخۡرَىٰهُمۡ لِأُولَىٰهُمۡ رَبَّنَا هَٰٓؤُلَآءِ أَضَلُّونَا فَـَٔاتِهِمۡ عَذَابࣰ ا ضِعۡفࣰ ا مِّنَ ٱلنَّارِۖ قَالَ لِكُلࣲّ ضِعۡفࣱ وَلَٰكِن لَّا تَعۡلَمُونَ

Mulungu adzati: “Lowani, mgulu la mitundu amene adalipo inu musanadze, anthu ndi majin, kupita ku moto, ndipo pamene uzidzalowa mtundu uliwonse udzakhala uli kutemberera mtundu umene udalipo iwo usanadze mpaka pamene adzasonkhanitsidwa onse m’moto ndipo mtundu womaliza udzati kwa mtundu woyambirira, ‘Ambuye wathu! Awa ndiwo anthu amene adatisokoneza ife motero apatseni chilango choonjezedwa kawiri m’moto.” Iye adzati: “Kwa aliyense kuli chilango chowilikiza koma inu simudziwa.”

Ayah 38

وَقَالَتۡ أُولَىٰهُمۡ لِأُخۡرَىٰهُمۡ فَمَا كَانَ لَكُمۡ عَلَيۡنَا مِن فَضۡلࣲ فَذُوقُواْ ٱلۡعَذَابَ بِمَا كُنتُمۡ تَكۡسِبُونَ

Ndipo m’badwo woyamba udzati kwa m’badwo womaliza, “Inu simunachite zabwino kuposa ife motero lawani chilango cha ntchito zanu zimene mudali kuchita.”

Ayah 39

إِنَّ ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا وَٱسۡتَكۡبَرُواْ عَنۡهَا لَا تُفَتَّحُ لَهُمۡ أَبۡوَٰبُ ٱلسَّمَآءِ وَلَا يَدۡخُلُونَ ٱلۡجَنَّةَ حَتَّىٰ يَلِجَ ٱلۡجَمَلُ فِي سَمِّ ٱلۡخِيَاطِۚ وَكَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلۡمُجۡرِمِينَ

Ndithudi amene amati zizindikiro zathu ndi zabodza ndipo amazinyoza izo, makomo a kumwamba sadzatsegulidwa kwa iwo ndipo iwo sadzalowa ku Paradiso pokhapokha ngati ngamira italowa pa diso la zingano. Mmenemo ndi mmene timalipirira anthu ochita zoipa malipiro awo

Ayah 40

لَهُم مِّن جَهَنَّمَ مِهَادࣱ وَمِن فَوۡقِهِمۡ غَوَاشࣲۚ وَكَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلظَّٰلِمِينَ

Wawo adzakhala kama wa moto ndipo pamwamba pawo padzakhala malawi a moto. M’menemo ndi m’mene tidzawalipirira anthu ochita zoipa

Ayah 41

وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ لَا نُكَلِّفُ نَفۡسًا إِلَّا وُسۡعَهَآ أُوْلَٰٓئِكَ أَصۡحَٰبُ ٱلۡجَنَّةِۖ هُمۡ فِيهَا خَٰلِدُونَ

Koma iwo amene anakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino; Ife sitisenzetsa munthu katundu amene sangathe kumunyamula; iwo ndi anthu a ku Paradiso. Ndipo adzakhalako mpaka kalekale

Ayah 42

وَنَزَعۡنَا مَا فِي صُدُورِهِم مِّنۡ غِلࣲّ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهِمُ ٱلۡأَنۡهَٰرُۖ وَقَالُواْ ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ ٱلَّذِي هَدَىٰنَا لِهَٰذَا وَمَا كُنَّا لِنَهۡتَدِيَ لَوۡلَآ أَنۡ هَدَىٰنَا ٱللَّهُۖ لَقَدۡ جَآءَتۡ رُسُلُ رَبِّنَا بِٱلۡحَقِّۖ وَنُودُوٓاْ أَن تِلۡكُمُ ٱلۡجَنَّةُ أُورِثۡتُمُوهَا بِمَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ

Ndipo Ife tidzachotsa chidani m’mitima mwawo ndipo mitsinje idzayenda pansi pa mapazi awo ndipo iwo adzati: “Kuyamikidwa ndi kwa Mulungu amene watitsogolera ife ku izi ndipo ife sitikadakhala otsogozedwa pakadapanda Mulungu kutitsogolera! Ndithudi Atumwi a Ambuye wathu adadza ndi choonadi.” Ndipo zidzanenedwa kwa iwo kuti: “Iyi ndiyo Paradiso imene mwailandira chifukwa cha ntchito zanu zimene mudali kuchita.”

Ayah 43

وَنَادَىٰٓ أَصۡحَٰبُ ٱلۡجَنَّةِ أَصۡحَٰبَ ٱلنَّارِ أَن قَدۡ وَجَدۡنَا مَا وَعَدَنَا رَبُّنَا حَقࣰّ ا فَهَلۡ وَجَدتُّم مَّا وَعَدَ رَبُّكُمۡ حَقࣰّ اۖ قَالُواْ نَعَمۡۚ فَأَذَّنَ مُؤَذِّنُۢ بَيۡنَهُمۡ أَن لَّعۡنَةُ ٱللَّهِ عَلَى ٱلظَّٰلِمِينَ

Ndipo anthu okhala ku Paradiso adzaitana anthu a ku Moto. “Ndithudi chimene adatilonjeza ife Ambuye wathu tachipeza kuti ndi choona. Kodi inu mwapeza chomwe adakulonjezani Ambuye wanu kuti ndi choona?” Iwo adzati: Inde. Ndipo wofuula adzanena pakati pawo: “Matemberero a Mulungu ali pa anthu olakwa.”

Ayah 44

ٱلَّذِينَ يَصُدُّونَ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِ وَيَبۡغُونَهَا عِوَجࣰ ا وَهُم بِٱلۡأٓخِرَةِ كَٰفِرُونَ

Iwo amene anali kuletsa anzawo kutsatira njira ya Mulungu ndipo amafuna kuti iyo ikhale yokhotakhota ndipo adalibe chikhulupiriro m’moyo umene uli nkudza

Ayah 45

وَبَيۡنَهُمَا حِجَابࣱۚ وَعَلَى ٱلۡأَعۡرَافِ رِجَالࣱ يَعۡرِفُونَ كُلَّۢا بِسِيمَىٰهُمۡۚ وَنَادَوۡاْ أَصۡحَٰبَ ٱلۡجَنَّةِ أَن سَلَٰمٌ عَلَيۡكُمۡۚ لَمۡ يَدۡخُلُوهَا وَهُمۡ يَطۡمَعُونَ

Ndipo pakati pawo padzakhala chotchinga ndi chipupa mmene mudzakhala anthu amene adzazindikira wina aliyense poona zizindikiro zawo. Iwo adzaitana anthu a ku Paradiso: Mtendere ukhale pa inu. Koma panthawi imeneyo iwo adzakhala asadalowe ku Paradiso koma iwo adzakhala ndi chikhulupiriro choti adzalowanso mopanda chikaiko

Ayah 46

۞وَإِذَا صُرِفَتۡ أَبۡصَٰرُهُمۡ تِلۡقَآءَ أَصۡحَٰبِ ٱلنَّارِ قَالُواْ رَبَّنَا لَا تَجۡعَلۡنَا مَعَ ٱلۡقَوۡمِ ٱلظَّٰلِمِينَ

Ndipo pamene iwo adzaona iwo amene adzakhala ku moto, iwo adzati: “Oh Ambuye wathu! Musatiike ife malo a anthu oipa.”

Ayah 47

وَنَادَىٰٓ أَصۡحَٰبُ ٱلۡأَعۡرَافِ رِجَالࣰ ا يَعۡرِفُونَهُم بِسِيمَىٰهُمۡ قَالُواْ مَآ أَغۡنَىٰ عَنكُمۡ جَمۡعُكُمۡ وَمَا كُنتُمۡ تَسۡتَكۡبِرُونَ

Ndipo anthu a m’chipupa adzawaitana anthu omwe adzawadziwa ndi zizindikiro zawo ndipo adzati: “Kodi kuchuluka kwanu, kwakuthandizani chiani ndiponso mwano umene mumaonetsa ku chipembedzo?”

Ayah 48

أَهَٰٓؤُلَآءِ ٱلَّذِينَ أَقۡسَمۡتُمۡ لَا يَنَالُهُمُ ٱللَّهُ بِرَحۡمَةٍۚ ٱدۡخُلُواْ ٱلۡجَنَّةَ لَا خَوۡفٌ عَلَيۡكُمۡ وَلَآ أَنتُمۡ تَحۡزَنُونَ

Kodi awa ndi anthu amene munkalumbira kuti sadzalandira chisomo cha Mulungu? “Lowani ku Paradiso, inu simudzachita mantha ndiponso simudzada nkhawa ayi.”

Ayah 49

وَنَادَىٰٓ أَصۡحَٰبُ ٱلنَّارِ أَصۡحَٰبَ ٱلۡجَنَّةِ أَنۡ أَفِيضُواْ عَلَيۡنَا مِنَ ٱلۡمَآءِ أَوۡ مِمَّا رَزَقَكُمُ ٱللَّهُۚ قَالُوٓاْ إِنَّ ٱللَّهَ حَرَّمَهُمَا عَلَى ٱلۡكَٰفِرِينَ

Ndipo anthu a ku Moto adzaitana anthu a ku Paradiso kuti, “Tithireni madzi kapena china chilichonse chimene Mulungu wakupatsani inu!” Anthu a ku Paradiso adzati, “Mulungu adaletsa zonse ziwiri kuti anthu osakhulupirira alandire.”

Ayah 50

ٱلَّذِينَ ٱتَّخَذُواْ دِينَهُمۡ لَهۡوࣰ ا وَلَعِبࣰ ا وَغَرَّتۡهُمُ ٱلۡحَيَوٰةُ ٱلدُّنۡيَاۚ فَٱلۡيَوۡمَ نَنسَىٰهُمۡ كَمَا نَسُواْ لِقَآءَ يَوۡمِهِمۡ هَٰذَا وَمَا كَانُواْ بِـَٔايَٰتِنَا يَجۡحَدُونَ

“Iwo amene adasandutsa chipembedzo chawo ngatinthabwalandichoseweretsandipoadalikunyengedwa ndi zokoma za m’moyo wa padziko lapansi. Motero lero Ife tiwaiwala monga mmene adaiwalira za kukumana kwa tsiku lawoli ndi chifukwa chokana zizindikiro zathu.”

Ayah 51

وَلَقَدۡ جِئۡنَٰهُم بِكِتَٰبࣲ فَصَّلۡنَٰهُ عَلَىٰ عِلۡمٍ هُدࣰ ى وَرَحۡمَةࣰ لِّقَوۡمࣲ يُؤۡمِنُونَ

Ndithudi Ifetawabweretsera Bukum’menetalongosola za nzeru, chilangizo ndi madalitso kwa anthu okhulupirira kwenikweni

Ayah 52

هَلۡ يَنظُرُونَ إِلَّا تَأۡوِيلَهُۥۚ يَوۡمَ يَأۡتِي تَأۡوِيلُهُۥ يَقُولُ ٱلَّذِينَ نَسُوهُ مِن قَبۡلُ قَدۡ جَآءَتۡ رُسُلُ رَبِّنَا بِٱلۡحَقِّ فَهَل لَّنَا مِن شُفَعَآءَ فَيَشۡفَعُواْ لَنَآ أَوۡ نُرَدُّ فَنَعۡمَلَ غَيۡرَ ٱلَّذِي كُنَّا نَعۡمَلُۚ قَدۡ خَسِرُوٓاْ أَنفُسَهُمۡ وَضَلَّ عَنۡهُم مَّا كَانُواْ يَفۡتَرُونَ

Kodi iwo akudikira kuti chikwaniritsidwe? Patsiku limene chidzakwaniritsidwe iwo amene adaliiwala kale adzati, “Ndithudi,Atumwi aAmbuye wathu adadza ndi choonadi. Kodi palibe wina amene akhoza kutilankhulira m’malo mwathu? Kapena kuti tibwezedwe kupitanso ku dziko lapansi kuti tikachite nthito zabwino osati zoipa zimene timachita?” Ndithudi iwo adadziononga okha ndipo chonse chimene adali kupeka chawathawira iwo

Ayah 53

إِنَّ رَبَّكُمُ ٱللَّهُ ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ فِي سِتَّةِ أَيَّامࣲ ثُمَّ ٱسۡتَوَىٰ عَلَى ٱلۡعَرۡشِۖ يُغۡشِي ٱلَّيۡلَ ٱلنَّهَارَ يَطۡلُبُهُۥ حَثِيثࣰ ا وَٱلشَّمۡسَ وَٱلۡقَمَرَ وَٱلنُّجُومَ مُسَخَّرَٰتِۭ بِأَمۡرِهِۦٓۗ أَلَا لَهُ ٱلۡخَلۡقُ وَٱلۡأَمۡرُۗ تَبَارَكَ ٱللَّهُ رَبُّ ٱلۡعَٰلَمِينَ

Ndithudi Ambuye wanu ndi Mulungu, amene m’masiku asanu ndi limodzi adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndipo atatero adabuka pamwamba pa Mpando wake wa Chifumu. Iye amavundikira usiku ndi usana ndipo mofulumira usiku umatsata usana. Ndipo dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zimayenda motsatira malamulo ake. Ndithudi zake ndi zolengedwa zonse ndi ulamuliro. Olemekezeka akhale Mulungu, Ambuye wa zolengedwa zonse

Ayah 54

ٱدۡعُواْ رَبَّكُمۡ تَضَرُّعࣰ ا وَخُفۡيَةًۚ إِنَّهُۥ لَا يُحِبُّ ٱلۡمُعۡتَدِينَ

Pemphani kwa Ambuye wanu modzichepetsa ndi mwamseri. Iye sakonda anthu oswa malamulo

