Surah Al-Mumtahana — She that is to be examined
Surah Al-Mumtahana (She that is to be examined) is chapter 60 of the Quran, with 13 verses. This page presents the Arabic text with a Chichewa translation, verse by verse.
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَا تَتَّخِذُواْ عَدُوِّي وَعَدُوَّكُمۡ أَوۡلِيَآءَ تُلۡقُونَ إِلَيۡهِم بِٱلۡمَوَدَّةِ وَقَدۡ كَفَرُواْ بِمَا جَآءَكُم مِّنَ ٱلۡحَقِّ يُخۡرِجُونَ ٱلرَّسُولَ وَإِيَّاكُمۡ أَن تُؤۡمِنُواْ بِٱللَّهِ رَبِّكُمۡ إِن كُنتُمۡ خَرَجۡتُمۡ جِهَٰدࣰ ا فِي سَبِيلِي وَٱبۡتِغَآءَ مَرۡضَاتِيۚ تُسِرُّونَ إِلَيۡهِم بِٱلۡمَوَدَّةِ وَأَنَا۠ أَعۡلَمُ بِمَآ أَخۡفَيۡتُمۡ وَمَآ أَعۡلَنتُمۡۚ وَمَن يَفۡعَلۡهُ مِنكُمۡ فَقَدۡ ضَلَّ سَوَآءَ ٱلسَّبِيلِ
oh inu anthu amene mwakhulupirira! Musasandutse adani anga ndi adani anu kukhala abwenzi anu powaonetsa chikondi chanu pamene iwo akana choonadi chimene chadza kwa inu ndipo amupirikitsa Mtumwi pamodzi ndi inu nomwe kuchokera ku nyumba zanu, chifukwa chakuti inu mumakhulupirira mwa Mulungu Ambuye wanu. Ngati inu mwadza ndi cholinga chogwira ntchito m’njira yanga ndi kufunafuna chisangalalo changa(musachite nawo ubwenzi). Ndipo ngati inu mumaonetsa chikondi kwa iwo mwamseri, ndithudi, mukatero mwasochera. Ine ndimadziwa zonse zimene mumachita mseri
Ayah 1إِن يَثۡقَفُوكُمۡ يَكُونُواْ لَكُمۡ أَعۡدَآءࣰ وَيَبۡسُطُوٓاْ إِلَيۡكُمۡ أَيۡدِيَهُمۡ وَأَلۡسِنَتَهُم بِٱلسُّوٓءِ وَوَدُّواْ لَوۡ تَكۡفُرُونَ
Ngati iwo akupambanani, ndithudi, adzakuonetsani kuti ndi adani anu ndipo adzagwiritsa ntchito manja awo ndi malirime awo pa inu pokuchitirani zoipa. Iwo afunitsitsa kuti nanu mukhale anthu osakhulupirira
Ayah 2لَن تَنفَعَكُمۡ أَرۡحَامُكُمۡ وَلَآ أَوۡلَٰدُكُمۡۚ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ يَفۡصِلُ بَيۡنَكُمۡۚ وَٱللَّهُ بِمَا تَعۡمَلُونَ بَصِيرࣱ
Abale anu kapena ana anu sadzakhala a phindu kwa inu patsiku la chiweruzo. Iye adzaweruza pakati panu chifukwa Mulungu amaona zonse zimene mumachita
Ayah 3قَدۡ كَانَتۡ لَكُمۡ أُسۡوَةٌ حَسَنَةࣱ فِيٓ إِبۡرَٰهِيمَ وَٱلَّذِينَ مَعَهُۥٓ إِذۡ قَالُواْ لِقَوۡمِهِمۡ إِنَّا بُرَءَٰٓؤُاْ مِنكُمۡ وَمِمَّا تَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ كَفَرۡنَا بِكُمۡ وَبَدَا بَيۡنَنَا وَبَيۡنَكُمُ ٱلۡعَدَٰوَةُ وَٱلۡبَغۡضَآءُ أَبَدًا حَتَّىٰ تُؤۡمِنُواْ بِٱللَّهِ وَحۡدَهُۥٓ إِلَّا قَوۡلَ إِبۡرَٰهِيمَ لِأَبِيهِ لَأَسۡتَغۡفِرَنَّ لَكَ وَمَآ أَمۡلِكُ لَكَ مِنَ ٱللَّهِ مِن شَيۡءࣲۖ رَّبَّنَا عَلَيۡكَ تَوَكَّلۡنَا وَإِلَيۡكَ أَنَبۡنَا وَإِلَيۡكَ ٱلۡمَصِيرُ
Muli chitsanzo chabwino kwa inu mwa Abrahamu ndi mwa iwo amene adali naye pamene iwo ananena kwa anthu awo kuti: “Ife sitili m’gulu lanu ndipo sitipembedza zimene inu mumapembedza pozifanizira ndi Mulungu. Ife takukanani ndipo pabuka pakati pa ife ndi inu udani ndi chidani chosatha kupatula ngati inu mukhulupirira mwa Mulungu ndi mwa Iye yekha.” Kupatula zonena za Abrahamu kwa Abambo ake kuti: “Ine ndidzapempha chikhululukiro chanu chifukwa ine ndilibe mphamvu pa chilichonse cha inu kuchokera kwa Mulungu. Ambuye wathu, mwa Inu ife takhulupirira ndi kwa Inu ndiko timapempha chikhululukiro, ndipo kwa Inu ndiko kumene tonse tidzabwerera pomaliza.”