Ayah 55

وَلَا تُفۡسِدُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ بَعۡدَ إِصۡلَٰحِهَا وَٱدۡعُوهُ خَوۡفࣰ ا وَطَمَعًاۚ إِنَّ رَحۡمَتَ ٱللَّهِ قَرِيبࣱ مِّنَ ٱلۡمُحۡسِنِينَ

Ndipo musayambitse chisokonezo padziko ilo litakonzedwa ndipo pemphani kwa Iye mwamantha ndi chikhulupiriro; ndithudi, chifundo cha Mulungu chili pafupi ndi anthu ochita zabwino

Ayah 56

وَهُوَ ٱلَّذِي يُرۡسِلُ ٱلرِّيَٰحَ بُشۡرَۢا بَيۡنَ يَدَيۡ رَحۡمَتِهِۦۖ حَتَّىٰٓ إِذَآ أَقَلَّتۡ سَحَابࣰ ا ثِقَالࣰ ا سُقۡنَٰهُ لِبَلَدࣲ مَّيِّتࣲ فَأَنزَلۡنَا بِهِ ٱلۡمَآءَ فَأَخۡرَجۡنَا بِهِۦ مِن كُلِّ ٱلثَّمَرَٰتِۚ كَذَٰلِكَ نُخۡرِجُ ٱلۡمَوۡتَىٰ لَعَلَّكُمۡ تَذَكَّرُونَ

Iye ndi amene amatumiza mphepo ngati yobweretsa uthenga wabwino umene umadza pambuyo pa chisomo chake. Mpaka pamene iyo isonkhanitsa mitambo yolemera, timaiyendetsa kupita ku nthaka yakufa ndipo timatumiza mvula kuti igwe pa iyo. Ndipo timameretsa zipatso za mitundu mitundu. Mmenemu ndi mmene tidzadzutsire anthu akufa kuti mwina mukhoza ku chenjezedwa

Ayah 57

وَٱلۡبَلَدُ ٱلطَّيِّبُ يَخۡرُجُ نَبَاتُهُۥ بِإِذۡنِ رَبِّهِۦۖ وَٱلَّذِي خَبُثَ لَا يَخۡرُجُ إِلَّا نَكِدࣰ اۚ كَذَٰلِكَ نُصَرِّفُ ٱلۡأٓيَٰتِ لِقَوۡمࣲ يَشۡكُرُونَ

Nthaka yabwino imabereka zipatso mwachifuniro cha Mulungu. Nthaka yoipa siibereka chilichonse pokhapokha movutikira. Motero timafotokoza zivumbulutso zathu poyera kwa anthu amene amathokoza

Ayah 58

لَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا نُوحًا إِلَىٰ قَوۡمِهِۦ فَقَالَ يَٰقَوۡمِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ مَا لَكُم مِّنۡ إِلَٰهٍ غَيۡرُهُۥٓ إِنِّيٓ أَخَافُ عَلَيۡكُمۡ عَذَابَ يَوۡمٍ عَظِيمࣲ‏

Ndithudi Ife tidatumiza Nowa kwa anthu ake ndipo iye adati: “Oh anthu anga! Pembedzani Mulungu! Inu mulibe mulungu wina kupatula Iye yekha. Ndithudi ine ndili kuchita mantha ndi chilango chowawa chimene chidzadza pa inu patsiku lalikulu.”

Ayah 59

قَالَ ٱلۡمَلَأُ مِن قَوۡمِهِۦٓ إِنَّا لَنَرَىٰكَ فِي ضَلَٰلࣲ مُّبِينࣲ‏

Atsogoleri a anthu ake adati: “Ndithudi ife tili kuona kuti iwe wasochera kwambiri.”

Ayah 60

قَالَ يَٰقَوۡمِ لَيۡسَ بِي ضَلَٰلَةࣱ وَلَٰكِنِّي رَسُولࣱ مِّن رَّبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ

Iye adati: “oh anthu anga! Ine sindine wosochera, koma ndine Mtumwi wochokera kwa Ambuye wazolengedwa zonse.”

Ayah 61

أُبَلِّغُكُمۡ رِسَٰلَٰتِ رَبِّي وَأَنصَحُ لَكُمۡ وَأَعۡلَمُ مِنَ ٱللَّهِ مَا لَا تَعۡلَمُونَ

“Ndipo ndili kukulalikirani uthenga wa Ambuye wanga ndi kukulangizani inu. Ndipo ndili kudziwa kuchokera kwa Mulungu zimene inu simukudziwa ayi.”

Ayah 62

أَوَعَجِبۡتُمۡ أَن جَآءَكُمۡ ذِكۡرࣱ مِّن رَّبِّكُمۡ عَلَىٰ رَجُلࣲ مِّنكُمۡ لِيُنذِرَكُمۡ وَلِتَتَّقُواْ وَلَعَلَّكُمۡ تُرۡحَمُونَ

“Kodi inu mukudabwa kuti kwadza kwa inu chenjezo lochokera kwa Ambuye wanu kudzera mwa munthu amene ali pakati panu kuti akuchenjezeni kuti mukhale anthu oopa Mulungu ndi kuti mupeze chisomo chake?”

Ayah 63

فَكَذَّبُوهُ فَأَنجَيۡنَٰهُ وَٱلَّذِينَ مَعَهُۥ فِي ٱلۡفُلۡكِ وَأَغۡرَقۡنَا ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَآۚ إِنَّهُمۡ كَانُواْ قَوۡمًا عَمِينَ

Koma iwo adamutsutsa ndipo Ife tidamupulumutsa iye pamodzi ndi amene adali ndi iye M’chombo ndipo tidawamiza onse amene adakana chivumbulutso chathu. Ndithudi iwo adali anthu akhungu

Ayah 64

۞وَإِلَىٰ عَادٍ أَخَاهُمۡ هُودࣰ اۚ قَالَ يَٰقَوۡمِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ مَا لَكُم مِّنۡ إِلَٰهٍ غَيۡرُهُۥٓۚ أَفَلَا تَتَّقُونَ

Ndipo kwa Ad tidatumiza m’bale wawo Hud. Iye adati: “Oh anthu anga! Pembedzani Mulungu! Inu mulibe mulungu wina koma Iye yekha basi. Kodi simuopa?”

Ayah 65

قَالَ ٱلۡمَلَأُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ مِن قَوۡمِهِۦٓ إِنَّا لَنَرَىٰكَ فِي سَفَاهَةࣲ وَإِنَّا لَنَظُنُّكَ مِنَ ٱلۡكَٰذِبِينَ

Atsogoleri a anthu osakhulupirira ochokera ku mtundu wa Hudadati:“Ifetilikukuonakutiiwendiwewopusandipo ife tili kuganiza kuti ndiwe mmodzi wa anthu a bodza.”

Ayah 66

قَالَ يَٰقَوۡمِ لَيۡسَ بِي سَفَاهَةࣱ وَلَٰكِنِّي رَسُولࣱ مِّن رَّبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ

Iye adati: “oh anthu anga! Ine sindine wopusa koma ndine Mtumwi wochokera kwa Ambuye wazolengedwa zonse.”

Ayah 67

أُبَلِّغُكُمۡ رِسَٰلَٰتِ رَبِّي وَأَنَا۠ لَكُمۡ نَاصِحٌ أَمِينٌ

“Ine ndili kukulalikirani Uthenga wa Ambuye wanga ndipo ndine mchenjezi wanu wokhulupirika.”

Ayah 68

أَوَعَجِبۡتُمۡ أَن جَآءَكُمۡ ذِكۡرࣱ مِّن رَّبِّكُمۡ عَلَىٰ رَجُلࣲ مِّنكُمۡ لِيُنذِرَكُمۡۚ وَٱذۡكُرُوٓاْ إِذۡ جَعَلَكُمۡ خُلَفَآءَ مِنۢ بَعۡدِ قَوۡمِ نُوحࣲ وَزَادَكُمۡ فِي ٱلۡخَلۡقِ بَصۜۡطَةࣰۖ فَٱذۡكُرُوٓاْ ءَالَآءَ ٱللَّهِ لَعَلَّكُمۡ تُفۡلِحُونَ

“Kodimukudabwakutikwadzachikumbutsochochokera kwa Ambuye kudzera mwa munthu wa mtundu wanu kuti akhale okuchenjezani inu? Ndipo kumbukirani kuti adakupangani inu kukhala alowam’malo a anthu a Nowa ndipo adakuonjezerani mphamvu pachilengedwe. Motero kumbukirani madalitso a Mulungu kuti mupambane.”

Ayah 69

قَالُوٓاْ أَجِئۡتَنَا لِنَعۡبُدَ ٱللَّهَ وَحۡدَهُۥ وَنَذَرَ مَا كَانَ يَعۡبُدُ ءَابَآؤُنَا فَأۡتِنَا بِمَا تَعِدُنَآ إِن كُنتَ مِنَ ٱلصَّٰدِقِينَ

Iwo adati: “Iwe wadza kuti ife tizingopembedza Mulungu yekha ndi kusiya milungu imene makolo athu adali kupembedza. Motero bweretsa chimene ukutiopseza nacho ngati zimene uli kunena ndi zoona.”

Ayah 70

قَالَ قَدۡ وَقَعَ عَلَيۡكُم مِّن رَّبِّكُمۡ رِجۡسࣱ وَغَضَبٌۖ أَتُجَٰدِلُونَنِي فِيٓ أَسۡمَآءࣲ سَمَّيۡتُمُوهَآ أَنتُمۡ وَءَابَآؤُكُم مَّا نَزَّلَ ٱللَّهُ بِهَا مِن سُلۡطَٰنࣲۚ فَٱنتَظِرُوٓاْ إِنِّي مَعَكُم مِّنَ ٱلۡمُنتَظِرِينَ

Iye adati: “Mkwiyo wa Ambuye wanu ndiponso chilango chake chadza kale pa inu. Kodi inu mukutsutsana ndi ine pa mayina amene inu ndi makolo anu mudapeka, opanda chilolezo cha Mulungu? Dikirani nanenso ndili mmodzi mwa odikira.”

Ayah 71

فَأَنجَيۡنَٰهُ وَٱلَّذِينَ مَعَهُۥ بِرَحۡمَةࣲ مِّنَّا وَقَطَعۡنَا دَابِرَ ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَاۖ وَمَا كَانُواْ مُؤۡمِنِينَ

Ife tidamupulumutsa iye ndi onse amene adali naye mwa chifundo chathu ndipo tidadula maziko ya onse amene anatsutsa chivumbulutso chathu ndipo iwo adali osakhulupirira

Ayah 72

وَإِلَىٰ ثَمُودَ أَخَاهُمۡ صَٰلِحࣰ اۚ قَالَ يَٰقَوۡمِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ مَا لَكُم مِّنۡ إِلَٰهٍ غَيۡرُهُۥۖ قَدۡ جَآءَتۡكُم بَيِّنَةࣱ مِّن رَّبِّكُمۡۖ هَٰذِهِۦ نَاقَةُ ٱللَّهِ لَكُمۡ ءَايَةࣰۖ فَذَرُوهَا تَأۡكُلۡ فِيٓ أَرۡضِ ٱللَّهِۖ وَلَا تَمَسُّوهَا بِسُوٓءࣲ فَيَأۡخُذَكُمۡ عَذَابٌ أَلِيمࣱ‏

Ndipo kwa anthu a Thamud, Ife tidawatumizira m’bale wawo Saleh. Iye adati: “Oh anthu anga! Pembedzani Mulungu. Inu mulibe mulungu wina koma Iye yekha. Ndithudi wadza umboni wokhulupirika kuchokera kwa Ambuye wanu. Iyi ndi Ngamira yaikazi ya Mulungu, chizindikiro kwa inu. Motero ilekeni kuti izidya m’dziko la Mulungu ndipo musaizunze ayi chifukwa mungapute chilango chowawa.”

Ayah 73

وَٱذۡكُرُوٓاْ إِذۡ جَعَلَكُمۡ خُلَفَآءَ مِنۢ بَعۡدِ عَادࣲ وَبَوَّأَكُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ تَتَّخِذُونَ مِن سُهُولِهَا قُصُورࣰ ا وَتَنۡحِتُونَ ٱلۡجِبَالَ بُيُوتࣰ اۖ فَٱذۡكُرُوٓاْ ءَالَآءَ ٱللَّهِ وَلَا تَعۡثَوۡاْ فِي ٱلۡأَرۡضِ مُفۡسِدِينَ

“Ndipo kumbukirani pamene Iye adakupangani inu kuti mukhale alowa m’malo a Ad, ndipo adakupatsani malo okhala m’dziko lino. Inu mwamanga nyumba zolemekezeka m’chidikha chake ndiponso mwaboola nyumba pakati pa mapiri ake. Motero kumbukirani zokoma za Mulungu ndipo musachulukitse kuwononga padziko lapansi.”

Ayah 74

قَالَ ٱلۡمَلَأُ ٱلَّذِينَ ٱسۡتَكۡبَرُواْ مِن قَوۡمِهِۦ لِلَّذِينَ ٱسۡتُضۡعِفُواْ لِمَنۡ ءَامَنَ مِنۡهُمۡ أَتَعۡلَمُونَ أَنَّ صَٰلِحࣰ ا مُّرۡسَلࣱ مِّن رَّبِّهِۦۚ قَالُوٓاْ إِنَّا بِمَآ أُرۡسِلَ بِهِۦ مُؤۡمِنُونَ

Atsogoleri a anthu amene amadzikweza mu anthu ake anati kwa anthu ofoka amene adakhulupirira mwa iwo: “Kodi mukudziwa kuti Saleh ndi wotumidwa kuchokera kwa Ambuye wake?” Iwo adati: “Ndithudi ife takhulupirira mzimene iye watumidwa.”

Ayah 75

قَالَ ٱلَّذِينَ ٱسۡتَكۡبَرُوٓاْ إِنَّا بِٱلَّذِيٓ ءَامَنتُم بِهِۦ كَٰفِرُونَ

Iwo amene adali odzikuza adati: “Ndithudi ife tili kuzikanazonsezimeneinumulikuzikhulupirira.”

Ayah 76

فَعَقَرُواْ ٱلنَّاقَةَ وَعَتَوۡاْ عَنۡ أَمۡرِ رَبِّهِمۡ وَقَالُواْ يَٰصَٰلِحُ ٱئۡتِنَا بِمَا تَعِدُنَآ إِن كُنتَ مِنَ ٱلۡمُرۡسَلِينَ

Motero iwo adapha ngamira yaikazi ija ndipo ananyoza lamulo la Ambuye wawo ndipo adati: “Iwe Saleh! Bweretsa chimene udatiopseza nacho ngati iwe ndiwe Mtumwi woona.”

Ayah 77

فَأَخَذَتۡهُمُ ٱلرَّجۡفَةُ فَأَصۡبَحُواْ فِي دَارِهِمۡ جَٰثِمِينَ

Motero nthawi yomweyo chivomerezi chidagwa pa iwo ndipo pamene kumacha m’mawa onse adali lambilambi m’nyumba zawo atafa

Ayah 78

فَتَوَلَّىٰ عَنۡهُمۡ وَقَالَ يَٰقَوۡمِ لَقَدۡ أَبۡلَغۡتُكُمۡ رِسَالَةَ رَبِّي وَنَصَحۡتُ لَكُمۡ وَلَٰكِن لَّا تُحِبُّونَ ٱلنَّٰصِحِينَ

Motero Saleh adachoka nati, “oh anthu anga! Ine, ndithudi, ndapereka uthenga wa Ambuye wanga ndipo ndakupatsani chilangizo chabwino koma inu simukonda anthu okuchenjezani.”

Ayah 79

وَلُوطًا إِذۡ قَالَ لِقَوۡمِهِۦٓ أَتَأۡتُونَ ٱلۡفَٰحِشَةَ مَا سَبَقَكُم بِهَا مِنۡ أَحَدࣲ مِّنَ ٱلۡعَٰلَمِينَ

Ndi pamene Loti adanena kwa anthu ake, “Kodi inu mukuchita zinthu zonyansa zimene palibe mtundu wa anthu umene udachitapo ndi kale lomwe?”

Ayah 80

إِنَّكُمۡ لَتَأۡتُونَ ٱلرِّجَالَ شَهۡوَةࣰ مِّن دُونِ ٱلنِّسَآءِۚ بَلۡ أَنتُمۡ قَوۡمࣱ مُّسۡرِفُونَ

“Ndithudi inu mufuna kukwaniritsa zilakolako za matupi anu ndi amuna anzanu m’malo mwa akazi? Iyayi, ndithudi, inu ndinu anthu ochimwa kwambiri.”

Ayah 81

وَمَا كَانَ جَوَابَ قَوۡمِهِۦٓ إِلَّآ أَن قَالُوٓاْ أَخۡرِجُوهُم مِّن قَرۡيَتِكُمۡۖ إِنَّهُمۡ أُنَاسࣱ يَتَطَهَّرُونَ

Ndipo yankho la anthu ake silinali lina koma adati: “Achotseni iwo mu Mzinda wanu. Awa ndi anthu amene afuna kukhala angwiro.”

Ayah 82

فَأَنجَيۡنَٰهُ وَأَهۡلَهُۥٓ إِلَّا ٱمۡرَأَتَهُۥ كَانَتۡ مِنَ ٱلۡغَٰبِرِينَ

Ndipo Ife tidamupulumutsa iye pamodzi ndi omutsatira ake kupatula mkazi wake amene adali mmodzi mwa otsalira m’mbuyo

Ayah 83

وَأَمۡطَرۡنَا عَلَيۡهِم مَّطَرࣰ اۖ فَٱنظُرۡ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلۡمُجۡرِمِينَ

Ndipo tidagwetsa pa iwo mvula yambiri. Onani mapeto a anthu ochita zoipa

Ayah 84

وَإِلَىٰ مَدۡيَنَ أَخَاهُمۡ شُعَيۡبࣰ اۚ قَالَ يَٰقَوۡمِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ مَا لَكُم مِّنۡ إِلَٰهٍ غَيۡرُهُۥۖ قَدۡ جَآءَتۡكُم بَيِّنَةࣱ مِّن رَّبِّكُمۡۖ فَأَوۡفُواْ ٱلۡكَيۡلَ وَٱلۡمِيزَانَ وَلَا تَبۡخَسُواْ ٱلنَّاسَ أَشۡيَآءَهُمۡ وَلَا تُفۡسِدُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ بَعۡدَ إِصۡلَٰحِهَاۚ ذَٰلِكُمۡ خَيۡرࣱ لَّكُمۡ إِن كُنتُم مُّؤۡمِنِينَ

Kwa anthu a ku Midiyani tidatumiza m’bale wawo Shaibu. Iye anati: “Oh anthu anga! Pembedzani Mulungu, inu mulibe mulungu wina koma Iye yekha. Ndithudi chizindikiro chooneka chadza kwa inu kuchokera kwa Ambuye wanu motero perekani muyeso woyenera ndipo yesani zonse moyenera ndipo musachite chinyengo kwa anthu pa katundu wawo ndipo musawononge dziko lapansi pambuyo poti layeretsedwa kale. Chimenecho ndicho chinthu chabwino kwa inu ngati inu ndinu okhulupirira kwenikweni.”

Ayah 85

وَلَا تَقۡعُدُواْ بِكُلِّ صِرَٰطࣲ تُوعِدُونَ وَتَصُدُّونَ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِ مَنۡ ءَامَنَ بِهِۦ وَتَبۡغُونَهَا عِوَجࣰ اۚ وَٱذۡكُرُوٓاْ إِذۡ كُنتُمۡ قَلِيلࣰ ا فَكَثَّرَكُمۡۖ وَٱنظُرُواْ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلۡمُفۡسِدِينَ

“Ndipo musakhale mu msewu uliwonse ndi kumaopseza anthu okhulupirira ndi kuwaletsa kutsatira njira ya Mulungu ndi kufunafuna njira yoti mukhotetsere njirayo. Kumbukirani mmene adakuchulukitsirani inu pamene mudali ochepa. Ndipo onani mmene adalili mapeto a anthu ochita zoipa.”

Ayah 86

وَإِن كَانَ طَآئِفَةࣱ مِّنكُمۡ ءَامَنُواْ بِٱلَّذِيٓ أُرۡسِلۡتُ بِهِۦ وَطَآئِفَةࣱ لَّمۡ يُؤۡمِنُواْ فَٱصۡبِرُواْ حَتَّىٰ يَحۡكُمَ ٱللَّهُ بَيۡنَنَاۚ وَهُوَ خَيۡرُ ٱلۡحَٰكِمِينَ

“Ndipo ngati lilipo gulu lina pakati panu limene lidakhulupirira mu Uthenga umene ndidatumizidwa ndi gulu limene silidakhulupirire motero pilira mpaka pamene Mulungu aweruza pakati pathu. Iye ndiye wabwino mwa oweruza onse.”

Ayah 87

۞قَالَ ٱلۡمَلَأُ ٱلَّذِينَ ٱسۡتَكۡبَرُواْ مِن قَوۡمِهِۦ لَنُخۡرِجَنَّكَ يَٰشُعَيۡبُ وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ مَعَكَ مِن قَرۡيَتِنَآ أَوۡ لَتَعُودُنَّ فِي مِلَّتِنَاۚ قَالَ أَوَلَوۡ كُنَّا كَٰرِهِينَ

Mafumu odzikweza a gulu lina la mtundu wake adati: “Iwe Shaibu! Ndithudi ife tidzakuthamangitsa iwe mu mzinda wathu pamodzi ndi iwo amene akhulupirira ndi iwe kapena kuti mubwerere ku chipembedzo chathu.” Iye adati: “Chiyani! Ngakhale kuti zikutinyansa?”

Ayah 88

قَدِ ٱفۡتَرَيۡنَا عَلَى ٱللَّهِ كَذِبًا إِنۡ عُدۡنَا فِي مِلَّتِكُم بَعۡدَ إِذۡ نَجَّىٰنَا ٱللَّهُ مِنۡهَاۚ وَمَا يَكُونُ لَنَآ أَن نَّعُودَ فِيهَآ إِلَّآ أَن يَشَآءَ ٱللَّهُ رَبُّنَاۚ وَسِعَ رَبُّنَا كُلَّ شَيۡءٍ عِلۡمًاۚ عَلَى ٱللَّهِ تَوَكَّلۡنَاۚ رَبَّنَا ٱفۡتَحۡ بَيۡنَنَا وَبَيۡنَ قَوۡمِنَا بِٱلۡحَقِّ وَأَنتَ خَيۡرُ ٱلۡفَٰتِحِينَ

“Ndithudi ife timpekera Mulungu bodza ngati tibwerera ku chipembedzo chanu pamene Mulungu watipulumutsa ife ku icho. Ndipo ife sitikadatha mwa njira iliyonse kubwerera ku icho pokhapokha ndi chifuniro cha Mulungu. Ambuye wathu amadziwa chili chonse. Mwa Mulungu ife taika chikhulupiriro chathu. Ambuye wathu! Weruzani pakati pa ife ndi anthu athu mwachoonadi chifukwa Inu ndinu wodziwa kuweruza.”

Ayah 89

وَقَالَ ٱلۡمَلَأُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ مِن قَوۡمِهِۦ لَئِنِ ٱتَّبَعۡتُمۡ شُعَيۡبًا إِنَّكُمۡ إِذࣰ ا لَّخَٰسِرُونَ

Ndipo mafumu a iwo amene sadakhulupirire a mtundu wa Shaibu adati: “Ngati inu mutsatira Shaibu ndithudi, mudzakhala olephera pa zochita zanu.”

Ayah 90

فَأَخَذَتۡهُمُ ٱلرَّجۡفَةُ فَأَصۡبَحُواْ فِي دَارِهِمۡ جَٰثِمِينَ

Ndipo nthawi yomweyo chivomerezi chidagwa pa iwo ndipo onse adali lambilambi m’nyumba zawo

Ayah 91

ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ شُعَيۡبࣰ ا كَأَن لَّمۡ يَغۡنَوۡاْ فِيهَاۚ ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ شُعَيۡبࣰ ا كَانُواْ هُمُ ٱلۡخَٰسِرِينَ

onse amene adatsutsa Shaibu adakhala ngati sadakhalenso malo amenewa. onse amene sadakhulupirire mwa Shaibu adali otaika

Ayah 92

فَتَوَلَّىٰ عَنۡهُمۡ وَقَالَ يَٰقَوۡمِ لَقَدۡ أَبۡلَغۡتُكُمۡ رِسَٰلَٰتِ رَبِّي وَنَصَحۡتُ لَكُمۡۖ فَكَيۡفَ ءَاسَىٰ عَلَىٰ قَوۡمࣲ كَٰفِرِينَ

Motero Shaibu adawasiya iwo nati: “Oh inu anthu anga! Ndithudi ine ndidakuuzani uthenga wa Ambuye wanga ndipo ndakupatsani ulangizi wabwino. Kodi ine ndingamvere bwanji chisoni anthu osakhulupirira?”

Ayah 93

وَمَآ أَرۡسَلۡنَا فِي قَرۡيَةࣲ مِّن نَّبِيٍّ إِلَّآ أَخَذۡنَآ أَهۡلَهَا بِٱلۡبَأۡسَآءِ وَٱلضَّرَّآءِ لَعَلَّهُمۡ يَضَّرَّعُونَ

Ndipo Ife sitimatumiza Mtumwi ku mzinda wina uli wonse koma timagwetsa pa anthu ake umphawi, matenda ndi matsoka kuti akhoza kudzichepetsa

Ayah 94

ثُمَّ بَدَّلۡنَا مَكَانَ ٱلسَّيِّئَةِ ٱلۡحَسَنَةَ حَتَّىٰ عَفَواْ وَّقَالُواْ قَدۡ مَسَّ ءَابَآءَنَا ٱلضَّرَّآءُ وَٱلسَّرَّآءُ فَأَخَذۡنَٰهُم بَغۡتَةࣰ وَهُمۡ لَا يَشۡعُرُونَ

Ndipo tidasanduliza matsoka kukhala mwayi mpaka pamene iwo adachuluka ndikukhala ndi chuma ndipo adayamba kunena kuti: “Makolo athu nawonso adali kuona zosangalatsa ndiponso mavuto.” Ndipo Ife tidawapatsa chilango mwadzidzidzi pamene iwo sadali kudziwa

Ayah 95

وَلَوۡ أَنَّ أَهۡلَ ٱلۡقُرَىٰٓ ءَامَنُواْ وَٱتَّقَوۡاْ لَفَتَحۡنَا عَلَيۡهِم بَرَكَٰتࣲ مِّنَ ٱلسَّمَآءِ وَٱلۡأَرۡضِ وَلَٰكِن كَذَّبُواْ فَأَخَذۡنَٰهُم بِمَا كَانُواْ يَكۡسِبُونَ

Ndipo anthu a m’Mizinda imeneyi akadakhulupirira ndi kuopa uchimo, tikadawatsegulira madalitso kuchokera kumwamba ndi padziko lapansi. Koma iwo adakana choonadi. Motero Ife tidawalanga chifukwa cha zimene adali kuchita

Ayah 96

أَفَأَمِنَ أَهۡلُ ٱلۡقُرَىٰٓ أَن يَأۡتِيَهُم بَأۡسُنَا بَيَٰتࣰ ا وَهُمۡ نَآئِمُونَ

Kodi anthu a m’mizinda amaganiza kuti adali wotetezedwa ku chilango chathu ngati chikanadza kwa iwo nthawi ya usiku pamene iwo adali kugona

Ayah 97

أَوَأَمِنَ أَهۡلُ ٱلۡقُرَىٰٓ أَن يَأۡتِيَهُم بَأۡسُنَا ضُحࣰ ى وَهُمۡ يَلۡعَبُونَ

Kapena anthu a m’Mizinda amaganiza kuti anali otetezedwa ku chilango chathu chimene chingadze kwa iwo masana pamene ali kusewera