Ayah 4رَبَّنَا لَا تَجۡعَلۡنَا فِتۡنَةࣰ لِّلَّذِينَ كَفَرُواْ وَٱغۡفِرۡ لَنَا رَبَّنَآۖ إِنَّكَ أَنتَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ
“Ambuye wathu, musatisandutse ife kukhala mayesero a anthu osakhulupirira koma tikhululukireni Ambuye wathu. Ndithudi Inu ndinu Mwini mphamvu zonse ndi Mwini nzeru zonse.”
Ayah 5لَقَدۡ كَانَ لَكُمۡ فِيهِمۡ أُسۡوَةٌ حَسَنَةࣱ لِّمَن كَانَ يَرۡجُواْ ٱللَّهَ وَٱلۡيَوۡمَ ٱلۡأٓخِرَۚ وَمَن يَتَوَلَّ فَإِنَّ ٱللَّهَ هُوَ ٱلۡغَنِيُّ ٱلۡحَمِيدُ
Ndithudi, mwa iwo mudali chitsanzo chabwino kwa inu kuti mutsatire, makamaka iwo amene amaika chikhulupiriro chawo mwa Mulungu ndi m’tsiku la chiweruzo. Ndithudi Mulungu ndi wolemera ndipo ndiye yekha amene ayenera kulemekezedwa
Ayah 6۞عَسَى ٱللَّهُ أَن يَجۡعَلَ بَيۡنَكُمۡ وَبَيۡنَ ٱلَّذِينَ عَادَيۡتُم مِّنۡهُم مَّوَدَّةࣰۚ وَٱللَّهُ قَدِيرࣱۚ وَٱللَّهُ غَفُورࣱ رَّحِيمࣱ
Mwina Mulungu angakhazikitse chikondi pakati pa inu ndi iwo amene inu mumawaganizira kuti ndi adani anu. Ndithudi Mulungu ali ndi mphamvu pa china chilichonse ndipo Mulungu ndi wokhululukira ndi Mwini chisoni chosatha
Ayah 7لَّا يَنۡهَىٰكُمُ ٱللَّهُ عَنِ ٱلَّذِينَ لَمۡ يُقَٰتِلُوكُمۡ فِي ٱلدِّينِ وَلَمۡ يُخۡرِجُوكُم مِّن دِيَٰرِكُمۡ أَن تَبَرُّوهُمۡ وَتُقۡسِطُوٓاْ إِلَيۡهِمۡۚ إِنَّ ٱللَّهَ يُحِبُّ ٱلۡمُقۡسِطِينَ
Mulungu sali kukuletsani kuti muonetse chilungamo ndi chisoni kwa iwo amene sadamenyane nanu chifukwa cha chikhulupiliro chanu ndipo sanakuthamangitseni mu nyumba zanu. Ndithudi, Mulungu amakonda iwo amene amachita zolungama
Ayah 8إِنَّمَا يَنۡهَىٰكُمُ ٱللَّهُ عَنِ ٱلَّذِينَ قَٰتَلُوكُمۡ فِي ٱلدِّينِ وَأَخۡرَجُوكُم مِّن دِيَٰرِكُمۡ وَظَٰهَرُواْ عَلَىٰٓ إِخۡرَاجِكُمۡ أَن تَوَلَّوۡهُمۡۚ وَمَن يَتَوَلَّهُمۡ فَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلظَّٰلِمُونَ
Mulungu wakuletsani kuchita ubwenzi ndi anthu amene munamenyana nawo chifukwa cha chikhulupiriro ndipo anakuthamangitsani ku nyumba zanu kapena adathandiza anthu ena kuti amenyane ndi kukupirikitsani inu. Ndipo aliyense amene achita ubwenzi ndi anthu otere ndi ochimwa
Ayah 9يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ إِذَا جَآءَكُمُ ٱلۡمُؤۡمِنَٰتُ مُهَٰجِرَٰتࣲ فَٱمۡتَحِنُوهُنَّۖ ٱللَّهُ أَعۡلَمُ بِإِيمَٰنِهِنَّۖ فَإِنۡ عَلِمۡتُمُوهُنَّ مُؤۡمِنَٰتࣲ فَلَا تَرۡجِعُوهُنَّ إِلَى ٱلۡكُفَّارِۖ لَا هُنَّ حِلࣱّ لَّهُمۡ وَلَا هُمۡ يَحِلُّونَ لَهُنَّۖ وَءَاتُوهُم مَّآ أَنفَقُواْۚ وَلَا جُنَاحَ عَلَيۡكُمۡ أَن تَنكِحُوهُنَّ إِذَآ ءَاتَيۡتُمُوهُنَّ أُجُورَهُنَّۚ وَلَا تُمۡسِكُواْ بِعِصَمِ ٱلۡكَوَافِرِ وَسۡـَٔلُواْ مَآ أَنفَقۡتُمۡ وَلۡيَسۡـَٔلُواْ مَآ أَنفَقُواْۚ ذَٰلِكُمۡ حُكۡمُ ٱللَّهِ يَحۡكُمُ بَيۡنَكُمۡۖ وَٱللَّهُ عَلِيمٌ حَكِيمࣱ