Ayah 98

أَفَأَمِنُواْ مَكۡرَ ٱللَّهِۚ فَلَا يَأۡمَنُ مَكۡرَ ٱللَّهِ إِلَّا ٱلۡقَوۡمُ ٱلۡخَٰسِرُونَ

Kodi iwo amaganiza kuti ndi otetezedwa ku chiweruzo cha Mulungu? Palibe amene angaganize kuti ndiotetezedwa kuchilango cha Mulungu, kupatula anthu otayika

Ayah 99

أَوَلَمۡ يَهۡدِ لِلَّذِينَ يَرِثُونَ ٱلۡأَرۡضَ مِنۢ بَعۡدِ أَهۡلِهَآ أَن لَّوۡ نَشَآءُ أَصَبۡنَٰهُم بِذُنُوبِهِمۡۚ وَنَطۡبَعُ عَلَىٰ قُلُوبِهِمۡ فَهُمۡ لَا يَسۡمَعُونَ

Kodi m’badwo uno, umene wadza pambuyo pa wina, siuzindikira kuti ngati Ife titafuna, tikhoza kuulanga chifukwa cha machimo awo? Ndipo timaika chimatiro m’mitima mwawo kuti asamve

Ayah 100

تِلۡكَ ٱلۡقُرَىٰ نَقُصُّ عَلَيۡكَ مِنۡ أَنۢبَآئِهَاۚ وَلَقَدۡ جَآءَتۡهُمۡ رُسُلُهُم بِٱلۡبَيِّنَٰتِ فَمَا كَانُواْ لِيُؤۡمِنُواْ بِمَا كَذَّبُواْ مِن قَبۡلُۚ كَذَٰلِكَ يَطۡبَعُ ٱللَّهُ عَلَىٰ قُلُوبِ ٱلۡكَٰفِرِينَ

Imeneyo ndi mizinda imene nkhani zake tili kukuuza iwe. Ndithudi kudadza kwa iwo Atumwi awo ndi zizindikiro zooneka. Koma iwo sadakhulupirire zimene adazikana kale. Kotero Mulungu amamata mitima ya anthu osakhulupirira

Ayah 101

وَمَا وَجَدۡنَا لِأَكۡثَرِهِم مِّنۡ عَهۡدࣲۖ وَإِن وَجَدۡنَآ أَكۡثَرَهُمۡ لَفَٰسِقِينَ

Ife sitidaone ambiri mwa iwo amene adasunga malonjezo koma Ife tidawapeza, ndithudi, ambiri a iwo ali anthu ochita zoipa

Ayah 102

ثُمَّ بَعَثۡنَا مِنۢ بَعۡدِهِم مُّوسَىٰ بِـَٔايَٰتِنَآ إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ وَمَلَإِيْهِۦ فَظَلَمُواْ بِهَاۖ فَٱنظُرۡ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلۡمُفۡسِدِينَ

Atapita awa, Ife tidatumiza Mose ndi zizindikiro zathu kwa Farao ndi mafumu ake koma iwo adazikana. Motero taona mapeto a anthu ochita zoipa

Ayah 103

وَقَالَ مُوسَىٰ يَٰفِرۡعَوۡنُ إِنِّي رَسُولࣱ مِّن رَّبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ

Ndipo Mose adati: “oh Farao! Ine ndine Mtumwi wochokera kwa Ambuye wazolengedwa zonse

Ayah 104

حَقِيقٌ عَلَىٰٓ أَن لَّآ أَقُولَ عَلَى ٱللَّهِ إِلَّا ٱلۡحَقَّۚ قَدۡ جِئۡتُكُم بِبَيِّنَةࣲ مِّن رَّبِّكُمۡ فَأَرۡسِلۡ مَعِيَ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ

Ndithudi ine sindidzanena china chilichonse chokhudza Mulungu kupatula choonadi. Ndithudi ine ndakubweretserani chizindikiro chosakaikitsa kuchokera kwa Ambuye wanu. Motero alole ana a Israyeli kuti apite ndi ine.”

Ayah 105

قَالَ إِن كُنتَ جِئۡتَ بِـَٔايَةࣲ فَأۡتِ بِهَآ إِن كُنتَ مِنَ ٱلصَّٰدِقِينَ

Farao adati: “Ngati wabwera ndi chizindikiro, chionetse msanga ngati uli kunena zoona.”

Ayah 106

فَأَلۡقَىٰ عَصَاهُ فَإِذَا هِيَ ثُعۡبَانࣱ مُّبِينࣱ‏

Ndipo Mose adaponya pansi ndodo yake ndipo nthawi yomweyo idasanduka njoka yeniyeni

Ayah 107

وَنَزَعَ يَدَهُۥ فَإِذَا هِيَ بَيۡضَآءُ لِلنَّٰظِرِينَ

Ndipo iye adatulutsa dzanja lake ndipo nthawi yomweyo lidasanduka loyera kwa iwo amene adaliona

Ayah 108

قَالَ ٱلۡمَلَأُ مِن قَوۡمِ فِرۡعَوۡنَ إِنَّ هَٰذَا لَسَٰحِرٌ عَلِيمࣱ‏

Mafumu a anthu a Farao adati: “Ndithudi munthu uyu ndi wodziwa matsenga kwambiri

Ayah 109

يُرِيدُ أَن يُخۡرِجَكُم مِّنۡ أَرۡضِكُمۡۖ فَمَاذَا تَأۡمُرُونَ

Iye akufuna kukutulutsani inu mu dziko lanu, nanga inu mukuti bwanji?”

Ayah 110

قَالُوٓاْ أَرۡجِهۡ وَأَخَاهُ وَأَرۡسِلۡ فِي ٱلۡمَدَآئِنِ حَٰشِرِينَ

Iwo adati: “Bamusungani pa kanthawi, iye pamodzi ndi m’bale wake ndipo tumizani anthu ku mizinda kuti akasonkhanitse.”

Ayah 111

يَأۡتُوكَ بِكُلِّ سَٰحِرٍ عَلِيمࣲ‏

Ndipo kuti abweretse kwa iwe onse odziwa matsenga.”

Ayah 112

وَجَآءَ ٱلسَّحَرَةُ فِرۡعَوۡنَ قَالُوٓاْ إِنَّ لَنَا لَأَجۡرًا إِن كُنَّا نَحۡنُ ٱلۡغَٰلِبِينَ

Ndipo anthu a matsenga adadza kwa Farao. Iwo adati: “Ndithudi ife tidzapeza malipiro abwino ngati ife tipambana.”

Ayah 113

قَالَ نَعَمۡ وَإِنَّكُمۡ لَمِنَ ٱلۡمُقَرَّبِينَ

Iye adati: “Inde ndipo inu mudzakhala pafupi ndi ine.”

Ayah 114

قَالُواْ يَٰمُوسَىٰٓ إِمَّآ أَن تُلۡقِيَ وَإِمَّآ أَن نَّكُونَ نَحۡنُ ٱلۡمُلۡقِينَ

Iwo adati: “oh iwe Mose! Kapena uyambe ndiwe kuponya ndodo yako kapena tiyambe ndife?”

Ayah 115

قَالَ أَلۡقُواْۖ فَلَمَّآ أَلۡقَوۡاْ سَحَرُوٓاْ أَعۡيُنَ ٱلنَّاسِ وَٱسۡتَرۡهَبُوهُمۡ وَجَآءُو بِسِحۡرٍ عَظِيمࣲ‏

Iye adati: “Yambani ndinu.” Ndipo pamene iwo adaponya, iwo adalodza maso a anthu ndi kuwachititsa mantha ndipo adaonetsa matsenga akulu

Ayah 116

۞وَأَوۡحَيۡنَآ إِلَىٰ مُوسَىٰٓ أَنۡ أَلۡقِ عَصَاكَۖ فَإِذَا هِيَ تَلۡقَفُ مَا يَأۡفِكُونَ

Ndipo ife tidati kwa Mose: “Tsopano ponya pansi ndodo yako.” Ndipo nthawi yomweyo ndodo yake idameza zonse za matsenga zimene iwo amaonetsa

Ayah 117

فَوَقَعَ ٱلۡحَقُّ وَبَطَلَ مَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ

Motero choonadi chidakhazikitsidwa ndipo zochita zawo zidakhala zopanda pake

Ayah 118

فَغُلِبُواْ هُنَالِكَ وَٱنقَلَبُواْ صَٰغِرِينَ

Motero iwo adagonjetsedwa nthawi yomweyo ndipo anachititsidwa manyazi

Ayah 119

وَأُلۡقِيَ ٱلسَّحَرَةُ سَٰجِدِينَ

Ndipo anthu a matsenga onse adagwetsa mphumi zawo pansi ndi kulambira

Ayah 120

قَالُوٓاْ ءَامَنَّا بِرَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ

Iwo adati, “Ife takhulupirira mwa Ambuye wa zolengedwa zonse.”

Ayah 121

رَبِّ مُوسَىٰ وَهَٰرُونَ

“Ambuye wa Mose ndi Aroni.”

Ayah 122

قَالَ فِرۡعَوۡنُ ءَامَنتُم بِهِۦ قَبۡلَ أَنۡ ءَاذَنَ لَكُمۡۖ إِنَّ هَٰذَا لَمَكۡرࣱ مَّكَرۡتُمُوهُ فِي ٱلۡمَدِينَةِ لِتُخۡرِجُواْ مِنۡهَآ أَهۡلَهَاۖ فَسَوۡفَ تَعۡلَمُونَ

Ndipo Farao adati, “Kodi inu mwakhulupirira mwa iye popanda chilolezo changa? Ndithudi chimenechi ndi chiwembu chimene inu mwakonza mu mzinda ndi cholinga chotulutsa anthu ake koma posachedwapa mudzadziwa.”

Ayah 123

لَأُقَطِّعَنَّ أَيۡدِيَكُمۡ وَأَرۡجُلَكُم مِّنۡ خِلَٰفࣲ ثُمَّ لَأُصَلِّبَنَّكُمۡ أَجۡمَعِينَ

“Ndithudi ine ndidzadula manja anu ndi mapazi anu mosiyanitsa ndipo ndidzakupachikani nonse.”

Ayah 124

قَالُوٓاْ إِنَّآ إِلَىٰ رَبِّنَا مُنقَلِبُونَ

Iwo adamuyankha: “Ndithudi ife tili kubwerera kwa Ambuye wathu.”

Ayah 125

وَمَا تَنقِمُ مِنَّآ إِلَّآ أَنۡ ءَامَنَّا بِـَٔايَٰتِ رَبِّنَا لَمَّا جَآءَتۡنَاۚ رَبَّنَآ أَفۡرِغۡ عَلَيۡنَا صَبۡرࣰ ا وَتَوَفَّنَا مُسۡلِمِينَ

“Ndipo inu mufuna kubwezera kwa ife chifukwa cha kuti takhulupirira mu zizindikiro za Ambuye wathu pamene zalangizidwa kwa ife! Ambuye wathu! Tipatseni kupirira ndipo konzani kuti ife tife ngati Asilamu.”

Ayah 126

وَقَالَ ٱلۡمَلَأُ مِن قَوۡمِ فِرۡعَوۡنَ أَتَذَرُ مُوسَىٰ وَقَوۡمَهُۥ لِيُفۡسِدُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَيَذَرَكَ وَءَالِهَتَكَۚ قَالَ سَنُقَتِّلُ أَبۡنَآءَهُمۡ وَنَسۡتَحۡيِۦ نِسَآءَهُمۡ وَإِنَّا فَوۡقَهُمۡ قَٰهِرُونَ

Mafumu a anthu a Farao adati: “Kodi inu mukumusiya Mose ndi anthu ake kuti azichita zoipa m’dziko ndi kukusiya iwe ndi milungu yako?” Iye adayankha, “Ife tidzapha ana awo amuna ndi kusiya ana awo akazi ndi moyo ndipo Ife ndithudi tili ndi mphamvu pa iwo.”

Ayah 127

قَالَ مُوسَىٰ لِقَوۡمِهِ ٱسۡتَعِينُواْ بِٱللَّهِ وَٱصۡبِرُوٓاْۖ إِنَّ ٱلۡأَرۡضَ لِلَّهِ يُورِثُهَا مَن يَشَآءُ مِنۡ عِبَادِهِۦۖ وَٱلۡعَٰقِبَةُ لِلۡمُتَّقِينَ

Mose adawauza anthu ake kuti, “Pemphani thandizo kwa Mulungu ndipo mupirire. Ndithudi Mwini wake wa dziko lino ndi Mulungu. Iye amalipereka ngati mokhalamo kwa iwo, akapolo ake, amene Iye wawasankha ndipo mapeto abwino adzakhala kwa anthu angwiro.”

Ayah 128

قَالُوٓاْ أُوذِينَا مِن قَبۡلِ أَن تَأۡتِيَنَا وَمِنۢ بَعۡدِ مَا جِئۡتَنَاۚ قَالَ عَسَىٰ رَبُّكُمۡ أَن يُهۡلِكَ عَدُوَّكُمۡ وَيَسۡتَخۡلِفَكُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ فَيَنظُرَ كَيۡفَ تَعۡمَلُونَ

Iwo adati, “Ife tidali kuzunzidwa iwe usadadze kwa ife ndipo tikuzunzidwabe pamene iwe wadza.” Iye adati: “Mwina Ambuye wanu akhoza kuwononga adani anu ndi kukupangani inu kukhala olamulira m’dziko kuti Iye aone mmene muzidzachitira.”

Ayah 129

وَلَقَدۡ أَخَذۡنَآ ءَالَ فِرۡعَوۡنَ بِٱلسِّنِينَ وَنَقۡصࣲ مِّنَ ٱلثَّمَرَٰتِ لَعَلَّهُمۡ يَذَّكَّرُونَ

Ndithudi Ife tidawalanga anthu a Farao ndi chilala cha zaka zambiri ndi kuchepa kwa zipatso kuti mwina akhoza kukumbuka

Ayah 130

فَإِذَا جَآءَتۡهُمُ ٱلۡحَسَنَةُ قَالُواْ لَنَا هَٰذِهِۦۖ وَإِن تُصِبۡهُمۡ سَيِّئَةࣱ يَطَّيَّرُواْ بِمُوسَىٰ وَمَن مَّعَهُۥٓۗ أَلَآ إِنَّمَا طَٰٓئِرُهُمۡ عِندَ ٱللَّهِ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَهُمۡ لَا يَعۡلَمُونَ

Koma pamene zabwino zinali kudza kwa iwo, iwo amati: “Zimenezi ndi zotiyenera.” Koma ngati choipa chimadza pa iwo, adali kunena kuti chadza chifukwa cha Mose ndi anthu ake. Dziwani! Ndithudi zoipa zawo zimachokera kwa Mulungu koma ambiri a iwo sadziwa

Ayah 131

وَقَالُواْ مَهۡمَا تَأۡتِنَا بِهِۦ مِنۡ ءَايَةࣲ لِّتَسۡحَرَنَا بِهَا فَمَا نَحۡنُ لَكَ بِمُؤۡمِنِينَ

Iwo adati: “Zodabwitsa zina zilizonse zimene ungabweretse ndi cholinga chotizunguza ife sitidzakukhulupirira ayi.”

Ayah 132

فَأَرۡسَلۡنَا عَلَيۡهِمُ ٱلطُّوفَانَ وَٱلۡجَرَادَ وَٱلۡقُمَّلَ وَٱلضَّفَادِعَ وَٱلدَّمَ ءَايَٰتࣲ مُّفَصَّلَٰتࣲ فَٱسۡتَكۡبَرُواْ وَكَانُواْ قَوۡمࣰ ا مُّجۡرِمِينَ

Motero ife tidawatumizira chigumula ndi dzombe, nsabwe, achule, ndi magazi kukhala zizindikiro zoonadi zosiyanasiyana zooneka komabe iwo adazikana izo chifukwa chakuti adali anthu ochimwa

Ayah 133

وَلَمَّا وَقَعَ عَلَيۡهِمُ ٱلرِّجۡزُ قَالُواْ يَٰمُوسَى ٱدۡعُ لَنَا رَبَّكَ بِمَا عَهِدَ عِندَكَۖ لَئِن كَشَفۡتَ عَنَّا ٱلرِّجۡزَ لَنُؤۡمِنَنَّ لَكَ وَلَنُرۡسِلَنَّ مَعَكَ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ

Ndipo pamene mlili unali kudza pa iwo, iwo amati: “Oh Mose! Chonde, pempha kwa Ambuye wako, m’malo mwathu, chifukwa cha lonjezo lake kwa iwe. Ngati iwe utichotsera mliliwu, ndithudi, ife tidzakhulupirira mwa iwe ndipo tidzawalola ana a Israyeli kuti apite nawe.”

Ayah 134

فَلَمَّا كَشَفۡنَا عَنۡهُمُ ٱلرِّجۡزَ إِلَىٰٓ أَجَلٍ هُم بَٰلِغُوهُ إِذَا هُمۡ يَنكُثُونَ

Koma pamene Ife tidachotsa mlili pa iwo mpaka nthawi yokhazikika, imene adzaifika, taona! Iwo adaphwanya lonjezo

Ayah 135

فَٱنتَقَمۡنَا مِنۡهُمۡ فَأَغۡرَقۡنَٰهُمۡ فِي ٱلۡيَمِّ بِأَنَّهُمۡ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا وَكَانُواْ عَنۡهَا غَٰفِلِينَ

Motero ife tidawabwezera chipongwe chawo. Ndipo tidawamiza m’nyanja chifukwa chakuti iwo adakana zizindikiro zathu ndipo sadafune kulabadira

Ayah 136

وَأَوۡرَثۡنَا ٱلۡقَوۡمَ ٱلَّذِينَ كَانُواْ يُسۡتَضۡعَفُونَ مَشَٰرِقَ ٱلۡأَرۡضِ وَمَغَٰرِبَهَا ٱلَّتِي بَٰرَكۡنَا فِيهَاۖ وَتَمَّتۡ كَلِمَتُ رَبِّكَ ٱلۡحُسۡنَىٰ عَلَىٰ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ بِمَا صَبَرُواْۖ وَدَمَّرۡنَا مَا كَانَ يَصۡنَعُ فِرۡعَوۡنُ وَقَوۡمُهُۥ وَمَا كَانُواْ يَعۡرِشُونَ

Ndipo Ife tidawapatsa anthu amene amati ndi ofooka ulamuliro wa maiko a ku m’mawa ndi ku madzulo, amene tidawadalitsa. Ndipo Mau olemekezeka Ambuye wako kwa ana a Israyeli, adakwaniritsidwa chifukwa cha kupirira kwawo. Ndipo Ife tidaononga zinthu zonse zomwe Farao ndi anthu ake adapanga ndi zimene anali kumanga

Ayah 137

وَجَٰوَزۡنَا بِبَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ ٱلۡبَحۡرَ فَأَتَوۡاْ عَلَىٰ قَوۡمࣲ يَعۡكُفُونَ عَلَىٰٓ أَصۡنَامࣲ لَّهُمۡۚ قَالُواْ يَٰمُوسَى ٱجۡعَل لَّنَآ إِلَٰهࣰ ا كَمَا لَهُمۡ ءَالِهَةࣱۚ قَالَ إِنَّكُمۡ قَوۡمࣱ تَجۡهَلُونَ

Ndipo Ife tidawatsogolera ana a Israyeli powoloka nyanja ndipo iwo adapeza anthu omwe anali kupembedza mafano awo. Iwo adati, “Mose tipangire ife mulungu wolingana ndi milungu yawo.” Mose anayankha: “Ndithudi inu ndinu anthu osadziwa.”

Ayah 138

إِنَّ هَٰٓؤُلَآءِ مُتَبَّرࣱ مَّا هُمۡ فِيهِ وَبَٰطِلࣱ مَّا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ

Ndithudi anthu awa adzawonongeka chifukwa chopembedza mafano. Ndipo ntchito zawo zonse ndi zopanda pake

Ayah 139

قَالَ أَغَيۡرَ ٱللَّهِ أَبۡغِيكُمۡ إِلَٰهࣰ ا وَهُوَ فَضَّلَكُمۡ عَلَى ٱلۡعَٰلَمِينَ

Iye anati: “Kodi ndikufunireni mulungu wina kupatula Mulungu weniweni pamene Iye wakulemekezani inu kuposa mitundu yonse.”

Ayah 140

وَإِذۡ أَنجَيۡنَٰكُم مِّنۡ ءَالِ فِرۡعَوۡنَ يَسُومُونَكُمۡ سُوٓءَ ٱلۡعَذَابِ يُقَتِّلُونَ أَبۡنَآءَكُمۡ وَيَسۡتَحۡيُونَ نِسَآءَكُمۡۚ وَفِي ذَٰلِكُم بَلَآءࣱ مِّن رَّبِّكُمۡ عَظِيمࣱ‏

Ndi pamene Ife tidakupulumutsani inu kwa anthu a Farao, amene adali kukuzunzani kwambiri, kupha ana anu amuna ndi kusiya ana anu akazi a moyo. Ndipo mmenemo munali mayesero akulu ochokera kwa Ambuye wanu

Ayah 141

۞وَوَٰعَدۡنَا مُوسَىٰ ثَلَٰثِينَ لَيۡلَةࣰ وَأَتۡمَمۡنَٰهَا بِعَشۡرࣲ فَتَمَّ مِيقَٰتُ رَبِّهِۦٓ أَرۡبَعِينَ لَيۡلَةࣰۚ وَقَالَ مُوسَىٰ لِأَخِيهِ هَٰرُونَ ٱخۡلُفۡنِي فِي قَوۡمِي وَأَصۡلِحۡ وَلَا تَتَّبِعۡ سَبِيلَ ٱلۡمُفۡسِدِينَ

Ife tidamusankhira Mose masiku makumi atatu ndipo tinaonjeza masiku khumi ena, motero iye adakwaniritsa nthawi imene adasankhidwa ndi Ambuye wake ya masiku makumi anayi ndipo Mose anamuuza m’bale wake Aroni kuti: Lowa m’malo mwanga pakati pa anthu anga. Uchite zinthu za ngwiro ndipo usatsatire njira ya anthu ochita zoipa

Ayah 142

وَلَمَّا جَآءَ مُوسَىٰ لِمِيقَٰتِنَا وَكَلَّمَهُۥ رَبُّهُۥ قَالَ رَبِّ أَرِنِيٓ أَنظُرۡ إِلَيۡكَۚ قَالَ لَن تَرَىٰنِي وَلَٰكِنِ ٱنظُرۡ إِلَى ٱلۡجَبَلِ فَإِنِ ٱسۡتَقَرَّ مَكَانَهُۥ فَسَوۡفَ تَرَىٰنِيۚ فَلَمَّا تَجَلَّىٰ رَبُّهُۥ لِلۡجَبَلِ جَعَلَهُۥ دَكࣰّ ا وَخَرَّ مُوسَىٰ صَعِقࣰ اۚ فَلَمَّآ أَفَاقَ قَالَ سُبۡحَٰنَكَ تُبۡتُ إِلَيۡكَ وَأَنَا۠ أَوَّلُ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ

Ndipo pamene Mose adabwera panthawi ndi malo osankhidwa ndi Ife, Ambuye wake adalankhula naye ndipo iye adati: “Oh Ambuye wanga! Dzionetseni inu kwa ine kuti ndikuoneni.” Mulungu adati: “Iwe siudzandiona Ine ayi. Koma uone kuphiri ndipo ngati ilo lingakhalebe chikhalire ndiye kuti ukhoza kundiona Ine.” Ndipo pamene Ambuye wake anadzionetsera pa phiri, phiri lidaphwanyika ndi kusanduka fumbi lokhalokha ndipo Mose adagwa pansi ndipo adakomoka koma pamene anatsitsimuka iye adati: “Ulemerero ukhale kwa Inu. Ine ndalapa kwa Inu ndipo ine ndine woyamba wa anthu okhulupirira.”

Ayah 143

قَالَ يَٰمُوسَىٰٓ إِنِّي ٱصۡطَفَيۡتُكَ عَلَى ٱلنَّاسِ بِرِسَٰلَٰتِي وَبِكَلَٰمِي فَخُذۡ مَآ ءَاتَيۡتُكَ وَكُن مِّنَ ٱلشَّٰكِرِينَ

Mulungu adati: “oh iwe Mose! Ine ndakusankha iwe kukhala wapamwamba pakati pa anthu a mitundu yonse polankhula nawe. Motero gwiritsa zimene takupatsa ndipo khala othokoza.”

Ayah 144

وَكَتَبۡنَا لَهُۥ فِي ٱلۡأَلۡوَاحِ مِن كُلِّ شَيۡءࣲ مَّوۡعِظَةࣰ وَتَفۡصِيلࣰ ا لِّكُلِّ شَيۡءࣲ فَخُذۡهَا بِقُوَّةࣲ وَأۡمُرۡ قَوۡمَكَ يَأۡخُذُواْ بِأَحۡسَنِهَاۚ سَأُوْرِيكُمۡ دَارَ ٱلۡفَٰسِقِينَ

Ndipo tidamulembera iye, pa matabwa, malamulo osiyanasiyana ndi malangizo okhudza zinthu zonse ndipo tidati kwa iye, “Gwiritsa malamulo awa mwamphamvu ndiponso lamulira anthu ako kuti awatsatire bwinobwino. Ine ndidzakuonetsa midzi ya anthu oswa malamulo.”

Ayah 145

سَأَصۡرِفُ عَنۡ ءَايَٰتِيَ ٱلَّذِينَ يَتَكَبَّرُونَ فِي ٱلۡأَرۡضِ بِغَيۡرِ ٱلۡحَقِّ وَإِن يَرَوۡاْ كُلَّ ءَايَةࣲ لَّا يُؤۡمِنُواْ بِهَا وَإِن يَرَوۡاْ سَبِيلَ ٱلرُّشۡدِ لَا يَتَّخِذُوهُ سَبِيلࣰ ا وَإِن يَرَوۡاْ سَبِيلَ ٱلۡغَيِّ يَتَّخِذُوهُ سَبِيلࣰ اۚ ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمۡ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا وَكَانُواْ عَنۡهَا غَٰفِلِينَ

Ine ndidzawabisila zizindikiro zanga anthu a odzikweza ndi ochita zoipa mopanda chilungamo padziko ngakhale kuti iwo ataona chizindikiro china chilichonse, sadzachikhulupirira. Ngati aona njira yoyenera, iwo sadzaitsata, koma akaona njira yopotoka, iwo adzaitsatira iyo; chifukwa chakuti iwo adakana zizindikiro zathu ndipo sadafune kuzimvera ayi

Ayah 146

وَٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا وَلِقَآءِ ٱلۡأٓخِرَةِ حَبِطَتۡ أَعۡمَٰلُهُمۡۚ هَلۡ يُجۡزَوۡنَ إِلَّا مَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ

Iwo amene akana zizindikiro zathu ndi kukumana kwa patsiku la chiweruzo ntchito zawo ndi zopanda pake. Kodi iwo amayembekeza kuti adzalipidwa kuposa zimene amachita

Ayah 147

وَٱتَّخَذَ قَوۡمُ مُوسَىٰ مِنۢ بَعۡدِهِۦ مِنۡ حُلِيِّهِمۡ عِجۡلࣰ ا جَسَدࣰ ا لَّهُۥ خُوَارٌۚ أَلَمۡ يَرَوۡاْ أَنَّهُۥ لَا يُكَلِّمُهُمۡ وَلَا يَهۡدِيهِمۡ سَبِيلًاۘ ٱتَّخَذُوهُ وَكَانُواْ ظَٰلِمِينَ

Ndipo anthu ake a Mose adaumba, iye atachoka, kuchokera ku mphete ndi ndolo zawo, chifanizo cha mwana wa ng’ombe amene adali ndi mawu. Kodi iwo sadathe kuona kuti iyo siinathe kuwalankhula kapena kuwalondolera njira? Iwo adaipembedza iyo, kotero adalakwa

Ayah 148

وَلَمَّا سُقِطَ فِيٓ أَيۡدِيهِمۡ وَرَأَوۡاْ أَنَّهُمۡ قَدۡ ضَلُّواْ قَالُواْ لَئِن لَّمۡ يَرۡحَمۡنَا رَبُّنَا وَيَغۡفِرۡ لَنَا لَنَكُونَنَّ مِنَ ٱلۡخَٰسِرِينَ

Koma pamene iwo adazindikira ndi kuona kuti adalakwa, iwo adati: “Ngati Ambuye wathu sakhala ndi chifundo ndi ife ndi kutikhululukira, ndithudi, ife tidzakhala anthu otayika.”