Oh inu anthu okhulupirira! Pamene akazi okhulupirira adza kwa inu ngati othawa mavuto, afufuzeni bwinobwino. Mulungu yekha ndiye amene adziwa bwino bwino chikhulupiriro chawo. Ngati inu mukhutitsidwa kuti ndi okhulupirira m’choonadi, musawabwezere kwa anthu osakhulupirira chifukwa iwo saloledwa kukwatiwa ndi anthu osakhulupirira monga momwe amuna osakhulupirira saloledwa kukwatira akazi okhulupirira. Koma abwezereni anthu osakhulupirira ziwongo zimene apereka. Ndipo sikulakwa ngati inu muwakwatira akazi okhulupirirawa ngati mwapereka chiwongo. Musapitilize ukwati wanu ndi akazi wosakhulupirira. Itanitsani zimene mwaononga ngati chiwongo cha ukwati ndipo aloleni osakhulupirira kuti nawonso aitanitse zimene aononga pa akazi okhulupirira amene adza kwa inu. Ili ndi lamulo la Mulungu. Iye amaweruza mwachilungamo pakati panu. Mulungu ndi wa nzeru ndi luntha
Ayah 10وَإِن فَاتَكُمۡ شَيۡءࣱ مِّنۡ أَزۡوَٰجِكُمۡ إِلَى ٱلۡكُفَّارِ فَعَاقَبۡتُمۡ فَـَٔاتُواْ ٱلَّذِينَ ذَهَبَتۡ أَزۡوَٰجُهُم مِّثۡلَ مَآ أَنفَقُواْۚ وَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ ٱلَّذِيٓ أَنتُم بِهِۦ مُؤۡمِنُونَ
Ndipo ngati ena, mwa akazi anu, athawa ndi kukakwatiwa ndi osakhulupirira, ndipo inu mupeza mwayi wolandira akazi wochokera kwa anthu osakhulupirira abwezereni chiwongo ndi china chilichonse chimene iwo adapereka anthu amene akazi awo awathawa. Ndipo opani Mulungu amene inu mumamukhulupirira
Ayah 11يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّبِيُّ إِذَا جَآءَكَ ٱلۡمُؤۡمِنَٰتُ يُبَايِعۡنَكَ عَلَىٰٓ أَن لَّا يُشۡرِكۡنَ بِٱللَّهِ شَيۡـࣰٔ ا وَلَا يَسۡرِقۡنَ وَلَا يَزۡنِينَ وَلَا يَقۡتُلۡنَ أَوۡلَٰدَهُنَّ وَلَا يَأۡتِينَ بِبُهۡتَٰنࣲ يَفۡتَرِينَهُۥ بَيۡنَ أَيۡدِيهِنَّ وَأَرۡجُلِهِنَّ وَلَا يَعۡصِينَكَ فِي مَعۡرُوفࣲ فَبَايِعۡهُنَّ وَٱسۡتَغۡفِرۡ لَهُنَّ ٱللَّهَۚ إِنَّ ٱللَّهَ غَفُورࣱ رَّحِيمࣱ
Oh iwe Mtumwi! Ngati akazi okhulupirira adza kwa iwe kudzalumbira lonjezo lakuti sadzamufanizira Mulungu ndi wina wake akamapembedza, kuti sadzaba, sadzachita chigololo, sadzapha ana awo, sadzalankhula mawu ojeda, sadzapeka nkhani zabodza ndipo kuti adzakumvera iwe pa nkhani ina iliyonse, iwe uyenera kulandira lonjezo lawo ndipo pempha kwa Mulungu kuti awakhululukire machimo awo chifukwa Mulungu ndi wokhululukira ndi Mwini chisoni chosatha
Ayah 12يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَا تَتَوَلَّوۡاْ قَوۡمًا غَضِبَ ٱللَّهُ عَلَيۡهِمۡ قَدۡ يَئِسُواْ مِنَ ٱلۡأٓخِرَةِ كَمَا يَئِسَ ٱلۡكُفَّارُ مِنۡ أَصۡحَٰبِ ٱلۡقُبُورِ
Oh inu okhulupirira! Musapalane ubwenzi ndi anthu amene adalandira mkwiyo wa Mulungu. Ndithudi iwo ali ndi mantha ndi zimene zidzawachitikira m’moyo umene uli nkudza monga momwe anthu osakhulupirira amachitira mantha ndi iwo amene adaikidwa m’manda
Ayah 13