Ayah 149

وَلَمَّا رَجَعَ مُوسَىٰٓ إِلَىٰ قَوۡمِهِۦ غَضۡبَٰنَ أَسِفࣰ ا قَالَ بِئۡسَمَا خَلَفۡتُمُونِي مِنۢ بَعۡدِيٓۖ أَعَجِلۡتُمۡ أَمۡرَ رَبِّكُمۡۖ وَأَلۡقَى ٱلۡأَلۡوَاحَ وَأَخَذَ بِرَأۡسِ أَخِيهِ يَجُرُّهُۥٓ إِلَيۡهِۚ قَالَ ٱبۡنَ أُمَّ إِنَّ ٱلۡقَوۡمَ ٱسۡتَضۡعَفُونِي وَكَادُواْ يَقۡتُلُونَنِي فَلَا تُشۡمِتۡ بِيَ ٱلۡأَعۡدَآءَ وَلَا تَجۡعَلۡنِي مَعَ ٱلۡقَوۡمِ ٱلظَّٰلِمِينَ

Ndipo pamene Mose adabwerera kwa anthu ake, wokwiya ndi wachisoni, iye adati: “Kodi ndi chinthu choipa bwanji chimene mwachita pamene ine kudalibe! Kodi inu munafulumira ndi kusiya kupembedza Ambuye wanu?” Ndipo iye adaponya pansi matabwa a malamulo, nagwira mutu wa m’bale wake ndi kumukokera kwa iye. Aroni adati: “Iwe mwana wa Amayi anga! Ndithu anthu awa adandiposa mphamvu ndipo adakhala pang’ono kundipha ndipo usalole kuti adani anga asangalale pa ine ndipo usandiike pa gulu la anthu ochita zoipa.”

Ayah 150

قَالَ رَبِّ ٱغۡفِرۡ لِي وَلِأَخِي وَأَدۡخِلۡنَا فِي رَحۡمَتِكَۖ وَأَنتَ أَرۡحَمُ ٱلرَّٰحِمِينَ

Mose adati: “Ambuye wanga! Ndikhululukireni ine pamodzi ndi m’bale wanga ndipo tilowetseni m’chisoni chanu chifukwa Inu ndinu oonetsa chisoni kwambiri kuposa onse omwe amaonetsa chisoni.”

Ayah 151

إِنَّ ٱلَّذِينَ ٱتَّخَذُواْ ٱلۡعِجۡلَ سَيَنَالُهُمۡ غَضَبࣱ مِّن رَّبِّهِمۡ وَذِلَّةࣱ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَاۚ وَكَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلۡمُفۡتَرِينَ

Ndithudi iwo amene adapembedza ng’ombe, mkwiyo wa Ambuye wawo ndi kupeputsidwa kudzadza kwa iwo m’moyo uno. Mmenemo ndi mmene timalipirira anthu opeka mabodza

Ayah 152

وَٱلَّذِينَ عَمِلُواْ ٱلسَّيِّـَٔاتِ ثُمَّ تَابُواْ مِنۢ بَعۡدِهَا وَءَامَنُوٓاْ إِنَّ رَبَّكَ مِنۢ بَعۡدِهَا لَغَفُورࣱ رَّحِيمࣱ‏

Koma iwo amene anachita zoipa ndipo pambuyo pake adalapa ndi kukhala ndi chikhulupiriro, ndithu Ambuye wako pambuyo pa izo ndi wokhululukira ndi wachisoni chosatha

Ayah 153

وَلَمَّا سَكَتَ عَن مُّوسَى ٱلۡغَضَبُ أَخَذَ ٱلۡأَلۡوَاحَۖ وَفِي نُسۡخَتِهَا هُدࣰ ى وَرَحۡمَةࣱ لِّلَّذِينَ هُمۡ لِرَبِّهِمۡ يَرۡهَبُونَ

Ndipo pamene mkwiyo wake udatha, Mose adatenga matabwa a malamulo, amene m’zolembedwa zake mudali chilangizo ndi chifundo kwa anthu amene amaopa Ambuye wawo

Ayah 154

وَٱخۡتَارَ مُوسَىٰ قَوۡمَهُۥ سَبۡعِينَ رَجُلࣰ ا لِّمِيقَٰتِنَاۖ فَلَمَّآ أَخَذَتۡهُمُ ٱلرَّجۡفَةُ قَالَ رَبِّ لَوۡ شِئۡتَ أَهۡلَكۡتَهُم مِّن قَبۡلُ وَإِيَّٰيَۖ أَتُهۡلِكُنَا بِمَا فَعَلَ ٱلسُّفَهَآءُ مِنَّآۖ إِنۡ هِيَ إِلَّا فِتۡنَتُكَ تُضِلُّ بِهَا مَن تَشَآءُ وَتَهۡدِي مَن تَشَآءُۖ أَنتَ وَلِيُّنَا فَٱغۡفِرۡ لَنَا وَٱرۡحَمۡنَاۖ وَأَنتَ خَيۡرُ ٱلۡغَٰفِرِينَ

Ndipo Mose adasankha, pakati pa anthu ake, amuna makumi asanu ndi awiri kuti adzakumane nafe ndipo pamene nthaka idagwedezeka pamapazi pawo, Mose adati: “Chikadakhala chifuniro chanu, Ambuye, mukadawaononga iwo ndi ine kale. Kodi inu mungationonge chifukwa cha ntchito za anthu amene ali pakati pathu? Awa ndi mayesero anu, amene Inu mumasocheretsa aliyense amene mwamufuna ndi kutsogolera yemwe mwamufuna. Inu nokha ndinu Mtetezi wathu ndipo tichitireni chisoni chifukwa Inu ndinu wopambana onse amene amakhululukira.”

Ayah 155

۞وَٱكۡتُبۡ لَنَا فِي هَٰذِهِ ٱلدُّنۡيَا حَسَنَةࣰ وَفِي ٱلۡأٓخِرَةِ إِنَّا هُدۡنَآ إِلَيۡكَۚ قَالَ عَذَابِيٓ أُصِيبُ بِهِۦ مَنۡ أَشَآءُۖ وَرَحۡمَتِي وَسِعَتۡ كُلَّ شَيۡءࣲۚ فَسَأَكۡتُبُهَا لِلَّذِينَ يَتَّقُونَ وَيُؤۡتُونَ ٱلزَّكَوٰةَ وَٱلَّذِينَ هُم بِـَٔايَٰتِنَا يُؤۡمِنُونَ

“Ndipo tipatseni ife zabwino m’moyo uno ndiponso m’moyo umene uli nkudza. Ndithudi ife tabwerera kwa Inu.” Mulungu adati: “Ine ndidzaonetsa chilango changa kwa aliyense amene ndimufuna ndipo chifundo changa chimakwanira zinthu zonse. Ine ndidzaonetsa chisoni kwa onse amene amalewa zoipa ndipo amapereka chaulere ndi iwo amene amakhulupirirazizindikirozathu.”

Ayah 156

ٱلَّذِينَ يَتَّبِعُونَ ٱلرَّسُولَ ٱلنَّبِيَّ ٱلۡأُمِّيَّ ٱلَّذِي يَجِدُونَهُۥ مَكۡتُوبًا عِندَهُمۡ فِي ٱلتَّوۡرَىٰةِ وَٱلۡإِنجِيلِ يَأۡمُرُهُم بِٱلۡمَعۡرُوفِ وَيَنۡهَىٰهُمۡ عَنِ ٱلۡمُنكَرِ وَيُحِلُّ لَهُمُ ٱلطَّيِّبَٰتِ وَيُحَرِّمُ عَلَيۡهِمُ ٱلۡخَبَٰٓئِثَ وَيَضَعُ عَنۡهُمۡ إِصۡرَهُمۡ وَٱلۡأَغۡلَٰلَ ٱلَّتِي كَانَتۡ عَلَيۡهِمۡۚ فَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ بِهِۦ وَعَزَّرُوهُ وَنَصَرُوهُ وَٱتَّبَعُواْ ٱلنُّورَ ٱلَّذِيٓ أُنزِلَ مَعَهُۥٓ أُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡمُفۡلِحُونَ

Iwoameneamatsatira Mtumwi kapena Mneneri amene sadziwa kulemba ndi kuwerenga, amene mbiri yake inalembedwa m’Buku la chipangano chakale ndi mu chipangano chatsopano. Iye amawalamulira kuchita zabwino ndipo amawaletsa kuchita zoipa. Ndipo amawaloleza zabwino ndi kuwaletsa zonyansa. Iye amawapeputsira katundu wolemera amene adali pa iwo. Motero iwo amene akhulupirira mwa iye ndi kumulemekeza, ndi kumuthandiza iye ndi kutsata kuunika kumene kwatumizidwa ndi iye, ndi okhawo amene adzakhala opambana

Ayah 157

قُلۡ يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ إِنِّي رَسُولُ ٱللَّهِ إِلَيۡكُمۡ جَمِيعًا ٱلَّذِي لَهُۥ مُلۡكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۖ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ يُحۡيِۦ وَيُمِيتُۖ فَـَٔامِنُواْ بِٱللَّهِ وَرَسُولِهِ ٱلنَّبِيِّ ٱلۡأُمِّيِّ ٱلَّذِي يُؤۡمِنُ بِٱللَّهِ وَكَلِمَٰتِهِۦ وَٱتَّبِعُوهُ لَعَلَّكُمۡ تَهۡتَدُونَ

Nena, “Oh inu anthu! Ndithudi ine ndatumizidwa ngati Mtumwi wa Mulungu kwa inu nonse, yemwe ali Mwini ufumu wakumwamba ndi wa padziko lapansi. Kulibe mulungu wina koma Iye yekha. Iye amapereka moyo ndi imfa. Motero khulupilirani mwa Mulungu ndi mwa Mtumwi wake, Mtumwi yemwe sadziwa kuwerenga ndi kulemba, amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi m’Mawu ake. Ndipo mutsatireni iye kuti mukhale otsogozedwa.”

Ayah 158

وَمِن قَوۡمِ مُوسَىٰٓ أُمَّةࣱ يَهۡدُونَ بِٱلۡحَقِّ وَبِهِۦ يَعۡدِلُونَ

Pakati pa anthu a Mose, pali anthu ena amene amatsogolera mwa choonadi ndipo anali kuchita chilungamo

Ayah 159

وَقَطَّعۡنَٰهُمُ ٱثۡنَتَيۡ عَشۡرَةَ أَسۡبَاطًا أُمَمࣰ اۚ وَأَوۡحَيۡنَآ إِلَىٰ مُوسَىٰٓ إِذِ ٱسۡتَسۡقَىٰهُ قَوۡمُهُۥٓ أَنِ ٱضۡرِب بِّعَصَاكَ ٱلۡحَجَرَۖ فَٱنۢبَجَسَتۡ مِنۡهُ ٱثۡنَتَا عَشۡرَةَ عَيۡنࣰ اۖ قَدۡ عَلِمَ كُلُّ أُنَاسࣲ مَّشۡرَبَهُمۡۚ وَظَلَّلۡنَا عَلَيۡهِمُ ٱلۡغَمَٰمَ وَأَنزَلۡنَا عَلَيۡهِمُ ٱلۡمَنَّ وَٱلسَّلۡوَىٰۖ كُلُواْ مِن طَيِّبَٰتِ مَا رَزَقۡنَٰكُمۡۚ وَمَا ظَلَمُونَا وَلَٰكِن كَانُوٓاْ أَنفُسَهُمۡ يَظۡلِمُونَ

Ndipo Ifetidawagawakukhalamafukokhumindiiwiri. Ndipo Ife tidamupatsa Mau Mose, ndipo tidati: “Menya thanthwe ndi ndodo yako.” Pomwepo a kasupe khumi ndi awiri anatumphuka kuchokera m’thanthwe ndipo gulu lililonse lidadziwa chitsime chake. Ife tidawavundikira ndi mitambo ndipo tidawatumizira Manna ndi mbalame ndipo tidati: “Idyani zinthu zabwino zimene takupatsani inu.” Iwo sadatilakwire Ife koma analakwira mizimu yawo

Ayah 160

وَإِذۡ قِيلَ لَهُمُ ٱسۡكُنُواْ هَٰذِهِ ٱلۡقَرۡيَةَ وَكُلُواْ مِنۡهَا حَيۡثُ شِئۡتُمۡ وَقُولُواْ حِطَّةࣱ وَٱدۡخُلُواْ ٱلۡبَابَ سُجَّدࣰ ا نَّغۡفِرۡ لَكُمۡ خَطِيٓـَٰٔتِكُمۡۚ سَنَزِيدُ ٱلۡمُحۡسِنِينَ

Ndi pamene zidanenedwa kwa iwo: “Khalani mu Mzinda uwu ndipo idyani mmene mungafunire ndipo munene kuti: ‘Tikhululukireni machimo athu; ndipo lowani pa khomo modzichepetsa.’ Ife tidzakukhululukirani machimo anu. Ndipo tidzaonjezera mphotho ya iwo amene achita zabwino.”

Ayah 161

فَبَدَّلَ ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ مِنۡهُمۡ قَوۡلًا غَيۡرَ ٱلَّذِي قِيلَ لَهُمۡ فَأَرۡسَلۡنَا عَلَيۡهِمۡ رِجۡزࣰ ا مِّنَ ٱلسَّمَآءِ بِمَا كَانُواْ يَظۡلِمُونَ

Koma anthu oipa amene adali pakati pawo, adasintha mawu amene adapatsidwa, motero Ife tidawatumizira chilango kuchokera kumwamba chifukwa cha kulakwa kwawo

Ayah 162

وَسۡـَٔلۡهُمۡ عَنِ ٱلۡقَرۡيَةِ ٱلَّتِي كَانَتۡ حَاضِرَةَ ٱلۡبَحۡرِ إِذۡ يَعۡدُونَ فِي ٱلسَّبۡتِ إِذۡ تَأۡتِيهِمۡ حِيتَانُهُمۡ يَوۡمَ سَبۡتِهِمۡ شُرَّعࣰ ا وَيَوۡمَ لَا يَسۡبِتُونَ لَا تَأۡتِيهِمۡۚ كَذَٰلِكَ نَبۡلُوهُم بِمَا كَانُواْ يَفۡسُقُونَ

Ndipo afunse iwo za Mzinda umene udali pa mbali pa nyanja pamene iwo adaphwanya malamulo a tsiku la Sabata pamene nsomba zinali kusewera pafupi ndi kumatulutsa mitu yawo pamene sizidali kutero pa masiku ena. Motero Ife tidawayesa chifukwa iwo adali anthu oswa malamulo

Ayah 163

وَإِذۡ قَالَتۡ أُمَّةࣱ مِّنۡهُمۡ لِمَ تَعِظُونَ قَوۡمًا ٱللَّهُ مُهۡلِكُهُمۡ أَوۡ مُعَذِّبُهُمۡ عَذَابࣰ ا شَدِيدࣰ اۖ قَالُواْ مَعۡذِرَةً إِلَىٰ رَبِّكُمۡ وَلَعَلَّهُمۡ يَتَّقُونَ

Ndi pamene gulu lina lidati, “Kodi ndi chifukwa chiyani uli kulalikira kwa anthu amene Mulungu ali pafupi kuwaononga kapena kuwalanga kwambiri?” Iwo adayankha kuti; “Ife tisadzakhale ndi mlandu kwa Ambuye wanu ndiponso kuti mwina iwo angaope Mulungu.”

Ayah 164

فَلَمَّا نَسُواْ مَا ذُكِّرُواْ بِهِۦٓ أَنجَيۡنَا ٱلَّذِينَ يَنۡهَوۡنَ عَنِ ٱلسُّوٓءِ وَأَخَذۡنَا ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ بِعَذَابِۭ بَـِٔيسِۭ بِمَا كَانُواْ يَفۡسُقُونَ

Ndipo pamaso pa iwo amene adaiwala chikumbutso chimene chidaperekedwa kwa iwo, Ife tidapulumutsa iwo amene amaletsa zoipa ndipo Ife tidawalanga amene adali olakwa ndi chilango chowawa chifukwa cha machimo awo

Ayah 165

فَلَمَّا عَتَوۡاْ عَن مَّا نُهُواْ عَنۡهُ قُلۡنَا لَهُمۡ كُونُواْ قِرَدَةً خَٰسِـِٔينَ

Ndipo pa nthawi imene iwo adapitiriza kuchita zinthu zimene adaletsedwa kuchita, Ife tidati kwa iwo! “Khalani anyani, onyozeka ndi okanidwa.”

Ayah 166

وَإِذۡ تَأَذَّنَ رَبُّكَ لَيَبۡعَثَنَّ عَلَيۡهِمۡ إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِ مَن يَسُومُهُمۡ سُوٓءَ ٱلۡعَذَابِۗ إِنَّ رَبَّكَ لَسَرِيعُ ٱلۡعِقَابِ وَإِنَّهُۥ لَغَفُورࣱ رَّحِيمࣱ‏

Ndi pamene Ambuye wako adalamula kuti adzawatumizira, mpaka tsiku la chiweruzo, iwo amene azibweretsa mazunzo ndi mnyozo pa iwo. Ndithudi Ambuye wako ndi wachangu polanga. Ndipo, ndithudi, Iye ndi wokhululukira ndipo ndi wachisoni chosatha

Ayah 167

وَقَطَّعۡنَٰهُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ أُمَمࣰ اۖ مِّنۡهُمُ ٱلصَّٰلِحُونَ وَمِنۡهُمۡ دُونَ ذَٰلِكَۖ وَبَلَوۡنَٰهُم بِٱلۡحَسَنَٰتِ وَٱلسَّيِّـَٔاتِ لَعَلَّهُمۡ يَرۡجِعُونَ

Ife tidawamwaza pa dziko lapansi m’magulu osiyanasiyana. Ena adali anthu angwiro pamene ena ndi anthu oipa. Ndipo Ife tidawayesa powapatsa madalitso ndi matsoka kuti mwina akhoza kubwerera

Ayah 168

فَخَلَفَ مِنۢ بَعۡدِهِمۡ خَلۡفࣱ وَرِثُواْ ٱلۡكِتَٰبَ يَأۡخُذُونَ عَرَضَ هَٰذَا ٱلۡأَدۡنَىٰ وَيَقُولُونَ سَيُغۡفَرُ لَنَا وَإِن يَأۡتِهِمۡ عَرَضࣱ مِّثۡلُهُۥ يَأۡخُذُوهُۚ أَلَمۡ يُؤۡخَذۡ عَلَيۡهِم مِّيثَٰقُ ٱلۡكِتَٰبِ أَن لَّا يَقُولُواْ عَلَى ٱللَّهِ إِلَّا ٱلۡحَقَّ وَدَرَسُواْ مَا فِيهِۗ وَٱلدَّارُ ٱلۡأٓخِرَةُ خَيۡرࣱ لِّلَّذِينَ يَتَّقُونَۚ أَفَلَا تَعۡقِلُونَ

Ndipo lidalowa m’malo gulu lina loipa limene linatenga Buku, koma iwo adasankha zinthu zopanda pake za pa dziko lapansi. Ndipo iwo adati “Tidzakhululukidwa.” Koma zitawapezanso zinthu zopanda pake za mtundu womwewo iwo akadazilandira. Kodi lonjezo la m’Buku silinalandiridwe kuchokera kwa iwo kuti sadzanena chili chonse chokhudza Mulungu kupatula choonadi? Ndipo iwo aphunzira zomwe zili m’menemo. Ndipo dziko limene lili nkudza ndi labwino kwa anthu oopa Mulungu. Kodi inu mulibe nzeru

Ayah 169

وَٱلَّذِينَ يُمَسِّكُونَ بِٱلۡكِتَٰبِ وَأَقَامُواْ ٱلصَّلَوٰةَ إِنَّا لَا نُضِيعُ أَجۡرَ ٱلۡمُصۡلِحِينَ

Akakhala iwo amene amatsatira moona Mau a Mulungu ndi kupitiriza mapemphero, ndithudi, Ife sitidzaononga mphotho za anthu ochita ntchito zabwino

Ayah 170

۞وَإِذۡ نَتَقۡنَا ٱلۡجَبَلَ فَوۡقَهُمۡ كَأَنَّهُۥ ظُلَّةࣱ وَظَنُّوٓاْ أَنَّهُۥ وَاقِعُۢ بِهِمۡ خُذُواْ مَآ ءَاتَيۡنَٰكُم بِقُوَّةࣲ وَٱذۡكُرُواْ مَا فِيهِ لَعَلَّكُمۡ تَتَّقُونَ

Ndi pamene tidakweza phiri ndikuliika pamwamba pawo kukhala ngati mthunzi ndipo iwo amaganiza kuti liwagwera. Ndipo Ife tidati, “Gwiritsani chimene takupatsani inu ndipo kumbukirani zimene zili m’kati mwake kuti mukhale oopa Mulungu ndi kumumvera Iye.”

Ayah 171

وَإِذۡ أَخَذَ رَبُّكَ مِنۢ بَنِيٓ ءَادَمَ مِن ظُهُورِهِمۡ ذُرِّيَّتَهُمۡ وَأَشۡهَدَهُمۡ عَلَىٰٓ أَنفُسِهِمۡ أَلَسۡتُ بِرَبِّكُمۡۖ قَالُواْ بَلَىٰ شَهِدۡنَآۚ أَن تَقُولُواْ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ إِنَّا كُنَّا عَنۡ هَٰذَا غَٰفِلِينَ

Ndi pamene Ambuye wako adabweretsa kuchokera kwa ana a Adamu, kuchokera m’misana mwawo mbeu yawo ndipo adawapanga kuti alumbire okha. Iye adati, “Kodi ine sindine Ambuye wanu?” Iwo adayankha: “Indedi! Ife tili kuchitira umboni.” Kuti mwina mungadzanene, pa tsiku louka kwa akufa kuti: “Ndithudi ife sitimadziwa china chilichonse cha izi.”

Ayah 172

أَوۡ تَقُولُوٓاْ إِنَّمَآ أَشۡرَكَ ءَابَآؤُنَا مِن قَبۡلُ وَكُنَّا ذُرِّيَّةࣰ مِّنۢ بَعۡدِهِمۡۖ أَفَتُهۡلِكُنَا بِمَا فَعَلَ ٱلۡمُبۡطِلُونَ

Kapena mwina mungadzanene kuti, “Ndi makolo athu akale amene amapembedza milungu ina pambali pa Mulungu. Ife tidali m’badwo wapambuyo pawo. Kodi inu mutiononga chifukwa cha zimene adachita anthu oipa?”

Ayah 173

وَكَذَٰلِكَ نُفَصِّلُ ٱلۡأٓيَٰتِ وَلَعَلَّهُمۡ يَرۡجِعُونَ

Motero Ife tili kulongosola chivumbulutso chathu kuti iwo abwerere

Ayah 174

وَٱتۡلُ عَلَيۡهِمۡ نَبَأَ ٱلَّذِيٓ ءَاتَيۡنَٰهُ ءَايَٰتِنَا فَٱنسَلَخَ مِنۡهَا فَأَتۡبَعَهُ ٱلشَّيۡطَٰنُ فَكَانَ مِنَ ٱلۡغَاوِينَ

Ndipo awerengere iwo za nkhani ya munthu amene Ife tidamupatsa zizindikiro zathu koma iye adazikana, ndipo Satana adamutsatira ndipo iye adali mmodzi wa anthu osochera

Ayah 175

وَلَوۡ شِئۡنَا لَرَفَعۡنَٰهُ بِهَا وَلَٰكِنَّهُۥٓ أَخۡلَدَ إِلَى ٱلۡأَرۡضِ وَٱتَّبَعَ هَوَىٰهُۚ فَمَثَلُهُۥ كَمَثَلِ ٱلۡكَلۡبِ إِن تَحۡمِلۡ عَلَيۡهِ يَلۡهَثۡ أَوۡ تَتۡرُكۡهُ يَلۡهَثۚ ذَّٰلِكَ مَثَلُ ٱلۡقَوۡمِ ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَاۚ فَٱقۡصُصِ ٱلۡقَصَصَ لَعَلَّهُمۡ يَتَفَكَّرُونَ

Ndipo tikadafuna Ife tikadamukweza iye, koma iye adaumirira moyo wa pa dziko lino lapansi ndi kutsatira zilakolako zake. Motero iye akhoza kufanizidwa ndi galu, amene ngati umupilikitsa, amatulutsa lilime lake, kaya umusiya yekha iye amalitulutsabe. Limenelo ndi fanizo la anthu amene amakana zizindikiro zathu. Motero auze nkhanizi kuti mwina iwo akhoza kuganiza bwino

Ayah 176

سَآءَ مَثَلًا ٱلۡقَوۡمُ ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا وَأَنفُسَهُمۡ كَانُواْ يَظۡلِمُونَ

Choipa ndicho chifanizo cha anthu amene amakana chivumbulutso chathu, ndipo iwo amachimwira mizimu yawo yomwe

Ayah 177

مَن يَهۡدِ ٱللَّهُ فَهُوَ ٱلۡمُهۡتَدِيۖ وَمَن يُضۡلِلۡ فَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡخَٰسِرُونَ

Aliyense amene Mulungu amamutsogolera, iye amatsogozedwa bwino ndipo aliyense amene Iye amusocheretsa, iye ndi olephera

Ayah 178

وَلَقَدۡ ذَرَأۡنَا لِجَهَنَّمَ كَثِيرࣰ ا مِّنَ ٱلۡجِنِّ وَٱلۡإِنسِۖ لَهُمۡ قُلُوبࣱ لَّا يَفۡقَهُونَ بِهَا وَلَهُمۡ أَعۡيُنࣱ لَّا يُبۡصِرُونَ بِهَا وَلَهُمۡ ءَاذَانࣱ لَّا يَسۡمَعُونَ بِهَآۚ أُوْلَٰٓئِكَ كَٱلۡأَنۡعَٰمِ بَلۡ هُمۡ أَضَلُّۚ أُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡغَٰفِلُونَ

Ndithudi, Ife tanalenga majini ndi anthu ambiri kuti akalowe ku Gahena. Iwo ali ndi mitima imene sangathe kuzindikira, ali ndi maso amene sangathe kuona, ali ndi makutu amene sangathe kumva ayi. Iwo ali ngati ng’ombe. Iyai! Iwo ndi osochera kwambiri. Amenewa! Ndi nkhutukumve

Ayah 179

وَلِلَّهِ ٱلۡأَسۡمَآءُ ٱلۡحُسۡنَىٰ فَٱدۡعُوهُ بِهَاۖ وَذَرُواْ ٱلَّذِينَ يُلۡحِدُونَ فِيٓ أَسۡمَٰٓئِهِۦۚ سَيُجۡزَوۡنَ مَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ

Mulungu ali ndi mayina abwino kwambiri. Motero muitaneni pa mayina amenewo ndipo asiyeni iwo amene amaononga ulemerero wa mayina ake. Iwo adzalangidwa chifukwa cha zimene adali kuchita

Ayah 180

وَمِمَّنۡ خَلَقۡنَآ أُمَّةࣱ يَهۡدُونَ بِٱلۡحَقِّ وَبِهِۦ يَعۡدِلُونَ

Ndipo pakati pa iwo amene tidawalenga, alipo anthu amene amalangiza choonadi ndipo amachita chilungamo

Ayah 181

وَٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا سَنَسۡتَدۡرِجُهُم مِّنۡ حَيۡثُ لَا يَعۡلَمُونَ

Iwo amene amakana chivumbulutso chathu, Ife tidzawagwira pang’onopang’ono ndi chilango chathu popanda iwo kuzindikira

Ayah 182

وَأُمۡلِي لَهُمۡۚ إِنَّ كَيۡدِي مَتِينٌ

Ndimawapatsa nthawi, ndithudi, chikonzero changa ndi chokhwima

Ayah 183

أَوَلَمۡ يَتَفَكَّرُواْۗ مَا بِصَاحِبِهِم مِّن جِنَّةٍۚ إِنۡ هُوَ إِلَّا نَذِيرࣱ مُّبِينٌ

Kodi iwo saganizira? Mulibe misala mwa m’bale wawo. Iye ndi mchenjezi basi

Ayah 184

أَوَلَمۡ يَنظُرُواْ فِي مَلَكُوتِ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا خَلَقَ ٱللَّهُ مِن شَيۡءࣲ وَأَنۡ عَسَىٰٓ أَن يَكُونَ قَدِ ٱقۡتَرَبَ أَجَلُهُمۡۖ فَبِأَيِّ حَدِيثِۭ بَعۡدَهُۥ يُؤۡمِنُونَ

Kodi iwo sayang’ana mu Ufumu wa kumwamba ndi wa dziko lapansi ndi zonse zimene Mulungu adazilenga kuti aone ngati ndi mapeto a moyo wawo? Kodi ndi uthenga uti pambuyo pa uwu umene iwo adzakhulupirire

Ayah 185

مَن يُضۡلِلِ ٱللَّهُ فَلَا هَادِيَ لَهُۥۚ وَيَذَرُهُمۡ فِي طُغۡيَٰنِهِمۡ يَعۡمَهُونَ

Aliyense amene Mulungu wamusocheza palibe wina amene angamutsogolere ndipo Iye amawasiya kuchita zinthu mwakhungu poswa malamulo

Ayah 186

يَسۡـَٔلُونَكَ عَنِ ٱلسَّاعَةِ أَيَّانَ مُرۡسَىٰهَاۖ قُلۡ إِنَّمَا عِلۡمُهَا عِندَ رَبِّيۖ لَا يُجَلِّيهَا لِوَقۡتِهَآ إِلَّا هُوَۚ ثَقُلَتۡ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ لَا تَأۡتِيكُمۡ إِلَّا بَغۡتَةࣰۗ يَسۡـَٔلُونَكَ كَأَنَّكَ حَفِيٌّ عَنۡهَاۖ قُلۡ إِنَّمَا عِلۡمُهَا عِندَ ٱللَّهِ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَ ٱلنَّاسِ لَا يَعۡلَمُونَ

Iwo amakufunsa iwe za ola lomaliza kuti lidzadza liti? Nena, “Amene adziwa za tsikuli ndi Ambuye wanga. Palibe amene adzaulule nthawi yake kupatula Iye yekha.” Lidzalemetsa kumwamba ndi dziko lapansi. Ilo silidzadza kwa inu kupatula mwadzidzidzi. Iwo alikufunsa ngati iwe umadziwa zambiri za olali. Nena, “Kuzindikira za tsikuli kuli kwa Mulungu yekha koma anthu ambiri sadziwa.”

Ayah 187

قُل لَّآ أَمۡلِكُ لِنَفۡسِي نَفۡعࣰ ا وَلَا ضَرًّا إِلَّا مَا شَآءَ ٱللَّهُۚ وَلَوۡ كُنتُ أَعۡلَمُ ٱلۡغَيۡبَ لَٱسۡتَكۡثَرۡتُ مِنَ ٱلۡخَيۡرِ وَمَا مَسَّنِيَ ٱلسُّوٓءُۚ إِنۡ أَنَا۠ إِلَّا نَذِيرࣱ وَبَشِيرࣱ لِّقَوۡمࣲ يُؤۡمِنُونَ

Nena, “Ine ndilibe mphamvu yopeza zinthu, kapena kupewa mavuto kupatula ndi chifuniro cha Mulungu. Ine ndikadakhala wodziwa chilichonse chobisika ndikadadzichulukitsira chuma ndipo palibe choipa chimene chikadandipeza. Ine sindine wina aliyense ayi koma wopereka chenjezo ndi wobweretsa nkhani yabwino kwa anthu okhulupirira.”

Ayah 188

۞هُوَ ٱلَّذِي خَلَقَكُم مِّن نَّفۡسࣲ وَٰحِدَةࣲ وَجَعَلَ مِنۡهَا زَوۡجَهَا لِيَسۡكُنَ إِلَيۡهَاۖ فَلَمَّا تَغَشَّىٰهَا حَمَلَتۡ حَمۡلًا خَفِيفࣰ ا فَمَرَّتۡ بِهِۦۖ فَلَمَّآ أَثۡقَلَت دَّعَوَا ٱللَّهَ رَبَّهُمَا لَئِنۡ ءَاتَيۡتَنَا صَٰلِحࣰ ا لَّنَكُونَنَّ مِنَ ٱلشَّٰكِرِينَ

Iye ndiye amene adakulengani inu kuchokera kwa munthu mmodzi ndipo kuchokera kwa munthu ameneyu adamulengera mkazi wake, kuti akhoza kupeza chisangalalo pokhala naye. Ndipo pamene iye amagona naye, iye adatenga pakati pamene ananyamula mosavutika. Koma pamene panakula, onse awiri amapempha Ambuye wawo: “Ngati Inu mutatipatsa mwana wabwino ndithudi ife tidzakhala othokoza.”

Ayah 189

فَلَمَّآ ءَاتَىٰهُمَا صَٰلِحࣰ ا جَعَلَا لَهُۥ شُرَكَآءَ فِيمَآ ءَاتَىٰهُمَاۚ فَتَعَٰلَى ٱللَّهُ عَمَّا يُشۡرِكُونَ

Koma pamene akawapatsa mwana wabwino, iwo amakhazikitsa milungu ina pambali pa Iye kuthokoza pa zimene wawapatsa. Alemekezeke Mulungu kuposa zimene akumphatikiza nazo

Ayah 190

أَيُشۡرِكُونَ مَا لَا يَخۡلُقُ شَيۡـࣰٔ ا وَهُمۡ يُخۡلَقُونَ

Kodi iwo akukhazikitsa milungu ina pambali pa Mulungu weni weni imene siingathe kulenga zina zilizonse koma kuti nayonso ndi yolengedwa

Ayah 191

وَلَا يَسۡتَطِيعُونَ لَهُمۡ نَصۡرࣰ ا وَلَآ أَنفُسَهُمۡ يَنصُرُونَ

Palibe chimene ingawathandize ayi ndiponso iyo siingathe kudzithandiza yokha

Ayah 192

وَإِن تَدۡعُوهُمۡ إِلَى ٱلۡهُدَىٰ لَا يَتَّبِعُوكُمۡۚ سَوَآءٌ عَلَيۡكُمۡ أَدَعَوۡتُمُوهُمۡ أَمۡ أَنتُمۡ صَٰمِتُونَ

Ndipo ngati iwe uwaitana kunjira yoyenera iwo sadzakutsatira ayi. Ndi chimodzimodzi kwa iwe kaya uwaitana kapena ukhala chete

Ayah 193

إِنَّ ٱلَّذِينَ تَدۡعُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ عِبَادٌ أَمۡثَالُكُمۡۖ فَٱدۡعُوهُمۡ فَلۡيَسۡتَجِيبُواْ لَكُمۡ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ

Ndithudi iwo amene mumawapembedza powonjezera pa Mulungu weniweni ndi akapolo ngati inu nomwe. Motero aitaneni ndipo akuyankheni ngati zimene munena ndi zoonadi

Ayah 194

أَلَهُمۡ أَرۡجُلࣱ يَمۡشُونَ بِهَآۖ أَمۡ لَهُمۡ أَيۡدࣲ يَبۡطِشُونَ بِهَآۖ أَمۡ لَهُمۡ أَعۡيُنࣱ يُبۡصِرُونَ بِهَآۖ أَمۡ لَهُمۡ ءَاذَانࣱ يَسۡمَعُونَ بِهَاۗ قُلِ ٱدۡعُواْ شُرَكَآءَكُمۡ ثُمَّ كِيدُونِ فَلَا تُنظِرُونِ

Kodi iwo ali ndi miyendo yoti angayendere? Kodi ali ndi manja oti angagwire china chilichonse? Kapena ali ndi maso oti angaonere? Kapena ali ndi makutu oti angamvere? Nena, “Itanani milungu yanu yabodza ndipo pangani chiwembu chanu pa ine ndipo musandipatse mpumulo ayi.”

Ayah 195

إِنَّ وَلِـِّۧيَ ٱللَّهُ ٱلَّذِي نَزَّلَ ٱلۡكِتَٰبَۖ وَهُوَ يَتَوَلَّى ٱلصَّٰلِحِينَ

Ndithudi Mtetezi wanga ndi Mulungu amene wavumbulutsa Buku ndipo Iye ndi Mtetezi wa anthu a chilungamo

Ayah 196

وَٱلَّذِينَ تَدۡعُونَ مِن دُونِهِۦ لَا يَسۡتَطِيعُونَ نَصۡرَكُمۡ وَلَآ أَنفُسَهُمۡ يَنصُرُونَ

Ndipo iwo amene mumawapembedza powonjezera pa Iye sangathe kukuthandizani inu ndiponso sangathe kudzithandiza iwo eni

Ayah 197

وَإِن تَدۡعُوهُمۡ إِلَى ٱلۡهُدَىٰ لَا يَسۡمَعُواْۖ وَتَرَىٰهُمۡ يَنظُرُونَ إِلَيۡكَ وَهُمۡ لَا يُبۡصِرُونَ

Ndipo ngati iwe uwaitanira ku njira yoyenera, sakumva ayi ndipo udzawaona ali kukuyang’ana iwe koma sakuona ai

Ayah 198

خُذِ ٱلۡعَفۡوَ وَأۡمُرۡ بِٱلۡعُرۡفِ وَأَعۡرِضۡ عَنِ ٱلۡجَٰهِلِينَ

Onetsa kukhululukira, lamulira zabwino ndipo uwapewe anthu osadziwa

Ayah 199

وَإِمَّا يَنزَغَنَّكَ مِنَ ٱلشَّيۡطَٰنِ نَزۡغࣱ فَٱسۡتَعِذۡ بِٱللَّهِۚ إِنَّهُۥ سَمِيعٌ عَلِيمٌ

Ndipo ngati Satana akuyesa iwe, thawira kwa Mulungu. Ndithudi Iye ndi wakumva ndi wodziwa

Ayah 200

إِنَّ ٱلَّذِينَ ٱتَّقَوۡاْ إِذَا مَسَّهُمۡ طَٰٓئِفࣱ مِّنَ ٱلشَّيۡطَٰنِ تَذَكَّرُواْ فَإِذَا هُم مُّبۡصِرُونَ

Ndithudi iwo amene amaopa Mulungu, ngati maganizo oipa adza kwa iwo kuchokera kwa Satana, iwo amakumbukira ndipo amaona kuunika

Ayah 201

وَإِخۡوَٰنُهُمۡ يَمُدُّونَهُمۡ فِي ٱلۡغَيِّ ثُمَّ لَا يُقۡصِرُونَ

Koma abale awo, iwo amawalowetsa mu uchimo ndipo salekerera

Ayah 202

وَإِذَا لَمۡ تَأۡتِهِم بِـَٔايَةࣲ قَالُواْ لَوۡلَا ٱجۡتَبَيۡتَهَاۚ قُلۡ إِنَّمَآ أَتَّبِعُ مَا يُوحَىٰٓ إِلَيَّ مِن رَّبِّيۚ هَٰذَا بَصَآئِرُ مِن رَّبِّكُمۡ وَهُدࣰ ى وَرَحۡمَةࣱ لِّقَوۡمࣲ يُؤۡمِنُونَ

Ndipo ngati iwe siubweretsa chozizwitsa iwo amati, “Kodi ndi chifukwa chiani siunabweretse?” Nena, “Ine ndimatsatira chokhacho chimene chavumbulutsidwa kwa ine kuchokera kwa Ambuye wanga.” Uwu ndi umboni wochokera kwa Ambuye wanu, malangizo ndi madalitso kwa anthu okhulupirira

Ayah 203

وَإِذَا قُرِئَ ٱلۡقُرۡءَانُ فَٱسۡتَمِعُواْ لَهُۥ وَأَنصِتُواْ لَعَلَّكُمۡ تُرۡحَمُونَ

Ndipo pamene Korani ilakatulidwa, mverani ndipo khalani chete kuti mulandire madalitso

Ayah 204

وَٱذۡكُر رَّبَّكَ فِي نَفۡسِكَ تَضَرُّعࣰ ا وَخِيفَةࣰ وَدُونَ ٱلۡجَهۡرِ مِنَ ٱلۡقَوۡلِ بِٱلۡغُدُوِّ وَٱلۡأٓصَالِ وَلَا تَكُن مِّنَ ٱلۡغَٰفِلِينَ

Ndipo kumbukira Ambuye wako ndi lilime lako, mwa iwe wekha, modzichepetsa ndi mwamantha ndiponso mosakweza mawu m’mawa ndi masana ndipo usakhale ngati iwo a unyizi

Ayah 205

إِنَّ ٱلَّذِينَ عِندَ رَبِّكَ لَا يَسۡتَكۡبِرُونَ عَنۡ عِبَادَتِهِۦ وَيُسَبِّحُونَهُۥ وَلَهُۥ يَسۡجُدُونَۤ۩

Ndithudi iwo amene ali ndi Ambuye wako sanyada pogwira ntchito yopembedza Mulungu koma amamulemekeza Iye ndipo amagunditsa phumi zawo pamaso pake

Ayah 206